Milagres de Jesus
Os Evangelhos registram dezenas de milagres realizados por Jesus — curas, ressurreições, domínio sobre a natureza e libertações. Cada milagre revelava sua divindade e compaixão.
Curas de cegos e surdos
Jesus devolveu a visão aos cegos e a audição aos surdos, manifestando seu poder sobre toda enfermidade e deficiência.
Yesu Achiritsa Osaona ndi Osayankhula
Yesu atapitirira ulendo wake, amuna awiri osaona anamutsatira Iye, akufuwula kuti, "Tichitireni chifundo, Mwana wa Davide!"
Atalowa mʼnyumba, amuna awiri osaonawo anabwera kwa Iye ndipo anawafunsa kuti, "Kodi mukhulupirira kuti ndikhoza kukuchiritsani?"
Iwo anayankha kuti, "Inde Ambuye."
Pomwepo anakhudza maso awo nati, "Zichitike kwa inu monga mwachikhulupiriro chanu." Ndipo anayamba kuona. Yesu anawachenjeza kwambiri nati, "Onani, wina aliyense asadziwe za zimenezi." Koma iwo anatuluka mʼnyumbamo nafalitsa za Iye mʼchigawo chonse.
Yesu Achiritsa Anthu Awiri Osaona
Pamene Yesu ndi ophunzira ake ankachoka ku Yeriko, gulu lalikulu la anthu linawatsata. Amuna awiri osaona anakhala mʼmbali mwa msewu, ndipo pamene anamva kuti Yesu akudutsa anafuwula kuti, "Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!"
Gulu la anthulo linawadzudzula iwo ndi kuwawuza kuti akhale chete, koma anafuwulitsabe kuti, "Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!"
Yesu anayima ndi kuwayitana ndipo anawafunsa kuti, "Mukufuna ndikuchitireni chiyani?"
Anamuyankha nati, "Ambuye, tikufuna tione!"
Yesu anamva nawo chifundo ndipo anakhudza maso awo. Nthawi yomweyo anaona namutsata Iye.
Kuchiritsidwa kwa Munthu Wosaona ku Betisaida
Iwo anafika ku Betisaida, ndipo anthu ena anabweretsa munthu wosaona ndipo anamupempha Yesu kuti amukhudze. Iye anagwira dzanja la munthu wosaonayo napita naye kunja kwa mudzi. Atalavulira mʼmaso a munthuyo ndi kumusanjika manja, Yesu anafunsa kuti, "Kodi ukuona kalikonse?"
Iye anakweza maso nati, "Ndikuona anthu; akuoneka ngati mitengo imene ikuyendayenda."
Kenakanso Yesu anayika manja ake mʼmaso a munthuyo. Ndipo maso ake anatsekuka, naonanso, ndipo anaona zonse bwinobwino. Yesu anamuwuza kuti apite kwawo nati, "Usapite mʼmudzimo."
Kuchiritsidwa kwa Munthu Wosamva ndi Wosayankhula
Ndipo Yesu anachoka ku dera la Turo nadutsa pakati pa Sidoni, kutsikira ku nyanja ya Galileya kupita ku dera la Dekapoli. Kumeneko anthu ena anabweretsa kwa Iye munthu amene anali wosamva ndi wosayankhula, ndipo anamupempha kuti asanjike dzanja pa iye.
Atamutengera iye pambali, patali ndi gulu la anthu, Yesu analowetsa zala zake mʼmakutu a munthuyo. Kenaka anapaka malovu pachala ndi kukhudza lilime la munthuyo. Iye anayangʼana kumwamba ndipo ndi mawu otsitsa moyo, anati kwa iye, "Efataa!" (Kutanthauza kuti, "Tsekuka!") Atachita izi, makutu a munthuyo anatsekuka komanso lilime lake linamasuka ndipo anayamba kuyankhula momveka bwino.
Yesu anawalamula kuti asawuze wina aliyense. Koma pamene anapitiriza kuwaletsa, iwo anapitiriza kuyankhula za izi. Anthu anadabwa kwambiri. Iwo anati, "Wachita zonse bwino, ngakhale Iyenso atsekula makutu a osamva ndi osayankhula kuti ayankhule."
Bartumeyu Wosaona
Ndipo anafika ku Yeriko. Pamene Yesu ndi ophunzira ake, pamodzi ndi gulu lalikulu la anthu, ankatuluka mu mzinda, munthu wosaona, Bartumeyu (mwana wa Tumeyu), amakhala mʼmbali mwa msewu ali kupempha. Pamene anamva kuti anali Yesu wa ku Nazareti, anayamba kufuwula kuti, "Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!"
Ambiri anamukalipira ndi kumuwuza kuti akhale chete, koma iye anafuwulitsabe kuti, "Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!"
Yesu anayima nati, "Muyitaneni." Ndipo anamuyitana kuti, "Kondwera! Imirira! Akukuyitana." Anaponya mkanjo wake kumbali, analumpha nabwera kwa Yesu.
Yesu anamufunsa kuti, "Ukufuna ndikuchitire chiyani?"
Wosaonayo anayankha kuti, "Aphunzitsi, ndikufuna ndione."
Yesu anati, "Pita, chikhulupiriro chako chakuchiritsa!" Nthawi yomweyo anapenya, nʼkumatsatira Yesu pa ulendowo.
Yesu Achiritsa Wosaona
Yesu atayandikira ku Yeriko, munthu wina wosaona amene amakhala pambali pa msewu namapempha, anamva gulu la anthu likudutsa. Iye anafunsa chomwe chimachitika. Iwo anamuwuza kuti "Yesu wa ku Nazareti akudutsa."
Iye anayitana mofuwula, "Yesu Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!"
Iwo amene amamutsogolera njira anamudzudzula ndi kumuwuza kuti akhale chete, koma iye anafuwulabe, "Mwana wa Davide, chitireni chifundo!"
Yesu anayima nalamula kuti abwere naye kwa Iye. Atabwera pafupi, Yesu anamufunsa kuti, "Kodi ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?"
Iye anayankha kuti, "Ambuye, ine ndifuna ndionenso."
Yesu anati kwa iye, "Onanso; chikhulupiriro chako chakupulumutsa." Nthawi yomweyo anaonanso ndipo anayamba kumutsatira Yesu, akulemekeza Mulungu. Anthu onse ataona izi, iwonso analemekeza Mulungu.
Yesu Achiritsa Munthu Wosaona Chibadwire
Iye akuyendabe, anaona munthu wosaona chibadwire. Ophunzira ake anamufunsa Iye kuti, "Rabi anachimwa ndani, munthuyu kapena makolo ake, kuti iye abadwe wosaona?"
Yesu anayankha kuti, "Sikuti iyeyu anachimwa kapena makolo ake, koma izi zinachitika kuti Mulungu aonetse ntchito zake mwa iyeyu. Ife tiyenera kugwira ntchito za Iye amene anandituma kukanali masana. Usiku ukubwera, pamene wina aliyense sadzagwira ntchito. Pamene Ine ndili mʼdziko lapansi, Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi."
Atanena izi, Iye anathira malovu pansi ndi kukanda dothi, napaka matopewo mʼmaso a munthuyo. Yesu anamuwuza iye kuti, "Pita kasambe mʼdziwe la Siloamu" (mawu awa akutanthauza Wotumidwa). Choncho munthuyo anapita ndi kukasamba ndipo anabwerako akupenya.
Curas de paralíticos e enfermos
Paralíticos caminharam, leprosos ficaram limpos e todo tipo de doença foi curada pelo toque e pela palavra de Jesus.
Ndipo munthu wakhate anadza kwa Yesu namugwadira nati, "Ambuye, ngati mufuna, mukhoza kundiyeretsa."
Yesu anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo nati, "Ndikufuna, yeretsedwa!" Nthawi yomweyo anachiritsidwa khate lake. Ndipo Yesu anati kwa iye, "Taona, usawuze wina aliyense. Koma upite kwa mkulu wa ansembe ukadzionetse wekha ndi kupereka mphatso imene Mose analamulira, kuti ukhale umboni kwa iwo."
Amuna ena anabwera ndi munthu wakufa ziwalo kwa Iye atamugoneka pa mphasa. Yesu ataona chikhulupiriro chawo anati kwa wakufa ziwaloyo, "Limba mtima mwana wanga, machimo ako akhululukidwa."
Pamenepo aphunzitsi ena amalamulo anaganiza mu mtima mwawo kuti, "Munthu uyu akuchitira Mulungu mwano."
Ndipo podziwa maganizo awo Yesu anati, "Bwanji mukuganiza zoyipa mʼmitima mwanu? Chapafupi ndi chiti kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa’ kapena kunena kuti, ‘Imirira ndipo yenda?’ Tsono kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro pa dziko wokhululuka machimo, pamenepo anati kwa wakufa ziwaloyo, ‘Imirira, tenga mphasa yako kazipita kwanu.’ " Ndipo munthuyo anayimirira napita kwawo.
Ndipo mʼmenemo munali munthu wolumala dzanja. Pofuna chifukwa chokamunenezera, iwo anamufunsa Yesu kuti, "Kodi nʼkololedwa kuchiritsa munthu tsiku la Sabata?"
Iye anawawuza kuti, "Ngati wina wa inu ali ndi nkhosa nigwera mʼdzenje tsiku la Sabata, kodi simudzayigwira ndi kuyitulutsa kunja? Nanga munthu sali oposa nkhosa kwambiri! Chifukwa chake nʼkololedwa kuchita zabwino pa Sabata."
Pamenepo Yesu anati kwa munthuyo, "Wongola dzanja lako." Iye analiwongola ndipo linakhala monga linalili kale.
Mpongozi wa Simoni anali chigonere akudwala malungo, ndipo anamuwuza Yesu za iye. Ndipo Yesu anapita kwa iye, namugwira dzanja namuthandiza kudzuka. Malungo anachoka ndipo anayamba kuwatumikira.
Yesu Achiritsa Wakhate
Munthu wakhate anabwera kwa Iye, nagwada, namupempha kuti, "Ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa."
Yesu pomva naye chifundo, anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo nati, "Ndikufuna, yeretsedwa!" Nthawi yomweyo khate linachoka ndipo anachiritsidwa.
Amuna anayi anabwera, atanyamula munthu wofa ziwalo. Popeza sakanatha kufika naye kwa Yesu chifukwa cha gulu la anthu, anasasula denga chapamwamba pamene panali Yesu, ndipo atabowoleza, anatsitsa mphasa yomwe munthu wofa ziwaloyo anagonapo. Yesu ataona chikhulupiriro chawo, anati kwa wofa ziwaloyo, "Mwana, machimo ako akhululukidwa."
Ndipo ena mwa aphunzitsi amalamulo anakhala pansi pomwepo, namaganiza mʼmitima mwawo kuti, "Nʼchifukwa chiyani munthuyu ayankhula chotere? Iye akuchitira mwano Mulungu! Ndani angakhululukire munthu machimo kupatula Mulungu yekha?"
Nthawi yomweyo Yesu anadziwa mu mzimu wake kuti izi ndi zimene ankaganiza mʼmitima yawo, ndipo anawawuza kuti, "Chifukwa chiyani mukuganiza zinthu izi? Chapafupi nʼchiyani; kunena kwa wofa ziwaloyu kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kuti, ‘Imirira, tenga mphasa yako ndipo yenda?’ Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro pa dziko lapansi wokhululukira machimo." Anati kwa wofa ziwaloyo, "Ndikuwuza iwe, imirira, tenga mphasa yako ndipo pita kwanu." Anayimirira, nanyamula mphasa yake natuluka onse akumuona. Izi zinadabwitsa aliyense ndipo anayamika Mulungu nati, "Sitinaonepo zinthu ngati izi!"
Yesu Achiritsa Wolumala Dzanja
Nthawi inanso analowa mʼsunagoge, ndipo munthu wa dzanja lolumala anali momwemo. Ena a iwo anafunafuna chifukwa chakuti akamuneneze Yesu, potero anamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati angamuchiritse tsiku la Sabata. Yesu anati kwa munthu wolumala dzanjayo, "Imirira, bwera kuno kutsogolo."
Ndipo Yesu anawafunsa kuti, "Kodi chololedwa ndi chiyani pa tsiku la Sabata: kuchita chabwino kapena kuchita choyipa, kupulumutsa moyo kapena kupha?" Koma iwo anakhala chete.
Yesu anawayangʼana ndi mkwiyo ndipo powawidwa mtima chifukwa cha mitima yawo yowuma anati kwa munthuyo, "Wongola dzanja lako." Iye analiwongola, ndipo dzanja lake linachira.
Yesu Achiritsa Munthu Wakhate
Yesu ali ku mudzi wina, munthu amene anali ndi khate thupi lonse anabwera kwa Iye. Munthuyo ataona Yesu, anagwa chafufumimba ndipo anamupempha Iye kuti, "Ambuye, ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa."
Yesu anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo. Iye anati, "Ine ndikufuna, yeretsedwa!" Ndipo nthawi yomweyo khate lake linachoka.
Amuna ena anabwera atanyamula munthu wofa ziwalo pa mphasa ndipo anayesa kumulowetsa mʼnyumba kuti amugoneke pamaso pa Yesu. Atalephera kupeza njira yochitira zimenezi chifukwa cha gulu la anthu, anakwera naye pa denga ali pa mphasa pomwepo ndi kumutsitsira mʼkati pakati pa gulu la anthu, patsogolo penipeni pa Yesu.
Yesu ataona chikhulupiriro chawo, anati, "Mnzanga, machimo ako akhululukidwa."
Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo anayamba kuganiza mwa iwo okha kuti, "Kodi munthu uyu ndi ndani amene ayankhula zamwano? Kodi ndani amene angakhululukire machimo kupatula Mulungu?"
Yesu anadziwa zomwe iwo amaganiza ndipo anafunsa kuti, "Kodi ndi chifukwa chiyani mukuganiza zimenezi mʼmitima mwanu? Kodi chapafupi ndi chiti: kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Nyamuka ndipo yenda?’ " Koma kuti inu mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro pa dziko lapansi wokhululukira machimo, Iye anati kwa munthu wofa ziwaloyo, "Ine ndikuwuza iwe kuti, ‘Imirira, nyamula mphasa ndipo uzipita kwanu.’ " Nthawi yomweyo anayimirira patsogolo pawo, nanyamula mphasa yake ndipo anapita kwawo akuyamika Mulungu.
La Sabata lina Iye analowa mʼsunagoge kukaphunzitsa ndipo mʼmenemo anapeza munthu wadzanja lolumala. Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo ankamuyangʼana kuti apeze chifukwa Yesu, choncho anamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati Iye akanamuchiritsa pa Sabata. Koma Yesu anadziwa zimene ankaganiza ndipo anati kwa munthu wadzanja lolumalayo, "Tanyamuka ndipo uyime patsogolo pa onsewa." Choncho iye ananyamuka nayima pamenepo.
Kenaka Yesu anawawuza kuti, "Ndikufunseni, kodi chololedwa pa Sabata ndi chiti: kuchita chabwino kapena kuchita choyipa, kupulumutsa moyo kapena kuwononga?"
Iye atawayangʼana onsewo, anati kwa munthuyo, "Wongola dzanja lako." Iye anaterodi, ndipo dzanja lake linachiritsidwa.
Chikhulupiriro cha Kenturiyo
Yesu atamaliza kunena zonsezi pamaso pa anthu amene ankamvetsera, analowa mu Kaperenawo. Kumeneko wantchito wa Kenturiyo, amene amamukhulupirira kwambiri, anadwala ndipo anali pafupi kufa. Kenturiyo anamva za Yesu ndipo anatumiza ena a akulu Ayuda kwa Iye kuti abwere adzachiritse wantchito wakeyo. Iwo atafika kwa Yesu, anamudandaulira kwambiri, nati, "Munthuyu ayenera kuthandizidwa chifukwa amakonda mtundu wathu ndipo anatimangira sunagoge wathu." Pamenepo Yesu anapita nawo.
Iye sanali patali ndi nyumba pamene Kenturiyo anatumiza anzake kuti akamuwuze kuti, "Ambuye, musadzivutitse, pakuti ndine wosayenera kuti mulowe mʼnyumba mwanga. Nʼchifukwa chake sindinadziyenereze ndi pangʼono pomwe kuti ndibwere kwa inu. Koma nenani mawu, ndipo wantchito wanga adzachira. Pakuti ndili pansi paulamuliro, ndiponso ndili ndi asilikali pansi panga. Ndikamuwuza uyu kuti, ‘Pita,’ iye amapita; ndi uyo kuti, ‘Bwera,’ amabwera. Ndikamuwuza wantchito wanga kuti, ‘Chita ichi,’ amachita."
Yesu atamva izi, anadabwa naye, ndipo anatembenukira gulu la anthu limene limamutsatira nati, "Ndikukuwuzani kuti, sindinapeze chikhulupiriro chachikulu ngati ichi mu Israeli." Kenaka anthu amene anatumidwawo anabwerera ku nyumba ndipo anakamupeza wantchitoyo atachira.
ndipo momwemo munali mayi amene anali ndi mzimu woyipa umene unamudwalitsa zaka 18. Iye anali wokhota msana ndipo samatha kuweramuka ndi pangʼono pomwe. Yesu atamuona anamuyitana kutsogolo ndipo anati kwa iye, "Amayi, mwamasulidwa ku mavuto." Kenaka anasanjika manja ake pa iye, ndipo nthawi yomweyo anawongoka nayamika Mulungu.
Yesu Mʼnyumba ya Mfarisi
Pa tsiku lina la Sabata, Yesu atapita kukadya ku nyumba ya Mfarisi wodziwika, Afarisi anamulonda mosamalitsa. Poteropo, patsogolo pake panali munthu amene anadwala matenda otupa mimba ndi miyendo. Yesu anafunsa Afarisi ndi akatswiri amalamulo kuti, "Kodi ndi zololedwa kuchiritsa pa tsiku la Sabata kapena ayi?" Koma iwo sanayankhe. Tsono atamutenga munthuyo, Iye anamuchiritsa ndipo anamuwuza kuti azipita.
Yesu Achiritsa Akhate Khumi
Tsopano Yesu anayenda mʼmalire a pakati pa Samariya ndi Galileya pa ulendo wake wa ku Yerusalemu. Akulowa mʼmudzi wina, amuna khumi amene anali ndi khate anakumana naye. Iwo anayima patali ndipo anafuwula ndi mawu okweza kuti, "Yesu, Ambuye, tichitireni chifundo!"
Iye atawaona, anati, "Pitani kadzionetseni nokha kwa ansembe." Ndipo pamene iwo ankapita, anachiritsidwa.
Mmodzi wa iwo, ataona kuti wachiritsidwa, anabwerera, nayamika Mulungu ndi mawu okweza. Anagwetsa nkhope yake nagwa pa mapazi a Yesu ndi kumuthokoza. Ndipo iye anali Msamariya.
Yesu anafunsa kuti, "Kodi amene anachiritsidwa sanalipo khumi? Nanga asanu ndi anayi ena ali kuti? Kodi palibe mmodzi mwa iwo amene anabwerera kudzalemekeza Mulungu kupatula mlendoyu?" Pamenepo anati kwa iye, "Imirira ndipo pita; chikhulupiriro chako chakuchiritsa iwe."
Yesu Achiritsa Munthu pa Sabata
Patapita nthawi Yesu anakwera kupita ku Yerusalemu ku phwando la Ayuda. Ndipo ku Yerusalemuko pafupi ndi chipata cha Nkhosa kuli dziwe limene mʼChihebri limatchedwa Betisaida ndipo ndi lozunguliridwa ndi makumbi asanu. Mʼmenemo munkagonamo gulu lalikulu la anthu odwala, osaona, olumala ndi ofa ziwalo. Pakuti nthawi zina mngelo wa Ambuye ankatsikira mʼdziwemo nʼkuvundula madziwo. Woyamba kulowamo madzi atavundulidwa, ankachira ngakhale akhale ndi nthenda yanji. Mmodzi wa amene anali pamenepo anali atadwala zaka 38. Yesu atamuona ali chigonere, nadziwa kuti anakhala chotero kwa nthawi yayitali, anamufunsa iye kuti, "Kodi ukufuna kuchira?"
Wodwalayo anayankha kuti, "Ambuye, ndilibe wina aliyense woti angandithandize kulowa mʼdziwe pamene madzi avundulidwa. Pamene ndikuyesera kuti ndilowemo, wina amalowamo ine ndisanalowemo."
Ndipo Yesu anati kwa iye, "Imirira! Nyamula mphasa yako yamba kuyenda." Nthawi yomweyo munthuyo anachiritsidwa. Iye ananyamula mphasa yake nayamba kuyenda.
Tsiku limene izi zinachitika linali la Sabata.
Iye anakafikanso ku Kana wa ku Galileya, kumene anasanduliza madzi kukhala vinyo. Ndipo kumeneko kunali nduna ina ya mfumu imene mwana wake wamwamuna anali chigonere akudwala ku Kaperenawo. Munthu uyu atamva kuti Yesu wafika ku Galileya kuchokera ku Yudeya, anapita kwa Iye, namupempha kuti apite akachiritse mwana wakeyo, amene anali pafupi kufa.
Yesu anawawuza iwo kuti, "Anthu inu pokhapokha mutaona zizindikiro zodabwitsa, simudzakhulupirira."
Nduna ya mfumuyo inati, "Ambuye tiyeni mwana wanga asanafe."
Yesu anayankha kuti, "Pita. Mwana wako adzakhala ndi moyo."
Munthuyo anakhulupirira mawu a Yesu ndipo ananyamuka. Iye ali pa njira, antchito ake anakumana naye, namuwuza kuti mwana wanu uja wachira. Iye atafunsa kuti ndi nthawi yanji imene mwana wake anapeza bwino, iwo anati kwa iye, "Malungo anamusiya iye dzulo pa ora lachisanu ndi chiwiri."
Ndipo bamboyo anazindikira kuti iyi inali nthawi yomweyo imene Yesu anati kwa iye, "Mwana wako adzakhala ndi moyo." Choncho iye ndi onse a pa banja lake anakhulupirira.
Ichi ndiye chinali chizindikiro chodabwitsa chachiwiri chimene Yesu anachita atafika ku Galileya kuchokera ku Yudeya.
A mulher com fluxo de sangue
Uma mulher que sofria há doze anos tocou a orla do manto de Jesus e foi curada instantaneamente pela sua fé.
Panali mayi wina amene ankadwala nthenda yotaya magazi kwa zaka khumi ndi ziwiri ndipo anadza mʼmbuyo mwake nakhudza mkanjo wake. Iyeyo anati mwa iye yekha, "Nditangokhudza kasonga ka mkanjo wake, ine ndidzachiritsidwa."
Ndipo Yesu anatembenuka namuona mayiyo nati, "Limbani mtima mayi iwe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa." Nthawi yomweyo mayiyo anachiritsidwa.
Pomwepo panali mayi amene amadwala nthenda yotaya magazi kwa zaka khumi ndi ziwiri. Iye anavutika kwambiri pamene asingʼanga ambiri ankamusamalira ndipo anagwiritsa ntchito zonse anali nazo, koma mʼmalo mochira, nthenda yake inkakulakulabe. Atamva za Yesu, anabwera kumbuyo kwake mʼgulu la anthu ndipo anakhudza mkanjo wake, chifukwa anaganiza kuti, "Ngati nditangokhudza mkanjo wake, ndidzachiritsidwa." Nthawi yomweyo magazi ake analeka kutuluka ndipo anamva mʼthupi mwake kuti wamasulidwa ku vuto lake.
Ndipo pomwepo panali mayi wina amene ankataya magazi kwa zaka khumi ndi ziwiri, koma panalibe wina akanamuchiritsa. Iye anafika kumbuyo kwake ndi kukhudza mothera mwa chovala chake, ndipo nthawi yomweyo magazi ake analeka kutuluka.
Yesu anafunsa kuti, "Wandikhudza ndani?"
Onse atakana, Petro anati, "Anthu akukupanikizani ndi kukukankhani."
Koma Yesu anati, "Wina wandikhudza; ndikudziwa chifukwa mphamvu yachoka mwa Ine."
Ndipo mayiyo podziwa kuti sanathe kuchoka wosadziwika, anabwera akunjenjemera ndipo anagwa pa mapazi a Yesu. Pamaso pa anthu onse, anafotokoza chifukwa chimene anamukhudzira Iye ndi mmene iye anachiritsidwira nthawi yomweyo. Kenaka anati kwa iye, "Mwana wamkazi, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere."
Ressurreições
Jesus ressuscitou mortos — a filha de Jairo, o filho da viúva de Naim e Lázaro. Ele é Senhor sobre a morte.
Za Mwana Wamkazi wa Yairo ndi Mayi Wokhudza Chovala cha Yesu
Pamene ankanena zimenezi, mkulu wa sunagoge anabwera namugwadira Iye nati, "Mwana wanga wamkazi wamwalira posachedwapa koma tiyeni mukasanjike dzanja lanu pa iye ndipo adzakhala ndi moyo." Yesu ndi ophunzira ake ananyamuka napita naye pamodzi.
Yesu atalowa mʼnyumba ya mkulu wa sunagoge ndi kuona oyimba zitoliro ndi gulu la anthu ochita phokoso, anati, "Tulukani, mtsikanayu sanafe koma ali mtulo." Koma anamuseka Iye. Atangowatulutsa anthuwo, analowa mʼnyumba ndipo anagwira dzanja la mtsikanayo ndipo anauka.
mmodzi wa akulu a mʼsunagoge, dzina lake Yairo anafika pamenepo. Ataona Yesu, anagwa pa mapazi ake, ndi kumudandaulira kwambiri nati, "Mwana wanga wamkazi wamngʼono ali pafupi kufa. Chonde tiyeni kuti mukamusanjike manja kuti akachiritsidwe nakhala ndi moyo." Ndipo Yesu anapita naye.
Gulu lalikulu la anthu linamutsata ndi kumamupanikiza Iye.
Atafika ku nyumba ya mkulu wa sunagoge, Yesu anaona chipiringu cha anthu akulira ndi kufuwula kwambiri. Analowa nati kwa iwo, "Mukuchita phokoso ndi kulira chifukwa chiyani? Mwanayu sanamwalire koma ali mtulo." Koma anamuseka Iye.
Atawatulutsa onse panja, Iye anatenga abambo ndi amayi ake a mwanayo ndi ophunzira omwe anali naye, ndipo analowa mʼmene munali mwanayo. Anagwira dzanja lake nanena kwa iye, "Talita Kumi!" (Kutanthauza kuti, "Mtsikana, ndikunena ndi iwe, imirira!") Nthawi yomweyo anayimirira nayenda mozungulira (anali wa zaka khumi ndi ziwiri). Pa ichi onse anadabwa kwambiri.
"Kodi ndingawafanizire chiyani anthu a mʼbado uno? Ali ngati chiyani? Ali ngati ana amene akukangana pa msika, ena akufunsa anzawo kuti,
" ‘Ife tinakuyimbirani chitoliro,
koma inu simunavine.
Tinakuyimbirani nyimbo zamaliro,
koma inu simunalire.’
Pakuti Yohane Mʼbatizi sanabwere kudzadya buledi kapena kumwa vinyo, koma inu mumati, ‘Ali ndi chiwanda.’ Mwana wa Munthu anabwera nadya ndi kumwa, ndipo inu mukuti, ‘Ali ndi dyera komanso ndi woledzera, bwenzi la amisonkho ndi ochimwa.’ Ndipo nzeru zimaoneka zolondola mwa ana ake onse."
Yesu Adzozedwa ndi Mayi Wochimwa
Tsopano mmodzi mwa Afarisi anayitana Yesu kuti akadye naye ku nyumba kwake ndipo anapita nakakhala pa tebulo. Mayi amene amakhala moyo wauchimo mu mzindawo atadziwa kuti Yesu akudya ku nyumba ya Mfarisiyo, anabweretsa botolo la mafuta onunkhira a alabasta.
Nthawi yomweyo munthu wotchedwa Yairo, woweruza wa mu sunagoge, anabwera ndi kugwa pa mapazi a Yesu, namupempha Iye kuti apite ku nyumba kwake, chifukwa mwana wake yekhayo wamkazi, kamtsikana ka zaka khumi ndi ziwiri, kanali pafupi kufa.
Pamene Yesu ankapita gulu la anthu linkamupanikiza.
Pamene Yesu ankayankhulabe, munthu wina anabwera kuchokera ku nyumba ya Yairo, woweruza wa ku sunagoge uja. Iye anati, "Mwana wanu wa mkazi wamwalira, musawavutitsenso Aphunzitsiwa."
Atamva zimenezi, Yesu anati kwa Yairo, "Usachite mantha, ingokhulupirira basi ndipo adzachiritsidwa."
Iye atafika ku nyumba ya Yairo, sanalole wina aliyense kulowa kupatula Petro, Yohane, ndi Yakobo ndi abambo ndi amayi a mwanayo. Pa nthawiyi nʼkuti anthu onse akubuma ndi kumulirira iye. Yesu anati, "Lekani kulira, sanafe koma wagona tulo."
Iwo anamuseka podziwa kuti anali atamwalira. Koma Iye anamugwira dzanja lake ndipo anati, "Mwana wanga, dzuka!" Mzimu wake unabwerera, ndipo nthawi yomweyo anayimirira. Kenaka Yesu anawawuza kuti amupatse chakudya. Makolo ake anadabwa, koma Iye anawalamulira kuti asawuze wina aliyense zimene zinachitikazo.
Imfa ndi Kuukitsidwa kwa Lazaro
Tsopano munthu wina dzina lake Lazaro anadwala. Iye anali wa ku Betaniya, mudzi wa Mariya ndi mchemwali wake Marita. Mariyayo ndi yemwe uja amene anadzoza Ambuye ndi mafuta onunkhira napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake. Lazaro wodwalayo anali mlongo wake. Choncho alongo ake anatumiza mawu kwa Yesu kuti, "Ambuye, uja amene Inu mumamukonda akudwala."
Atamva izi, Yesu anati, "Kudwalako safa nako. Koma akudwala kuti Mulungu alemekezedwe; ndi kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe chifukwa cha matendawo." Yesu anakonda Marita, mchemwali wake ndi Lazaro. Koma atamva kuti Lazaro akudwala, Iye anakhalabe kumene anali masiku ena awiri.
Kenaka anati kwa ophunzira ake, "Tiyeni tibwerere ku Yudeya."
Ophunzira akewo anati, "Rabi, posachedwa pomwepa Ayuda anafuna kukugendani ndi miyala, koma Inu mukupitanso komweko?"
Yesu anayankha kuti, "Kodi sipali maora khumi ndi awiri pa tsiku? Munthu amene amayenda masana sapunthwa, popeza akuona chifukwa cha kuwala kwa dziko lapansi. Koma amene akuyenda usiku amapunthwa, chifukwa kuwalako alibe."
Iye atatha kunena izi, anapitirira kuwawuza iwo kuti, "Bwenzi lathu Lazaro wagona tulo; koma Ine ndikupita kumeneko kukamudzutsa."
Ophunzira ake anayankha kuti, "Ambuye, ngati wagona adzapeza bwino." Yesu ankayankhula za imfa yake koma ophunzira ake ankaganiza kuti amanena za tulo chabe.
Ndipo kenaka anawawuza momveka kuti, "Lazaro wamwalira.
Domínio sobre a natureza
Jesus acalmou a tempestade, andou sobre as águas e multiplicou pães. A natureza obedece à voz do seu Criador.
Yesu Aletsa Namondwe
Iye atalowa mʼbwato, ophunzira ake anamutsatira. Ndipo taonani mwadzidzidzi mphepo yayikulu yamkuntho inawomba pa nyanjapo, kotero kuti bwatolo linayamba kumizidwa ndi mafunde. Koma Yesu anali mtulo. Ophunzira ake anapita namudzutsa nati, "Ambuye! Tipulumutseni! Tikumira!"
Iye anawayankha kuti, "Inu achikhulupiriro chochepa, chifukwa chiyani mukuchita mantha?" Ndipo anayimirira nadzudzula mphepoyo ndi mafunde ndipo panali bata lalikulu.
Ndipo ophunzirawo anadabwa nafunsa kuti, "Ndi munthu wotani uyu? Kuti ngakhale mphepo ndi mafunde zimvera Iye!"
Kutayamba mdima, ophunzira anabwera kwa Iye nati, "Kuno ndi kutchire ndipo kwayamba kale kuda. Awuzeni anthu azipita kuti afike ku midzi ndi kukadzigulira zakudya."
Yesu anawayankha kuti, "Sikofunika kuti azipita. Inuyo muwapatse kanthu kuti adye."
Iwo anayankha kuti, "Tili ndi malofu asanu okha a buledi ndi nsomba ziwiri."
Koma Iye anati, "Bweretsani kwa Ine." Analamula anthu kuti akhale pansi pa udzu ndipo anatenga buledi musanu ndi nsomba ziwiri nayangʼana kumwamba, nayamika nagawa bulediyo. Kenaka anapereka bulediyo kwa ophunzira ake ndipo ophunzirawo anagawira anthu. Onse anadya nakhuta ndipo ophunzira anatola zotsalira ndi kudzaza madengu khumi ndi awiri. Chiwerengero cha amene anadya kupatulako amayi ndi ana chinali pafupifupi amuna 5,000.
Pa ora lachinayi usiku, Yesu anabwera kwa iwo akuyendabe pa nyanja.
Yesu anayitana ophunzira ake nati, "Ndili ndi chifundo ndi anthu awa; akhala kale ndi Ine masiku atatu ndipo alibe chakudya. Ine sindifuna kuti apite kwawo ndi njala chifukwa angakomoke pa njira."
Ophunzira anayankha kuti, "Ndikuti kumene tingakapeze buledi mʼtchire muno okwanira kudyetsa gulu lotere?"
Yesu anawafunsa kuti, "Muli ndi malofu a buledi angati?"
Iwo anayankha kuti, "Asanu ndi awiri ndi tinsomba pangʼono."
Iye anawuza gululo kuti likhale pansi. Kenaka anatenga malofu asanu ndi awiri aja ndi tinsombato ndipo atayamika anagawa napatsa ophunzira ake ndipo iwo anagawira anthuwo. Onse anadya ndipo anakhuta. Pomaliza ophunzira anatolera zotsalira nadzaza madengu asanu ndi awiri. Chiwerengero cha anthu amene anadya chinali 4,000 kupatula amayi ndi ana.
Yesu Apereka Msonkho
Yesu ndi ophunzira ake atafika ku Kaperenawo, wolandira msonkho wa ku Nyumba ya Mulungu anabwera kwa Petro namufunsa kuti, "Kodi aphunzitsi anu sapereka msonkho wa Nyumba ya Mulungu?"
Iye anayankha kuti, "Inde amapereka."
Petro atalowa mʼnyumba, Yesu ndiye anayamba kuyankhula. Ndipo anamufunsa kuti, "Ukuganiza bwanji Simoni, kodi mafumu a dziko lapansi amalandira msonkho kuchokera kwa ana awo kapena kwa ena?"
Petro anayankha kuti, "Kuchokera kwa ena."
Yesu ananena kwa iye kuti, "Ndiye kuti ana sapereka." Koma kuti ife tisawakhumudwitse pita ku nyanja kaponye mbedza yako. Katenge nsomba imene ukayambe kuyikola; kayitsekule kukamwa ndipo ukapezamo ndalama. Katenge ndalamayo ndi kukapereka msonkho wanga ndi wanu.
Yesu Atemberera Mtengo wa Mkuyu
Mmamawa, pamene amabwera ku mzinda, anamva njala. Ataona mtengo wamkuyu mʼmbali mwa msewu, anapitapo koma sanapeze kanthu koma masamba okhaokha. Pamenepo anati kwa mtengowo, "Usadzabalenso chipatso!" Nthawi yomweyo mtengowo unafota.
Ophunzira ataona zimenezi, anadabwa nafunsa kuti, "Kodi mtengo wamkuyuwu wauma msanga bwanji?"
Yesu anayankha kuti, "Zoonadi, ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro ndipo simukayika, simudzangochita zokha zachitika kwa mkuyuzi, koma mudzatha kuwuza phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye wekha mʼnyanja,’ ndipo zidzachitikadi. Ngati mukhulupirira, mudzalandira chilichonse chimene muchipempha mʼpemphero."
Mphepo yamkuntho inabuka, ndipo mafunde anawomba bwatolo, kotero kuti linali pafupi kumira. Pa nthawi imeneyi Yesu anali akugona atatsamira pilo kumbuyo kwa bwato. Ophunzira anamudzutsa nati kwa Iye, "Aphunzitsi, kodi simukusamala kuti timira?"
Yesu anauka nadzudzula mphepo nati kwa mafunde, "Chete! Khala bata!" Pamenepo mphepo inaleka ndipo kunachita bata.
Iye anati kwa ophunzira ake, "Muli ndi mantha chifukwa chiyani? Kodi mukanalibe chikhulupiriro?"
Iwo anachita mantha nafunsana wina ndi mnzake kuti, "Uyu ndani? Ngakhale mphepo ndi nyanja zimumvera Iye!"
Pa nthawi iyi nʼkuti dzuwa litapendeka, ndipo ophunzira ake anabwera kwa Iye nati, "Kuno ndi kuthengo, ndipo ano ndi madzulo. Awuzeni anthuwa azipita ku midzi ndi madera ozungulira, kuti akadzigulire kanthu kakuti adye."
Koma Iye anayankha kuti, "Apatseni kanthu koti adye."
Iwo anati kwa Iye, "Apa pafunika ndalama za miyezi isanu ndi itatu zomwe munthu amalandira! Kodi tipite kukagwiritsa ntchito ndalama zotere kugulira buledi kuti tiwapatse adye?"
Iye anawafunsa kuti, "Muli ndi malofu a buledi angati? Pitani mukaone."
Ataona anati kwa Iye, "Asanu ndi nsomba ziwiri."
Pamenepo Yesu anawalamulira kuti awakhazike anthu pansi mʼmagulu pa msipu obiriwira. Ndipo anakhala pansi mʼmagulu a anthu 100 ndi gulu la anthu makumi asanu. Atatenga malofu a buledi asanu ndi nsomba ziwiri, nayangʼana kumwamba, Iye anayamika nagawa malofu a bulediwo. Kenaka anawapatsa ophunzira ake kuti awapatse anthu. Ndipo anagawanso nsomba ziwirizo kwa onse. Onse anadya ndipo anakhuta, ndipo ophunzira ake anatola buledi ndi nsomba zotsalira zokwanira madengu khumi ndi awiri. Chiwerengero cha amuna amene anadya chinali 5,000.
Iye anaona ophunzira ake akuvutika popalasa bwato, chifukwa mphepo imawomba mokumana nawo. Pa nthawi ya mʼbandakucha Iye anafika kwa iwo akuyenda pa nyanja. Anali pafupi kuwapitirira, koma atamuona Iye akuyenda pa nyanja, anaganiza kuti anali mzukwa. Iwo anafuwula, pakuti onse anamuona ndipo anachita mantha.
Nthawi yomweyo Iye anawayankhula nati, "Limbani mtima! Ndine. Musachite mantha." Ndipo Iye anakwera mʼbwato pamodzi nawo, ndipo mphepo inaleka. Iwo anadabwa kwambiri,
Yesu Adyetsa Anthu 4,000
Mʼmasiku amenewo gulu lina lalikulu la anthu linasonkhana. Popeza iwo analibe chakudya, Yesu anayitana ophunzira ake nati kwa iwo, "Ndili ndi chifundo ndi anthu awa; akhala ali ndi Ine masiku atatuwa ndipo alibe chakudya. Ngati nditawawuza kuti apite kwawo ali ndi njala, iwo adzakomoka mʼnjira chifukwa ena a iwo achokera kutali."
Ophunzira ake anayankha nati, "Kodi ndi kuti kuthengo kuno kumene munthu angapeze buledi okwanira kuwadyetsa?"
Yesu anafunsa kuti, "Muli ndi malofu a buledi angati?"
Iwo anayankha kuti, "Asanu ndi awiri."
Iye anawuza gulu la anthu kuti likhale pansi. Atatenga malofu a buledi asanu ndi awiri, anayamika, nawanyema ndipo anapatsa ophunzira ake kuti agawire anthu, ndipo iwo anatero. Analinso ndi tinsomba tochepa; Iye anayamikanso chifukwa cha nsombazo. Ndipo anawuza ophunzira kuti awagawire. Anthu anadya ndipo anakhuta. Atamaliza, ophunzira anatola buledi ndi nsomba zotsalira ndi kudzaza madengu asanu ndi awiri. Panali amuna pafupifupi 4,000. Ndipo atawawuza kuti apite kwawo,
Yesu Atemberera Mkuyu
Mmawa mwake pamene amachoka ku Betaniya, Yesu anamva njala. Ataonera patali mtengo wamkuyu uli ndi masamba, anapita kuti akaone ngati unali ndi chipatso chilichonse. Atafika, sanapezemo kanthu koma masamba, chifukwa sinali nthawi ya nkhuyu. Ndipo Iye anati kwa mtengo, "Palibe amene adzadyenso chipatso kuchokera kwa iwe." Ndipo ophunzira ake anamva Iye akunena izi.
Mkuyu Wofota
Mmamawa, pamene ankayenda, anaona mtengo wamkuyu uja utafota kuyambira ku mizu. Petro anakumbukira nati kwa Yesu, "Aphunzitsi, taonani! Mtengo wamkuyu munawutemberera uja wafota!"
Yesu anayankha kuti, "Khalani ndi chikhulupiriro mwa Mulungu. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati wina aliyense angalamule phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye mʼnyanja,’ ndipo wosakayika mu mtima mwake koma kukhulupirira kuti chimene akunena chidzachitika, chidzachitikadi kwa iyeyo. Nʼchifukwa chake ndikukuwuzani kuti chilichonse chimene mupempha mʼpemphero, khulupirirani kuti mwalandira, ndipo chidzakhala chanu. Pamene muyimirira kupemphera, ngati muli ndi chifukwa ndi wina, mukhululukireni, kuti Atate anu akumwamba akukhululukireni machimo anu."
Yesu Ayitana Ophunzira Oyamba
Tsiku lina Yesu anayima mʼmbali mwa nyanja ya Genesareti, gulu la anthu litamuzungulira likumvetsera mawu a Mulungu. Iye anaona mabwato awiri ali mʼmphepete mwa nyanja, asodzi amene ankachapa makhoka awo atawasiya pamenepo. Iye analowa mʼbwato limodzi limene linali la Simoni, ndi kumupempha kuti alikankhire mʼkati mwa nyanja pangʼono. Kenaka Iye anakhala pansi nayamba kuphunzitsa anthu ali mʼbwatomo.
Atatha kuyankhula anati kwa Simoni, "Kankhirani kwa kuya ndipo muponye makhoka kuti mugwire nsomba."
Simoni anayankha kuti, "Ambuye, tagwira ntchito molimbika usiku wonse, koma sitinagwire kanthu. Koma pakuti mwatero, ndiponya makhoka."
Atachita izi, anagwira nsomba zambiri kotero kuti makhoka awo anayamba kungʼambika. Choncho anakodola anzawo a bwato linalo kuti abwere ndi kuwathandiza, ndipo anabwera nadzaza mabwato onse awiri mpaka kuyamba kumira.
Simoni Petro ataona izi, anagwa pa mawondo a Yesu nati, "Chokani kwa ine Ambuye: Ine ndine munthu wochimwa!" Iye ndi anzake onse anadabwa ndi nsomba zimene anagwira, chimodzimodzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, anzake a Simoniyo.
Kenaka Yesu anati kwa Simoni, "Musachite mantha; kuyambira tsopano ndidzakusandutsani asodzi a anthu." Kenaka anakokera mabwato awo ku mtunda, nasiya zonse namutsata Iye.
Yesu Aletsa Namondwe
Tsiku lina Yesu anati kwa ophunzira ake, "Tiyeni tiwolokere tsidya lina la nyanja." Ndipo analowa mʼbwato nanyamuka. Akuwoloka, Iye anagona tulo. Namondwe wamkulu anayamba pa nyanja, ndipo bwatolo linayamba kudzaza ndi madzi ndipo anali pa chiopsezo chachikulu.
Ophunzira anapita ndi kukamudzutsa Iye, nati, "Ambuye, Ambuye, ife tikumira!"
Anadzuka ndipo anadzudzula mphepo ndi madzi owindukawo. Namondwe anasiya, ndipo panali bata. Iye anafunsa ophunzira ake kuti, "Chikhulupiriro chanu chili kuti?"
Koma pogwidwa ndi mantha ndi kudabwa anafunsana wina ndi mnzake kuti, "Uyu ndi ndani? Iye alamulira ngakhale mphepo ndi madzi, ndipo zimumvera Iye."
Yesu Aletsa Namondwe
Tsiku lina Yesu anati kwa ophunzira ake, "Tiyeni tiwolokere tsidya lina la nyanja." Ndipo analowa mʼbwato nanyamuka. Akuwoloka, Iye anagona tulo. Namondwe wamkulu anayamba pa nyanja, ndipo bwatolo linayamba kudzaza ndi madzi ndipo anali pa chiopsezo chachikulu.
Ophunzira anapita ndi kukamudzutsa Iye, nati, "Ambuye, Ambuye, ife tikumira!"
Anadzuka ndipo anadzudzula mphepo ndi madzi owindukawo. Namondwe anasiya, ndipo panali bata. Iye anafunsa ophunzira ake kuti, "Chikhulupiriro chanu chili kuti?"
Koma pogwidwa ndi mantha ndi kudabwa anafunsana wina ndi mnzake kuti, "Uyu ndi ndani? Iye alamulira ngakhale mphepo ndi madzi, ndipo zimumvera Iye."
Achiritsidwa Munthu Wogwidwa ndi Ziwanda
Iwo anawolokera ku chigawo cha Gerasa chimene chili tsidya lina la nyanja kuchokera ku Galileya.
Chakumadzulo dzuwa litapita, khumi ndi awiriwo anabwera kwa Iye ndipo anati, "Uzani gulu la anthuli lichoke kuti apite ku midzi yotizungulira ndi madera a ku mudzi kuti akapeze chakudya ndi pogona, chifukwa kuno ndi kuthengo."
Iye anayankha kuti, "Apatseni chakudya kuti adye."
Iwo anayankha kuti, "Ife tili ndi malofu a buledi asanu okha ndi nsomba ziwiri, pokhapokha titapita kukagula chakudya cha gulu la anthu onsewa." (Pamenepo panali amuna pafupifupi 5,000).
Koma Iye anati kwa ophunzira ake, "Akhazikeni pansi mʼmagulu a anthu pafupifupi makumi asanu." Ophunzira ake anachita zomwezo ndipo aliyense anakhala pansi. Atatenga malofu a buledi asanu ndi nsomba ziwiri zija anayangʼana kumwamba, nayamika ndipo anazigawa. Kenaka anazipereka kwa ophunzira ake kuti azipereke kwa anthu. Onse anadya nakhuta, ndipo ophunzira ake anatolera madengu khumi ndi awiri odzaza ndi nyenyeswa zomwe zinatsala.
Yesu Asandutsa Madzi Kukhala Vinyo
Pa tsiku lachitatu munali ukwati mu Kana wa ku Galileya. Amayi ake a Yesu anali komweko, ndipo Yesu ndi ophunzira ake anayitanidwanso ku ukwatiwo. Vinyo atatha, amayi a Yesu anati kwa Iye, "Wawathera vinyo."
Yesu anayankha kuti, "Amayi, chifukwa chiyani mukundiwuza Ine? Nthawi yanga sinakwane."
Amayi ake anati kwa antchito, "Inu muchite chilichonse chimene akuwuzeni."
Pamenepo panali mitsuko yamiyala yothiramo madzi isanu ndi umodzi, imene Ayuda amagwiritsa ntchito pa mwambo wodziyeretsa. Uliwonse unali ndi malita 100 kapena kupitirirapo.
Yesu anati kwa antchitowo, "Dzazani madzi mʼmitsukoyi," ndipo iwo anadzaza ndendende.
Ndipo Iye anatinso kwa iwo, "Tsopano tungani ndipo kaperekeni kwa mkulu waphwando."
Iwo anachita momwemo. Mkulu waphwando analawa madziwo amene anasandulika vinyo, ndipo sanazindikire kumene vinyoyo anachokera, ngakhale kuti antchito amene anatunga madziwo amadziwa. Kenaka anayitanira mkwati pambali ndipo anati, "Aliyense amatulutsa vinyo wokoma kwambiri poyambirira ndipo kenaka vinyo wosakoma pamene oyitanidwa atamwa kale wambiri; koma iwe wasunga wokoma mpaka tsopano."
Ichi chinali chizindikiro chodabwitsa choyamba chimene Yesu anachita ku Kana wa ku Galileya. Potero Iye anawulula ulemerero wake, ndipo ophunzira ake anamukhulupirira Iye.
Iye anafunsa izi kumuyesa chabe, pakuti Iye ankadziwa chimene ankayenera kuchita.
Filipo anamuyankha Iye kuti, "Malipiro a miyezi isanu ndi itatu sangathe kugula buledi okwanira aliyense kuti adye!"
Mmodzi wa ophunzira ake, Andreya, mʼbale wa Simoni Petro, anati, "Pano pali mnyamata amene ali ndi buledi musanu wabarele ndi tinsomba tiwiri, kodi zingakwane onsewa?"
Yesu anati, "Awuzeni anthuwa akhale pansi." Pamalo pamenepa panali udzu wambiri ndipo amuna amene anakhala pansi anali osachepera 5,000. Kenaka Yesu anatenga bulediyo, atayamika anagawira iwo amene anakhala pansi, chimodzimodzinso nsombazo monga momwe iwo anafunira.
Ndipo atakhuta, Iye anati kwa ophunzira ake, "Tolani zotsala kuti pasawonongeke kanthu." Choncho iwo anasonkhanitsa makombo nadzaza madengu khumi ndi awiri.
Iwo atayenda makilomita asanu kapena asanu ndi limodzi, anaona Yesu akuyandikira bwatolo, akuyenda pa madzi; ndipo anachita mantha. Koma Iye anawawuza kuti, "Ndine, musaope." Ndipo iwo analola kumutenga mʼbwatomo, nthawi yomweyo bwatolo linafika ku gombe la nyanja kumene ankapita.
Yesu Aonekera kwa Ophunzira ku Nyanja ya Tiberiya
Zitatha izi Yesu anaonekeranso kwa ophunzira ake, mʼmbali mwa nyanja ya Tiberiya. Anadzionetsera motere: Simoni Petro, Tomasi (otchedwa Didimo), Natanieli wochokera ku Kana wa ku Galileya, ana a Zebedayo, ndi ophunzira ena awiri anali limodzi. Simoni Petro anawawuza iwo kuti, "Ine ndikupita kukasodza," ndipo iwo anati, "ife tipita nawe." Choncho anapita ndi kulowa mʼbwato, koma usiku umenewo sanagwire kanthu.
Mmamawa, Yesu anayimirira mʼmbali mwa nyanja, koma ophunzira ake sanazindikire kuti anali Yesu.
Yesu anawafunsa iwo kuti, "Anzanga, kodi muli nsomba?"
Iwo anayankha kuti, "Ayi."
Iye anati, "Ponyani khoka lanu kudzanja lamanja la bwato lanu ndipo mupha kanthu." Atatero, iwo analephera kukoka ukonde chifukwa chakuchuluka kwa nsomba.
Kenaka ophunzira amene Yesu amamukonda anati kwa Petro, "Ndi Ambuye!" Petro atangomva iye akunena kuti ndi Ambuye, iye anavala chovala chake (pakuti anali atavula) ndipo analumphira mʼnyanja. Ophunzira enawo analowa mʼbwato akukoka ukonde odzaza ndi nsomba, popeza iwo sanali kutali kuchokera ku mtunda, pafupifupi mamita makumi asanu ndi anayi. Atafika pa mtunda, iwo anaona moto wamakala pamenepo ndi nsomba, ndi buledi.
Yesu anawawuza kuti, "Tabweretsa nsomba zina mwagwirazo."
Simoni Petro anakwera mʼbwato ndi kukokera khoka ku gombe, lodzaza ndi nsomba zikuluzikulu 153, komabe ndi nsomba zochuluka chotero khoka silinangʼambike.
Libertações
Jesus expulsou demônios com autoridade. Os espíritos impuros não resistiam à sua palavra e saíam imediatamente.
Chikhulupiriro cha Kenturiyo
Yesu atalowa mʼKaperenamu, Kenturiyo anabwera kwa Iye napempha chithandizo, nati, "Ambuye, wantchito wanga ali chigonere ku nyumba, sakuthanso kuyenda, akumva kuwawa kwambiri."
Ndipo Yesu anati kwa iye, "Ine ndibwera kudzamuchiritsa."
Kenturiyo uja anayankha kuti, "Ambuye, ndine wosayenera kuti Inu mukalowe mʼnyumba mwanga. Koma mungonena mawu ndipo wantchito wanga adzachiritsidwa. Pakuti inenso ndili pansi pa ulamuliro ndipo ndili ndi asilikali amene ndiwalamulira. Ndikalamulira mmodzi kuti, ‘Pita,’ amapita; ndi kwa wina kuti, ‘Bwera,’ amabwera. Ndikawuza wantchito wanga kuti, ‘Chita ichi,’ iye amachita."
Yesu atamva zimenezi, anadabwa ndipo anati kwa omutsatira, "Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti sindinapeze wina aliyense mu Israeli wachikhulupiriro chachikulu chotere. Ndikuwuzani kuti ambiri adzabwera kuchokera kummawa ndi kumadzulo, nadzakhala nawo pa phwando pamodzi ndi Abrahamu, Isake ndi Yakobo mu ufumu wakumwamba. Koma eni ake ufumuwo adzaponyedwa ku mdima wakunja kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano."
Pamenepo Yesu anati kwa Kenturiyo, "Pita! Zichitike monga momwe wakhulupirira." Ndipo wantchito wake anachira pa nthawi yomweyo.
Ogwidwa ndi Ziwanda a ku Gadara
Ndipo atafika ku mbali ina ya dera la Gadara, anakumana ndi anthu awiri ogwidwa ndi ziwanda akuchokera ku manda. Iwowa anali woopsa kwambiri kotero kuti panalibe munthu akanatha kudzera njira imeneyo. Ndipo iwo anafuwulira kwa Yesu nati, "Mukufuna chiyani kwa ife, Inu Mwana wa Mulungu? Kodi mwabwera kuno kudzatizunza nthawi yake isanafike?"
Ndipo patali pake panali gulu la nkhumba zimene zimadya. Ndipo ziwandazo zinamupempha Yesu kuti, "Ngati mutitulutsa ife mutitumize mu nkhumba izo."
Iye anati kwa ziwandazo, "Pitani!" Ndipo pamenepo zinatuluka ndi kukalowa mʼnkhumbazo ndipo nkhumba zonse zinathamangira mʼnyanja ndi kufera momwemo. Koma amene amaziweta anathawa nalowa mʼmudzi nafotokoza zonse, kuphatikizapo zimene zinachitika ndi anthu ogwidwa ndi ziwanda aja. Ndipo anthu onse a mʼmudziwo anatuluka kukakumana ndi Yesu. Ndipo atamuona Iye, anamupempha kuti achoke mʼdera lawo.
Pamene iwo ankatuluka kunja, anthu anabwera kwa Iye ndi munthu wogwidwa ndi mzimu wosayankhula. Ndipo atatulutsa mzimuwo, munthuyo anayankhula. Gulu la anthuwo linadabwa ndipo linati, "Zinthu zotere sizinaonekepo mu Israeli."
Mwano wa Afarisi
Pomwepo anthu anabwera naye kwa Yesu munthu wogwidwa ndi chiwanda amene anali wosaona ndi wosamva ndipo Yesu anamuchiritsa kotero kuti atatha anayamba kumva ndi kuona.
Mayi wa ku Kanaani
Yesu atachoka kumalo amenewo anapita kudera la ku Turo ndi ku Sidoni. Mayi wa Chikanaani wochokera dera la komweko anabwera kwa Iye akulira, nati, "Ambuye, Mwana wa Davide, ndichitireni chifundo! Mwana wanga wamkazi akuzunzika kwambiri ndi chiwanda."
Yesu sanayankhe kanthu. Ndipo ophunzira ake anabwera namupempha Iye kuti, "Muwuzeni achoke chifukwa akulira mofuwula pambuyo pathu."
Iye anayankha kuti, "Ine ndinatumidwa kwa nkhosa zotayika za Israeli zokha."
Mayiyo anabwera ndi kugwada pamaso pake, nati, "Ambuye ndithandizeni!"
Iye anayankha kuti, "Sibwino kutenga chakudya cha ana ndi kuponyera agalu."
Mayiyo anati, "Inde Ambuye. Komatu ngakhale agalu amadya nyenyeswa zimene zimagwa kuchokera pa tebulo la mbuye wawo."
Pomwepo Yesu anayankha kuti, "Mayi iwe uli ndi chikhulupiriro chachikulu! Pempho lako lamveka." Ndipo mwana wake wamkazi anachira nthawi yomweyo.
Yesu Achiritsa Wodwala Matenda Akugwa
Atafika ku gulu la anthu, munthu wina anamuyandikira Yesu ndi kugwada pamaso pake. Iye anati, "Ambuye, muchitireni chifundo mwana wanga akudwala matenda akugwa ndipo akuvutika kwambiri. Kawirikawiri iye amagwa pa moto kapena mʼmadzi. Ine ndinabwera naye kwa ophunzira anu koma alephera kumuchiritsa."
Yesu anayankha nati, "Haa, mʼbado wosakhulupirira ndi wokhota maganizo! Kodi ndidzakhala nanu mpaka liti? Ndidzapirira nanu mpaka liti? Bwera nayeni kwa Ine mnyamatayo." Yesu anadzudzula chiwandacho ndipo chinatuluka mwa mnyamatayo ndipo anachira nthawi yomweyo.
Pomwepo munthu wina mʼsunagogemo amene anali wogwidwa ndi mzimu woyipa anafuwula kuti, "Mukufuna chiyani kwa ife, Yesu wa ku Nazareti? Kodi mwabwera kudzatiwononga? Ndikudziwa kuti ndinu ndani, ndinu Woyerayo wa Mulungu!"
Yesu anadzudzula chiwandacho mwamphamvu nati, "Khala chete! Tuluka mwa iye!" Mzimu woyipawo unamugwedeza mwamphamvu ndipo unatuluka mwa iye ukufuwula.
Yesu Achiritsa Wogwidwa ndi Ziwanda
Ndipo anawoloka nyanja napita ku dera la Gerasa. Yesu atatuluka mʼbwato, munthu amene anali ndi mzimu woyipa anachoka ku manda ndi kukumana naye. Munthuyu amakhala ku manda, ndipo panalibe amene akanatha kumumanganso ngakhale ndi unyolo. Pakuti nthawi zambiri akamumanga manja ndi miyendo amadula maunyolo ndi kudula zitsulo zimene zinali mʼmapazi ake. Panalibe amene anali ndi mphamvu yoti ndi kumugonjetsa. Usana ndi usiku ankakhala ku manda ndi kumapiri, akulira ndi kudzicheka ndi miyala.
Ataona Yesu ali patali, anathamanga nagwa pa mawondo ake pamaso pake. Iye anafuwula kwambiri nati, "Mukufuna muchite nane chiyani, Yesu Mwana wa Mulungu Wammwambamwamba? Lumbirani kwa Mulungu kuti simundizunza!" Pakuti Yesu anati kwa iye, "Tuluka mwa munthuyu, iwe mzimu woyipa!"
Ndipo Yesu anamufunsa iye, "Dzina lako ndani?"
Iye anayankha kuti, "Dzina langa ndine Legiyo, pakuti tilipo ambiri." Ndipo anamupempha Yesu mobwerezabwereza kuti asazitulutse mʼderalo.
Gulu lalikulu la nkhumba limadya mʼmbali mwa phiri limene linali pafupi. Ziwandazo zinapempha Yesu kuti, "Titumizeni pakati pa nkhumbazo; ndipo mutilole tilowe mwa izo." Iye anazipatsa chilolezo, ndipo mizimu yoyipayo inatuluka ndi kukalowa mu nkhumbazo. Gulu la nkhumba, zokwana pafupifupi 2,000 zinathamanga kutsetserekera ku nyanja ndipo zinamira.
Omwe amaweta nkhumbazo anathawa ndi kukawuza anthu za izi mu mzinda ndi ku madera a ku midzi, ndipo anthu anapita kukaona zomwe zinachitika.
Koma inu mumati, ngati munthu anena kwa abambo ake kapena amayi ake kuti, ‘Thandizo lililonse mukanayenera kulandira kuchokera kwa ine ndi Korobani’ (kutanthauza kuti, mphatso yoperekedwa kwa Mulungu), pamenepo inu simumalola kuti achitire kanthu kalikonse abambo kapena amayi ake. Potero mumachepetsa mawu a Mulungu kukhala wopanda mphamvu ndi miyambo yanu imene mumapatsirana. Ndipo mumachita zinthu zina zambiri monga zimenezi."
Yesu anayitananso gulu la anthu ndipo anati, "Tandimverani nonsenu, ndipo zindikirani izi. Palibe kanthu kunja kwa munthu kamene kakalowa mwa iye kangamusandutse wodetsedwa. Koma zimene zituluka mwa munthu ndizo zimupanga kukhala wodetsedwa."
Chikhulupiriro cha Mayi wa ku Siriya Fonisia
Yesu anachoka kumalo amenewo napita ku madera a Turo. Iye analowa mʼnyumba ndipo sanafune wina kuti adziwe zimenezi; komabe sanathe kudzibisa. Kunena zoona, amayi amene kamwana kawo kakakazi kanali kogwidwa ndi mzimu woyipa, atangomva za Iye, anabwera nagwada pa mapazi ake. Mayiyu anali Mhelene, wobadwira ku Fonisia wa ku Siriya. Anamupempha Yesu kuti atulutse chiwanda mwa mwana wake.
Iye anamuwuza kuti, "Choyamba asiye ana adye zimene akuzifuna, pakuti si kwabwino kutenga buledi wa ana ndi kuponyera agalu awo."
Mayiyo anayankha kuti, "Inde Ambuye, koma ngakhale agalu amadya zomwe zimagwa pansi kuchokera pa tebulo la ana."
Ndipo Iye anamuwuza kuti, "Chifukwa cha yankholi, ukhoza kupita; chiwanda chachoka mwa mwana wako wamkazi."
Atapita kwawo anakapeza mwana wake aligone pa bedi, chiwanda chitatuluka.
Munthu wina mʼgululo anayankha kuti, "Aphunzitsi, ndinakubweretserani mwana wanga wamwamuna, amene ndi ogwidwa ndi mzimu umene umamulepheretsa kuyankhula. Nthawi iliyonse ukamugwira umamugwetsa pansi. Amatuluka thovu kukamwa, amakukuta mano ake ndipo amawuma. Ndinapempha ophunzira anu kuti awutulutse mzimuwo, koma sanathe."
Yesu anayankha kuti, "Haa! Mʼbado osakhulupirira, kodi ndidzakhala nanu mpaka liti? Mubweretseni kwa Ine mnyamatayo."
Ndipo anamubweretsa kwa Iye. Mzimu woyipawo utaona Yesu, nthawi yomweyo unamukomola mnyamatayo. Anagwa pansi ndi kumagubuduka, ndi kuchita thovu kukamwa.
Yesu anafunsa abambo a mnyamatayo kuti, "Kodi wakhala chotere nthawi yayitali bwanji?"
Iye anayankha kuti, "Kuyambira ali wamngʼono, wakhala ukumuponya pa moto kapena mʼmadzi kuti umuphe. Koma ngati mungathe kuchita kanthu, tichitireni chifundo ndipo mutithandize."
Yesu anati, " ‘Ngati mungathe!’ Zinthu zonse ndi zotheka kwa iye amene akhulupirira."
Nthawi yomweyo abambo a mwanayo anafuwula kuti, "Ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga!"
Yesu ataona kuti gulu la anthu likuthamangira kumalowo, anadzudzula mzimu woyipawo kuti, "Iwe mzimu wolepheretsa kuyankhula ndi kumva, ndikulamulira tuluka mwa iye ndipo usadzalowenso."
Mzimuwo unafuwula ndi kumugubuduza kwambiri ndipo unatuluka. Mnyamatayo anaoneka ngati mtembo ndipo ambiri anati, "Wafa." Koma Yesu anamugwira dzanja ndipo anamuyimiritsa, ndipo anayimirira.
Yesu Achiritsa Anthu Ambiri
Yesu anatuluka mʼsunagoge ndipo anapita kwa Simoni. Tsopano mpongozi wake wa Simoni amadwala malungo akulu, ndipo anamupempha Yesu kuti amuthandize. Ndipo anawerama nadzudzula malungowo ndipo anamusiya. Anadzuka nthawi yomweyo nayamba kuwatumikira.
Yesu ataponda pa mtunda, anakumana ndi munthu wogwidwa ndi ziwanda wochokera mu mzindawo. Kwa nthawi yayitali munthuyu sanavale zovala kapena kukhala mʼnyumba, koma amakhala ku manda. Iye ataona Yesu, anakuwa nagwa pa mapazi ake akufuwula kwambiri kuti, "Mukufuna chiyani ndi ine, Yesu Mwana wa Mulungu Wammwambamwamba? Ndikupemphani Inu, musandizunze ine!" Pakuti Yesu analamula mzimu woyipawo kuti utuluke mwa munthuyo. Kawirikawiri umamugwira iye, ndipo ngakhale anali womangidwa ndi unyolo dzanja ndi mwendo ndi kuti ankamuyangʼanira, koma amadula maunyolo akewo ndipo ziwanda zimamutengera kumalo a yekha.
Yesu anamufunsa kuti, "Dzina lako ndani?"
Iye anayankha kuti, "Legiyo," chifukwa ziwanda zambiri zinalowa mwa iye. Ndipo ziwandazo zimamupempha mobwerezabwereza kuti asazitumize ku dzenje la mdima.
Gulu lalikulu la nkhumba limadya pamenepo mʼmbali mwa phiri. Ziwandazo zinamupempha Yesu kuti azilole kuti zikalowe mu nkhumbazo ndipo Iye anazilola. Ziwanda zija zitatuluka mwa munthuyo, zinakalowa mwa nkhumbazo, ndipo gulu lonselo linathamangira ku mtsetse ndi kukalowa mʼnyanja ndi kumira.
Oweta nkhumbazo ataona zimene zinachitikazo, anathamanga ndi kukanena izi mu mzinda ndi ku madera a ku midzi. Ndipo anthu anapita kukaona zimene zinachitika. Atafika kwa Yesu, anapeza munthu amene anatulutsidwa ziwanda uja atakhala pa mapazi a Yesu, atavala ndipo ali ndi nzeru zake; ndipo iwo anachita mantha.
Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti ena mwa inu amene mwayima pano simudzalawa imfa musanaone ufumu wa Mulungu."
Maonekedwe a Ulemerero wa Yesu pa Phiri
Patatha pafupifupi masiku asanu ndi atatu Yesu atanena izi, Iye anatenga Petro, Yohane ndi Yakobo ndi kukwera ku phiri kukapemphera. Pamene Iye ankapemphera, maonekedwe a nkhope yake, ndi zovala zake zinawala monyezimira kwambiri. Anthu awiri, Mose ndi Eliya, anaonekera mu ulemerero opambana akuyankhulana ndi Yesu. Iwo amayankhulana za kuchoka kwake, kumene Iye anali pafupi kukakwaniritsa ku Yerusalemu.
Petro ndi anzake anali ndi tulo tambiri, koma atadzuka, iwo anaona ulemerero wake ndi anthu awiri atayima pamodzi ndi Iye. Pamene anthuwo ankamusiya Yesu, Petro anati kwa Iye, "Ambuye, ndi chabwino kwa ife kuti tikhale pano. Tiloleni kuti timange misasa itatu, umodzi wanu, umodzi wa Mose ndi umodzi wa Eliya." (Iye sanadziwe chimene amayankhula).
Munthu wina mʼgulu la anthulo anayitana kuti, "Aphunzitsi, ndikupemphani kuti muone mwana wangayu, pakuti ndi mmodzi yekhayu. Chiwanda chikamugwira amafuwula mwadzidzidzi; chimamugwedeza kolimba mpaka kutuluka thovu kukamwa. Sichimusiya ndipo chikumuwononga. Ine ndinapempha ophunzira anu kuti achitulutse, koma alephera."
Yesu anayankha kuti, "Haa! Anthu osakhulupirira ndi mʼbado wokhota. Kodi Ine ndidzakhala nanu nthawi yayitali yotani ndi kukupirirani? Bweretsa mwana wako kuno."
Ngakhale pamene mnyamata amabwera kwa Yesu, chiwandacho chinamugwetsa pansi ndi kumugwedeza. Koma Yesu anadzudzula mzimu woyipawo nachiritsa mwa mnyamatayo ndi kumuperekanso kwa abambo ake. Ndipo iwo onse anadabwa ndi ukulu wa Mulungu.
Yesu Abwereza Kunena za Imfa yake
Aliyense akudabwa ndi zimene Yesu anachita, Iyeyo anati kwa ophunzira ake,
Yesu ndi Belezebabu
Yesu amatulutsa chiwanda chimene chinali chosayankhula. Chiwandacho chitatuluka, munthu wosayankhulayo anayankhula, ndipo gulu la anthu linadabwa.
Ndipo mmodzi wa iwo anatema wantchito wamkulu wa ansembe, nadula khutu lake lamanja.
Koma Yesu anayankha kuti, "Zisachitikenso zimenezi!" Ndipo Iye anakhudza khutu la munthuyo ndi kumuchiritsa.
Anthu otumidwa ndi Yohane aja atachoka, Yesu anayamba kuyankhula ndi gulu la anthu za Yohaneyo kuti, "Kodi munkapita ku chipululu kukaona chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo? Ngati si choncho, munkapita kukaona chiyani? Munthu wovala zovala zabwino? Ayi, ovala zovala zodula ndi okhala moyo wapamwamba ali mʼnyumba zaufumu. Koma inu munkapita kukaona chiyani? Mneneri? Inde, Ine ndikukuwuzani, woposa mneneri. Uyu ndi amene malemba akunena za Iye kuti,
" ‘Ine ndidzatuma mthenga wanga patsogolo panu,
amene adzakonza njira yanu.’
Ine ndikukuwuzani kuti pakati pa obadwa kuchokera mwa mkazi palibe wina wamkulu kuposa Yohane; komabe amene ali wamngʼono mu ufumu wa Mulungu ndi wamkulu kuposa iye."
Anthu onse, ngakhale amisonkho, atamva mawu a Yesu, anavomereza kuti njira ya Mulungu ndi yolondola, chifukwa anabatizidwa ndi Yohane. Koma Afarisi ndi akatswiri amalamulo anakana cholinga cha Mulungu kwa iwo okha, chifukwa sanabatizidwe ndi Yohane.