Pular para o conteúdo
Publicidade

Motivação

Por Bíblia Online

Motivação verdadeira vem de Deus. A Bíblia nos inspira a correr a carreira da fé com perseverança, sabendo que o Senhor fortalece, guia e recompensa os fiéis.

Força do alto

Tudo posso naquele que me fortalece. Deus dá poder aos fracos e renova a força dos cansados — Ele é a fonte de toda motivação.

Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu.

Iye amalimbitsa ofowoka

ndipo otopa amawawonjezera mphamvu.

Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufowoka,

ndipo achinyamata amapunthwa ndi kugwa;

koma iwo amene amakhulupirira Yehova

adzalandira mphamvu zatsopano.

Adzawuluka ngati chiwombankhanga;

adzathamanga koma sadzalefuka,

adzayenda koma sadzatopa konse.

Ine ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Yehova;

moyo wanga ukukondwera chifukwa cha Mulungu wanga.

Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso,

ndipo wandiveka mkanjo wachilungamo.

Zili ngati mkwati wovala nkhata ya maluwa mʼkhosi mwake,

ndiponso ngati mkwatibwi wovala mikanda yamtengowapatali.

pakuti ndi Mulungu amene amagwira ntchito mwa inu kuti mufune ndi kuchita zimene zimamukondweretsa Iyeyo.

Correr para o alvo

Prossigo para o alvo, para o prêmio da soberana vocação de Deus em Cristo Jesus. A corrida da fé exige disciplina e foco.

Abale, sindidziyesera ndekha kuti ndachipeza kale chimenechi. Koma chinthu chimodzi chimene ndimachita, nʼkuyiwala zamʼmbuyo ndi kuthamangira molimbika zinthu zimene zili mʼtsogolo mwanga. Ndikuthamangira kokathera mpikisanowo kuti ndikalandire mphotho imeneyi kumwamba, imene Mulungu anandiyitanira mwa Khristu Yesu.

Kufunika kwa Kudziretsa

Kodi simukudziwa kuti pa mpikisano wa liwiro onse amathamanga ndithu, koma mmodzi yekha ndiye amalandira mphotho? Motero thamangani kuti mupate mphotho. Aliyense wochita mpikisano amakonzekera mwamphamvu. Amachita izi kuti alandire mphotho yankhata yamaluwa yomwe imafota. Koma ife timachita izi kuti tilandire mphotho yosafota. Choncho sindithamanga monga wothamanga wopanda cholinga; komanso sindichita mpikisano wankhonya monga munthu amene amangomenya mophonya. Ine ndimazunza thupi langa ndi kulisandutsa kapolo kuti nditatha kulalikira ena, ineyo ndingadzapezeke wosayenera kulandira nawo mphotho.

Yesu Chitsanzo Chathu

Tsono popeza ifenso tazunguliridwa ndi gulu lalikulu la mboni, tiyeni titaye chilichonse chimene chimatitchinga, makamaka tchimo limene limatikola mosavuta, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu. Tiyeni tiyangʼanitsitse Yesu, amene ndi woyamba ndi wotsiriza wa chikhulupiriro chathu. Chifukwa cha chimwemwe chimene chimamudikira anapirira zowawa zapamtanda. Iye ananyoza manyazi a imfa yotere ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando waufumu wa Mulungu. Muzilingalira za Iye amene anapirira udani waukulu chotere wochokera kwa anthu ochimwa, kuti musafowoke ndi kutaya mtima.

Chilichonse mungachite, muchite ndi mtima wanu onse, monga mmene mungagwirire ntchito ya Ambuye osati ya anthu.

Propósito e missão

Deus tem planos de esperança para nós. Cada dia é oportunidade de fazer a sua vontade e avançar com confiança na missão.

Pakuti Ine ndikudziwa zimene ndinakukonzerani," akutero Yehova, "ndimalingalira zabwino zokhazokha za inu osati zoyipa, ayi. Ndimalingalira zinthu zokupatsani chiyembekezo chenicheni pa za mʼtsogolo.

Ndipo Ine ndidzachita chilichonse chimene inu mudzapempha mʼdzina langa kuti Atate alemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzapempha kanthu kalikonse mʼdzina langa, Ine ndidzachita.

Chifukwa chake, pitani kaphunzitseni anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza mʼdzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera, ndi kuwaphunzitsa amvere zonse zimene ndinakulamulirani. Ndipo onani, Ine ndidzakhala pamodzi ndi inu kufikira kutha kwa dziko lapansi pano."

Khalani amphamvu ndi olimba mtima. Musachite nawo mantha kapena kunjenjemera pamaso pawo, chifukwa Yehova Mulungu wanu apita nanu. Sadzakusiyani kapena kukutayani."

Ntchito iliyonse imene ukuyigwira, uyigwire ndi mphamvu zako zonse, pakuti ku manda kumene ukupita kulibe kugwira ntchito, kulibe malingaliro, chidziwitso ndiponso nzeru.

Anthu 1,000 atha kufa pambali pako,

anthu 10,000 kudzanja lako lamanja,

koma zoopsazo sizidzafika pafupi ndi iwe.

Ndipo musayike mtima wanu pa zimene mudzadye kapena kumwa; musade nazo nkhawa. Pakuti anthu akunja amathamanga kufunafuna zinthu zotere, ndipo Atate amadziwa kuti mumazifuna zimenezi.

Pakuti ngakhale pamene tinali nanu, tinakupatsani lamulo lakuti, "Munthu wosafuna kugwira ntchito, asadye."

Ife tikumva kuti pakati panu pali ena amene ndi alesi. Iwo safuna kugwira ntchito, koma amangolowerera pa za eni. Mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, tikuwalamula ndi kuwakakamiza kuti azigwira ntchito mwabata ndi kumadya chakudya chodzigwirira ntchito okha. Koma inu abale, musatope nʼkuchita zabwino.

Seja o primeiro