Livro da vida
O Livro da Vida é o registro celestial dos nomes daqueles que pertencem a Deus. Estar escrito no Livro da Vida é a garantia da salvação eterna e da entrada na Nova Jerusalém.
Registrados no céu
Alegrai-vos por terem vossos nomes escritos nos céus. O Livro da Vida pertence ao Cordeiro de Deus desde a fundação do mundo.
Komabe musakondwere chifukwa mizimu yoyipa inakugonjerani, koma kondwerani chifukwa mayina anu analembedwa kumwamba."
Inde, ndikupempha iwe mnzanga pa ntchitoyi, thandiza amayiwa amene ndagwira nawo ntchito ya Uthenga Wabwino pamodzi ndi Klementonso ndi ena onse antchito anzanga amene mayina awo ali mʼbuku lamoyo.
Anthu onse okhala pa dziko lapansi adzapembedza chirombocho, aliyense amene chilengedwere cha dziko lapansi dzina lake silinalembedwe mʼbuku la amoyo la Mwana Wankhosa anaphedwa uja.
Chirombo chimene wachionachi chinalipo kale koma tsopano kulibe ndipo chidzatuluka ku chidzenje chakuya ndi kupita kukawonongedwa. Anthu okhala pa dziko lapansi amene mayina awo sanalembedwe mʼbuku lamoyo kuyambira pa kulengedwa kwa dziko lapansi adzadabwa pamene adzaona chirombocho, chifukwa chinalipo kale, tsopano kulibe, komabe chidzabwera.
O juízo final
No dia do julgamento, os livros serão abertos. Quem não for encontrado no Livro da Vida será lançado no lago de fogo.
Chiweruzo Chotsiriza
Kenaka ndinaona Mpando Waufumu waukulu woyera ndi Iye amene anakhalapo. Dziko lapansi ndi kumwamba zinathawa pamaso pake ndipo panalibenso malo awo. Ndipo ndinaona akufa, aakulu ndi aangʼono omwe atayimirira patsogolo pa Mpando Waufumu ndipo mabuku anatsekulidwa. Buku lina linatsekulidwa limene linali Buku Lamoyo. Akufa anaweruzidwa monga mwa zimene anachita monga mmene zinalembedwera mʼmabuku. Nyanja inapereka amene anaferamo ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufa ake ndipo munthu aliyense anaweruzidwa monga mwa ntchito zake. Kenaka imfa ndi Hade zinaponyedwa mʼnyanja ya moto. Nyanja yamoto ndiyo imfa yachiwiri. Ngati dzina la wina aliyense silinapezeke mʼBuku Lamoyo, anaponyedwa mʼnyanja yamoto.
Kanthu kosayeretsedwa sikadzalowamo, kuphatikizanso aliyense wochita zinthu zochititsa manyazi ndi zachinyengo, koma okhawo amene mayina awo alembedwa mʼbuku lamoyo la Mwana Wankhosa.
Nthawi Yotsiriza
"Pa nthawi imeneyo Mikayeli, mngelo wamkulu amene amateteza anthu a mtundu wako, adzabwera. Imeneyi idzakhala nthawi ya mavuto aakulu omwe sanaonekepo kuyambira pachiyambi cha mitundu ya anthu mpaka nthawi ikudzayo. Komatu pa nthawiyi anthu a mtundu wako, aliyense amene dzina lake lidzapezeke lolembedwa mʼbuku adzapulumutsidwa. Ambiri mwa amene akugona mʼnthaka adzadzuka: ena adzapita ku moyo wosatha, ena ku malo amanyazi ndi chilango chosatha.
Amene adzapambane adzavala zoyera ngati ena aja. Sindidzafafaniza dzina lake mʼbuku lamoyo, koma ndidzamuchitira umboni pamaso pa Atate anga ndi angelo ake.
O registro divino
Deus registra cada vida, cada lágrima e cada momento. Nada passa despercebido diante daquele que tudo vê e tudo guarda.
Maso anu anaona thupi langa lisanawumbidwe.
Masiku onse amene anapatsidwa kwa ine, analembedwa mʼbuku lanu
asanayambe nʼkuwerengedwa komwe.
Mulembe za kulira kwanga,
mulembe chiwerengero cha misozi yanga mʼbuku lanu.
Kodi zimenezi sizinalembedwe mʼbuku lanulo?
Pakuti iwo amazunza amene inu munamuvulaza
ndi kuyankhula zowawa kwa amene munawapweteka.
Awonjezereni kulakwa pa kulakwa kwawo,
musalole kuti akhale ndi gawo pa chipulumutso chanu.
Iwo afufutidwe mʼbuku la amoyo
ndipo asalembedwe pamodzi ndi olungama.
Ndipo woopa Yehova anayamba kukambirana, ndipo Yehova anamvetsera. Buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, lonena za amene amaopa Yehova ndi kulemekeza dzina lake.
Koma tsopano, chonde akhululukireni tchimo lawo. Ngati simutero, ndiye mundifute ine mʼbuku limene mwalemba."
Yehova anamuyankha Mose kuti, "Ndidzafuta mʼbuku aliyense amene wandichimwira.
Este artigo te tocou? Faça uma oração!
+581 estão orando agora.
Junte-se à corrente de oração.