Publicidade

Mentira

Por Bíblia Online

A mentira é condenada pela Bíblia como pecado grave. Deus é verdade, e quem mente se alinha com o pai da mentira. O cristão é chamado a falar a verdade em amor.

Deus odeia a mentira

Os lábios mentirosos são abominação para o Senhor. A Bíblia adverte que todo mentiroso terá parte no lago de fogo.

Pakamwa pa bodza pamamunyansa Yehova,

koma amakondwera ndi anthu oyankhula zoona.

Koma amantha, osakhulupirira, okonda zonyansa, opha anthu, achiwerewere, amatsenga, opembedza mafano ndi abodza, malo awo adzakhala nyanja yamoto ya sulufule wotentha. Iyi ndi imfa yachiwiri."

Pali zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Yehova amadana nazo,

zinthu zisanu ndi ziwiri zimene zimamunyansa:

maso onyada,

pakamwa pabodza,

manja akupha munthu wosalakwa,

mtima wokonzekera kuchita zoyipa,

mapazi othamangira msanga ku zoyipa,

mboni yonama yoyankhula mabodza

komanso munthu amene amayambitsa mikangano pakati pa abale.

Musanamizane wina ndi mnzake, popeza munavula munthu wakale pamodzi ndi zochita zake

Falar a verdade

Despojai-vos da mentira e falai a verdade cada um com o próximo. Cristo é a verdade, e nos chama a ser testemunhas fiéis.

Chifukwa chake, aliyense wa inu aleke kunama ndipo ayankhule zoona kwa mʼbale wake, pakuti ife tonse ndife ziwalo za thupi limodzi.

Yesu anayankha kuti, "Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate popanda kudzera mwa Ine.

Inu ndinu ana a mdierekezi. Iye ndiye abambo anu ndipo mukufuna kuchita zimene abambo anuwo amakhumba. Iye anali wakupha kuyambira pachiyambi, sanasunge choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene Iye anena bodza, amayankhula chiyankhulo chobadwa nacho, popeza ndi wabodza ndipo ndi bambo wa mabodza.

Mboni yonama sidzalephera kulangidwa,

ndipo iye amene amanena mabodza adzawonongeka.

Aliyense wochita chinyengo

sadzakhala mʼnyumba mwanga.

Aliyense woyankhula mwachinyengo

sadzayima pamaso panga.

Consequências da falsidade

A mentira destrói confiança e relacionamentos. As Escrituras alertam sobre os frutos amargos do engano e da falsidade.

Chuma chochipeza ndi mawu onyenga ndi chosakhalitsa

ndipo chimakola anthu mu msampha wa imfa.

Mawu woona amakhala mpaka muyaya

koma mawu abodza sakhalitsa.

Munthu wonama amadana ndi amene anawapweteka,

ndipo pakamwa poshashalika pamabweretsa chiwonongeko.

Mumawononga iwo amene amanena mabodza;

anthu akupha ndi achinyengo,

Yehova amanyansidwa nawo.

" Musabe.

" Musamanamizane.

" Musachitirane zinthu mwachinyengo.

Seja o primeiro
Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-