O marido
A Bíblia define o papel do marido com clareza: amar a esposa como Cristo amou a Igreja, ser fiel, protetor e líder servo no lar.
Amar como Cristo amou
Maridos, amai vossas mulheres como Cristo amou a Igreja e se entregou por ela. O amor do marido deve ser sacrificial e incondicional.
Inu amuna, kondani akazi anu monga momwe Khristu anakondera mpingo nadzipereka yekha mʼmalo mwa mpingowo
Momwemonso, amuna akuyenera kukonda akazi awo monga matupi awo. Iye amene akonda mkazi wake adzikondanso yekha.
Momwemonso, amuna akuyenera kukonda akazi awo monga matupi awo. Iye amene akonda mkazi wake adzikondanso yekha. Pakuti palibe amene amadana nalo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulisamalira bwino, monga momwe Khristu amachitira ndi mpingo wake
Chomwecho, aliyense mwa inu akuyenera kukonda mkazi wake monga adzikondera iye mwini, ndipo mkazi akuyenera kulemekeza mwamuna wake.
Chifukwa chake, aliyense wa inu aleke kunama ndipo ayankhule zoona kwa mʼbale wake, pakuti ife tonse ndife ziwalo za thupi limodzi. Kwiyani koma musachimwe. Dzuwa lisalowe mukanali chikwiyire. Musamupatse mpata Satana. Iye amene wakhala akuba asabenso, koma agwire ntchito ndi kuchita kenakake kaphindu ndi manja ake, kuti akhale ndi kenakake kogawana ndi amene akusowa.
Mʼkamwa mwanu musatuluke mawu aliwonse onyansa, koma okhawo amene ndi othandiza kulimbikitsa ena molingana ndi zosowa zawo, kuti athandize amene akawamve. Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu amene mwasindikizidwa naye chizindikiro cha tsiku la kuwomboledwa. Chotsani kuzondana, ukali ndi kupsa mtima, chiwawa ndi kuyankhula zachipongwe, pamodzi ndi choyipa chilichonse. Mukomerane mtima ndi kuchitirana chifundo wina ndi mnzake. Khululukiranani wina ndi mnzake, monga momwe Mulungu anakukhululukirani mwa Khristu.
Inu amuna, kondani akazi anu ndipo musawapsere mtima.
Malangizo a Moyo wa Mʼbanja la Chikhristu
Inu akazi, gonjerani amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye.
Inu amuna, kondani akazi anu ndipo musawapsere mtima.
Ndipo kuwonjezera pa zonsezi valani chikondi, chimene chimangirira zonsezi pamodzi mu mgwirizano wangwiro.
Fidelidade conjugal
O casamento é honroso e o leito conjugal é santo. O marido deve ser fiel à esposa da sua juventude em pensamento e ação.
Ukwati muziwulemekeza nonse, ndipo mwamuna ndi mkazi azikhala wokhulupirika, pakuti anthu adama ndi achigololo Mulungu adzawalanga.
Imwa madzi a mʼchitsime chakochako,
madzi abwino ochokera mʼchitsime chako.
Kodi akasupe ako azingosefukira mʼmisewu?
Kodi mitsinje yako izingoyendayenda mʼzipata za mzinda?
Mitsinjeyo ikhale ya iwe wekha,
osati uyigawireko alendo.
Yehova adalitse kasupe wako,
ndipo usangalale ndi mkazi wa unyamata wako.
Iye uja ali ngati mbalale yayikazi yokongola ndiponso ngati gwape wa maonekedwe abwino.
Ukhutitsidwe ndi mawere ake nthawi zonse,
ndipo utengeke ndi chikondi chake nthawi zonse.
Mwana wanga, nʼchifukwa chiyani ukukopeka ndi mkazi wachigololo?
Bwanji ukukumbatira mkazi wachilendo?
Koma Ine ndikuwuzani kuti aliyense woyangʼana mkazi momusirira wachita naye kale chigololo mu mtima mwake.
Koma Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene asudzula mkazi wake pa chifukwa china chilichonse osati chifukwa cha chiwerewere, akumuchititsa mkaziyo chigololo ndipo aliyense wokwatira mkaziyo, akuchitanso chigololo.
Motero salinso awiri ayi koma mmodzi. Nʼchifukwa chake chimene Mulungu wachimanga pamodzi munthu wina asachilekanitse."
Mwamuna akwaniritse udindo wake wa pa banja kwa mkazi wake, ndipo chimodzimodzi mkazi kwa mwamuna wake. Thupi la mkazi wokwatiwa si la iye mwini yekha koma ndi la mwamuna wakenso. Momwemonso, thupi la mwamuna si la iye mwini yekha koma ndi la mkazi wakenso.
Musamakanizane, pokhapokha mutagwirizana awiri kuti mwakanthawi mudzipereke kumapemphero. Kenaka mukhalirenso pamodzi kuopa kuti Satana angakuyeseni chifukwa cholephera kudziretsa.
Kwa amene ali pa banja ndikupatsani lamulo ili (osati langa koma la Ambuye): Mkazi asalekane ndi mwamuna wake. Koma ngati atatero, asakwatiwenso, apo ayi, abwerere kwa mwamuna wakeyo. Ndipo mwamuna asaleke mkazi wake.
Kwa ena onse ndikunena izi (ineyo osati Ambuye); ngati mʼbale wina ali ndi mkazi wosakhulupirira ndipo mkaziyo walola kukhala pa banja ndi mʼbaleyo, ameneyo asamuleke.
Thawani dama. Machimo onse amene munthu amachita amakhala kunja kwa thupi lake, koma amene amachita machimo okhudza chigololo, amachimwira thupi lake lomwe.
Convivência com sabedoria
O marido sábio vive com a esposa com entendimento, dando-lhe honra como co-herdeira da graça. A união conjugal reflete Cristo e a Igreja.
Momwemonso amuna inu, khalani mwanzeru ndi akazi anu, ndipo muwachitire ulemu monga anzanu ofowoka ndiponso olandira nanu pamodzi mphatso ya moyo wosatha, kuti pasakhale kanthu kotsekereza mapemphero anu.
Nʼchifukwa chake, mwamuna amasiya abambo ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake ndipo awiriwo amakhala thupi limodzi.
Musachite kalikonse ndi mtima odzikonda chabe kapena odzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa ndipo aliyense aziona mnzake ngati womuposa iyeyo. Musamangofuna zokomera inu nokha koma aliyense azifuna zokomeranso ena.
Uzikondwerera moyo pamodzi ndi mkazi wako amene umamukonda, masiku onse a moyo uno wopanda phindu, amene Mulungu wakupatsa pansi pano. Pakuti mkaziyo ndiye gawo la moyo wako pa ntchito yako yolemetsa pansi pano.
Wapeza mkazi wapeza chinthu chabwino
ndipo Yehova amamukomera mtima.
Onetsetsani kuti wina asabwezere choyipa kwa omuchitira choyipa koma nthawi zonse yesetsani kukhala okoma mtima kwa wina ndi mnzake; ndiponso ndi kwa anthu ena onse.
Koma ngati kutumikira Yehova kukuyipirani, sankhani lero amene mudzamutumikire, kapena milungu imene makolo anu ankayitumikira kutsidya kwa mtsinje wa Yufurate, kapena milungu ya Aamori, amene mukukhala mʼdziko lawo. Koma ine ndi banja langa, tidzatumikira Yehova."
Kukhala Pamodzi ndi Osakhulupirira
Musamasenze goli pamodzi ndi osakhulupirira. Kodi pali mgwirizano wanji pakati pa kulungama ndi kusalungama? Kapena kodi pali mgwirizano wanji pakati pa kuwala ndi mdima?
Chikondi nʼcholeza mtima, chikondi nʼchokoma mtima, chilibe nsanje, sichidzikuza, sichidzitamandira. Chikondi chilibe mwano, sichodzikonda, sichipsa mtima msanga, sichisunga mangawa. Chikondi sichikondwera ndi zoyipa koma chimakondwera ndi choonadi. Chimatchinjiriza nthawi zonse, chimakhulupirika nthawi zonse, chimakhala ndi chiyembekezo nthawi zonse, chimapirira nthawi zonse.