Morte de Jesus
A morte de Jesus é o sacrifício supremo do amor de Deus. Na cruz, o Cordeiro de Deus carregou os pecados do mundo, satisfez a justiça divina e abriu o caminho da salvação para todos.
O sacrifício na cruz
Jesus disse: 'Está consumado!' Na cruz, Ele cumpriu toda a lei, pagou o preço do pecado e reconciliou a humanidade com Deus.
Atadziwa kuti zonse zatha tsopano komanso kuti malemba akwaniritsidwe, Yesu anati, "Ine ndili ndi ludzu." Pomwepo panali mtsuko wodzaza ndi vinyo wosasa, choncho iwo ananyika chinkhupule ndi kuchisomeka ku mtengo wa hisope nachifikitsa kukamwa kwa Yesu. Yesu atalandira chakumwachi anati, "Kwatha." Ndipo Iye anaweramitsa mutu wake napereka mzimu wake.
Asilikali atamupachika Yesu, anatenga zovala zake ndi kuzigawa zigawo zinayi, gawo limodzi la aliyense wa iwo, ndi kutsala mwinjiro wamʼkati wokha. Chovala ichi chinawombedwa kuyambira pamwamba mpaka pansi wopanda msoko.
Iwo anati kwa wina ndi mnzake, "Tiyeni tisachingʼambe koma tichite maere kuti tione amene achitenge."
Izi zinachitika kuti malemba akwaniritsidwe amene anati,
"Iwo anagawana zovala zanga pakati pawo
ndi kuchita maere pa zovala zangazo."
Choncho izi ndi zimene asilikali anachita.
Pafupi ndi mtanda wa Yesu panayima amayi ake, mngʼono wa amayi ake, Mariya mkazi wa Kaliyopa ndi Mariya wa ku Magadala. Yesu ataona amayi ake pamenepo ndi wophunzira amene Iye anamukonda atayima pafupipo, Iye anati kwa amayi ake, "Amayi nayu mwana wanu." Anawuzanso wophunzirayo kuti, "Nawa amayi ako." Kuyambira nthawi imeneyo, wophunzirayo anatenga amayiwo kupita nawo kwawo.
Pamene anafika pamalo otchedwa Bade, anamupachika Iye pamodzi ndi achifwambawo, mmodzi kudzanja lake lamanja ndi winayo la ku lamazere. Yesu anati, "Atate, akhululukireni, pakuti sakudziwa chimene akuchita." Ndipo anagawana malaya ake mochita maere.
Anthu anayimirira nʼkumaonerera, ngakhalenso akuluakulu ankamulalatira Iye. Iwo anati, "Iye anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati ndi Khristu wa Mulungu, Wosankhidwayo."
Asilikalinso anabwera ndi kumunyoza Iye. Iwo anamupatsa vinyo wosasa, ndipo anati, "Ngati ndiwe Mfumu ya Ayuda, dzipulumutse wekha."
Ndipo panalembedwa chikwangwani pamwamba pake chimene chinati: uyu ndi mfumu ya ayuda.
Mmodzi wa achifwambawo, amene anapachikidwa, anamunenera Iye zamwano nati, "Kodi sindiwe Khristu? Dzipulumutse wekha ndi ifenso!"
Koma wachifwamba winayo anamudzudzula iye nati, "Suopa Mulungu, iwenso ukulandira chilango chomwechi? Ife tikulangidwa mwachilungamo, pakuti ife tikulandira monga mwa ntchito zathu. Koma munthu uyu sanachimwe kanthu."
Kenaka anati, "Yesu, mundikumbukire ine pamene mulowa mu ufumu wanu."
Yesu anayankha kuti, "Zoonadi, ndikukuwuza kuti lero lino udzakhala ndi Ine mʼparadaiso."
Pa ora lachisanu ndi chimodzi masana mdima unabwera pa dziko lonse mpaka pa ora lachisanu ndi chinayi masana. Pa ora lachisanu ndi chinayi Yesu analira mofuwula kuti, "Eloi, Eloi, lama sabakitani?" Kutanthauza kuti, "Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?"
Pa nthawi imeneyo chinsalu chotchinga cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati kuyambira pamwamba mpaka pansi. Dziko linagwedezeka ndipo miyala inangʼambika. Manda anatsekuka ndipo mitembo yambiri ya anthu oyera mtima amene anafa inaukitsidwa. Anatuluka mʼmanda mwawo, ndipo chitachitika chiukitso cha Yesu, anapita mu mzinda woyera naonekera kwa anthu ambiri.
Mkulu wa asilikali ndi amene ankalondera Yesu ataona chivomerezi ndi zonse zinachitika, anachita mantha, ndipo anati, "Zoonadi, uyu anali Mwana wa Mulungu!"
Koma iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu,
ndipo anamuzunza chifukwa cha zoyipa zathu;
iye analangidwa kuti ife tikhale ndi mtendere,
ndipo ndi mabala ake ife tinachiritsidwa.
Ife tonse, ngati nkhosa, tasochera,
aliyense mwa ife akungodziyendera;
ndipo Yehova wamusenzetsa
zoyipa zathu zonse.
Anthu anamuzunza ndi kumusautsa,
koma sanayankhule kanthu.
Monga mwana wankhosa wopita naye kokamupha amachitira,
kapena monga nkhosa imakhalira duu poyimeta,
momwemonso iye sanatsekule pakamwa pake.
Agalu andizungulira;
gulu la anthu oyipa landizinga.
Alasa manja ndi mapazi anga.
Ine nditha kuwerenga mafupa anga onse;
anthu amandiyangʼanitsitsa ndi kundidzuma.
Iwo agawana zovala zanga pakati pawo
ndi kuchita maere pa zovala zangazo.
Onse amene amandiona amandiseka;
amandiyankhulira mawu achipongwe akupukusa mitu yawo kunena kuti
"Iyeyu amadalira Yehova,
musiyeni Yehovayo amulanditse.
Musiyeni Yehova amupulumutse
popeza amakondwera mwa Yehovayo."
O amor que se entrega
Ninguém tem maior amor do que aquele que dá a vida pelos amigos. Deus prova seu amor em que Cristo morreu por nós quando ainda éramos pecadores.
Palibe munthu ali ndi chikondi choposa ichi, choti munthu nʼkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.
"Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha.
Pakuti pamene tinali adani a Mulungu, tinayanjanitsidwa ndi Iye kudzera mu imfa ya Mwana wake. Nanga tidzapulumutsidwa bwanji kudzera mʼmoyo wake, titayanjanitsidwa naye?
Mmene timadziwira chikondi chenicheni ndi umu: Yesu anapereka moyo wake chifukwa cha ife. Ndipo nafenso tiyenera kupereka miyoyo yathu chifukwa cha abale athu.
Iyeyo ndiye nsembe yopepesera machimo athu, ndipo osati athu okha, komanso machimo onse a dziko lapansi.
Ndipo pokhala munthu choncho
anadzichepetsa yekha
ndipo anamvera mpaka imfa yake,
imfa yake ya pamtanda!
Morte e ressurreição
Jesus morreu e ressuscitou, e a morte não mais tem domínio sobre Ele. Pelo batismo, participamos de sua morte e ressurreição.
Pakuti tikudziwa kuti popeza Khristu anaukitsidwa kwa akufa, Iye sangafenso. Imfa ilibenso mphamvu pa Iye. Imfa imene Iye anafa, anafa ku tchimo kamodzi kokha, koma moyo umene akhala ndi wa kwa Mulungu.
Kodi simukudziwa kuti tonse amene tinabatizidwa mwa Khristu Yesu tinabatizidwa mu imfa yake? Chifukwa chake ife tinayikidwa mʼmanda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo. Tinalowa mu imfa ndi cholinga choti monga momwe Khristu anaukitsidwa kwa akufa ndi ulemerero wa Atate, ifenso tikakhale mʼmoyo watsopano.
Popeza kunayikika kwa munthu kufa kamodzi ndipo kenaka kuweruzidwa, momwemonso Khristu anadzipereka nsembe kamodzi kokha kuchotsa machimo a anthu ambiri. Ndipo Iye adzaonekanso kachiwiri, osati kudzachotsa tchimo, koma kudzapereka chipulumutso kwa amene akumudikira.
"Inu Aisraeli mverani mawu awa; Yesu wa ku Nazareti anali munthu amene anaperekedwa kwa inu ndi Mulungu. Ndipo Mulungu anakutsimikizirani zimenezi ndi zamphamvu, zodabwitsa ndi zizindikiro zimene anachita mwa Iye pakati panu, monga inu mukudziwa. Yesu ameneyu anaperekedwa kwa inu mwa kufuna ndi kudziwiratu kwa Mulungu; ndipo inu mothandizidwa ndi anthu oyipa, munamupha Iye pomupachika pa mtanda. Koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa, kumumasula Iye ku zowawa za imfa, chifukwa kunali kosatheka kuti agwiridwe ndi imfa.
"Ine ndine Mʼbusa wabwino. Mʼbusa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa zake.
Pakuti nthawi zonse pamene mudya bulediyu ndikumwa chikhochi, mukulalikira imfa ya Ambuye mpaka Iye adzabweranso.