Pular para o conteúdo
Publicidade

Maria

Por Bíblia Online

Maria, mãe de Jesus, é honrada nas Escrituras como a mulher escolhida por Deus para trazer ao mundo o Salvador. Sua fé, humildade e obediência são exemplo para todos os cristãos.

A escolhida de Deus

O anjo Gabriel anunciou a Maria que ela seria mãe do Filho do Altíssimo. Ela respondeu com fé: 'Faça-se em mim segundo a tua palavra.'

Aneneratu za Kubadwa kwa Yesu

Mwezi wachisanu ndi chimodzi, Mulungu anatuma mngelo Gabrieli ku Nazareti, mudzi wa ku Galileya, kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi Yosefe, wa fuko la Davide. Dzina la namwaliyo linali Mariya. Mngeloyo anafika kwa iye nati, "Moni, inu amene Ambuye wakukomerani mtima kwambiri! Ambuye ali ndi inu."

Koma mngeloyo anati kwa iye, "Usachite mantha Mariya, pakuti wapeza chisomo pamaso Mulungu. Udzakhala woyembekezera ndipo udzabala mwana wamwamuna ndipo udzamupatse dzina loti Yesu. Iye adzakhala wamkulu ndipo adzatchedwa Mwana wa Wammwambamwamba. Ambuye Mulungu adzamupatsa Iye mpando waufumu wa abambo ake Davide, ndipo adzalamulira pa nyumba ya Yakobo ku nthawi zonse; ufumu wake sudzatha."

Kubadwa kwa Yesu Khristu

Kubadwa kwa Yesu Khristu kunali motere: Amayi ake, Mariya, anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanagone malo amodzi, anapezeka ali woyembekezera mwana mwa mphamvu ya Mzimu Woyera.

O Magnificat

Maria cantou: 'Minha alma engrandece ao Senhor!' Seu cântico exalta a misericórdia, o poder e a fidelidade de Deus.

Nyimbo ya Mariya

Ndipo Mariya anati:

"Moyo wanga ulemekeza Ambuye.

Ndipo mzimu wanga ukondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga,

pakuti wakumbukira

kudzichepetsa kwa mtumiki wake.

Kuyambira tsopano mibado yonse idzanditcha wodala,

pakuti Wamkuluyo wandichitira ine zinthu zazikulu,

dzina lake ndi loyera.

Chifundo chake chifikira kwa iwo amene amuopa Iye

kufikira mibadomibado.

Iye wachita zamphamvu ndi dzanja lake;

Iye anabalalitsa iwo amene ali onyada mʼmaganizo awo.

Iye anachotsa olamulira pa mipando yawo yaufumu,

koma wakweza odzichepetsa.

Iye wakhutitsa a njala ndi zinthu zabwino

koma anachotsa olemera wopanda kanthu.

Iye anathandiza mtumiki wake Israeli,

pokumbukira chifundo chake.

Kwa Abrahamu ndi zidzukulu zake ku nthawi zonse

monga ananena kwa makolo athu."

Choncho Yosefe anachoka ku Nazareti ku Galileya kupita ku Yudeya, ku Betelehemu ku mudzi wa Davide, chifukwa anali wa banja ndi fuko la Davide. Iye anapita kumeneko kukalembetsa pamodzi ndi Mariya, amene anapalana naye ubwenzi kuti akwatirane ndipo anali woyembekezera. Ali kumeneko, nthawi inakwana yakuti mwana abadwe, ndipo anabereka mwana wake woyamba, wamwamuna. Iye anamukulunga mʼnsalu ndi kumuyika modyera ngʼombe, chifukwa kunalibe malo mʼnyumba ya alendo.

Koma Mariya anasunga zonsezi mu mtima mwake ndi kumazilingalira.

Kenaka Simeoni anawadalitsa ndipo anati kwa Mariya amayi ake: "Mwana uyu wakonzedwa kukhala kugwa ndi kudzuka kwa ambiri mu Israeli, ndi kukhala chizindikiro chimene adzayankhula motsutsana nacho, kotero kuti malingaliro a mitima ya ambiri adzawululidwa. Ndipo lupanga lidzabaya moyo wakonso."

Makolo ake atamuona, anadabwa. Amayi ake anati kwa Iye, "Mwanawe, watichitira zimenezi chifukwa chiyani? Abambo ako ndi ine takhala tili ndi nkhawa kukufunafuna Iwe."

Iye anawafunsa kuti, "Nʼchifukwa chiyani mumandifunafuna? Kodi simukudziwa kuti ndikuyenera kukhala mʼnyumba ya Atate anga?" Koma iwo sanazindikire chomwe Iye amatanthauza.

Kenaka anapita nawo ku Nazareti ndipo anawamvera iwo. Koma amayi ake anasunga zinthu zonsezi mu mtima mwawo.

Mãe fiel até o fim

Maria acompanhou Jesus desde o nascimento até a cruz. Ela estava entre os discípulos no Pentecostes, fiel em oração.

Vinyo atatha, amayi a Yesu anati kwa Iye, "Wawathera vinyo."

Yesu anayankha kuti, "Amayi, chifukwa chiyani mukundiwuza Ine? Nthawi yanga sinakwane."

Amayi ake anati kwa antchito, "Inu muchite chilichonse chimene akuwuzeni."

Pafupi ndi mtanda wa Yesu panayima amayi ake, mngʼono wa amayi ake, Mariya mkazi wa Kaliyopa ndi Mariya wa ku Magadala. Yesu ataona amayi ake pamenepo ndi wophunzira amene Iye anamukonda atayima pafupipo, Iye anati kwa amayi ake, "Amayi nayu mwana wanu." Anawuzanso wophunzirayo kuti, "Nawa amayi ako." Kuyambira nthawi imeneyo, wophunzirayo anatenga amayiwo kupita nawo kwawo.

Amayi ndi Abale ake a Yesu

Pamenepo amayi ndi abale ake a Yesu anafika. Atayima kunja, anatuma wina kuti akamuyitane Iye. Gulu la anthu linakhala momuzungulira Iye, ndipo anamuwuza kuti, "Amayi ndi abale anu ali panja akukufunani."

Iye anafunsa kuti, "Amayi ndi abale anga ndi ndani?"

Pamenepo anayangʼana anthu amene anakhala momuzungurira ndipo anati, "Awa ndi amayi anga ndi abale anga! Aliyense amene achita chifuniro cha Mulungu ndi mʼbale wanga ndi mlongo wanga ndi amayi anga."

Kodi si mwana wa wopala matabwa? Kodi dzina la amayi ake si Mariya ndipo kodi abale ake si Yakobo, Yosefe, Simoni ndi Yudasi? Kodi alongo ake onse sali ndi ife? Tsono ndi kuti kumene anazitenga zinthu izi?"

Onsewa ndi mtima umodzi anapitiriza kupemphera pamodzi ndi amayi, ndi Mariya amayi ake a Yesu, ndiponso abale ake a Yesu.

Seja o primeiro

Este artigo te tocou? Faça uma oração!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.