A mulher sábia
A mulher sábia constrói sua casa sobre o fundamento do temor do Senhor. Sua sabedoria abençoa a família, a comunidade e as gerações futuras.
A sabedoria que edifica
A mulher sábia edifica sua casa. O temor do Senhor é o princípio da sabedoria e a instrução que conduz à honra.
Mkazi wanzeru amamanga banja lake,
koma mkazi wopusa amalimasula ndi manja ake omwe.
Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru;
kudziwa Woyerayo ndiko kukhala womvetsa bwino zinthu.
Kuopa Yehova kumaphunzitsa munthu nzeru,
ndipo kudzichepetsa ndi ulemu chili patsogolo ndi kudzichepetsa.
Ngati wina pakati panu akusowa nzeru, apemphe kwa Mulungu amene amapereka kwa onse mwaulere ndi mosatonzera, ndipo adzapatsidwa.
Dalirani Yehova ndi mphamvu zake;
funafunani nkhope yake nthawi zonse.
Virtude e excelência
A mulher virtuosa é coroada de força e dignidade. Ela abre a boca com sabedoria e a instrução da bondade está na sua língua.
Mathero: Mkazi Wangwiro
Kodi mkazi wangwiro angathe kumupeza ndani?
Ndi wokwera mtengo kuposa miyala yamtengowapatali.
Mphamvu ndi ulemu zimakhala ngati chovala chake;
ndipo amaseka osaopa zamʼtsogolo.
Iye amayankhula mwanzeru,
amaphunzitsa anthu mwachikondi.
Ana ake amamunyadira ndipo amamutcha kuti wodala;
ndipo mwamuna wake, amamuyamikira nʼkumati,
"Pali akazi ambiri amene achita zinthu zopambana
koma iwe umawaposa onsewa."
Nkhope yachikoka ndi yonyenga, ndipo kukongola nʼkosakhalitsa;
koma mkazi amene amaopa Yehova ayenera kutamandidwa.
Mkazi wakhalidwe labwino ali ngati chipewa chaufumu kwa mwamuna wake,
koma mkazi wochititsa manyazi ali ngati chilonda cha mafinya kwa mwamuna wake.
Mkazi wodekha amalandira ulemu,
koma amuna ankhanza amangopata chuma.
Nyumba ndi chuma ndiye cholowa chochokera kwa makolo;
koma mkazi wanzeru ndi wochokera kwa Yehova.
Exemplo e influência
A mulher sábia é exemplo de fé e bom testemunho. Suas atitudes inspiram e seu legado abençoa as gerações que virão.
Chimodzimodzinso, phunzitsa amayi achikulire kuti akhale aulemu mʼmakhalidwe awo, asakhale osinjirira anzawo kapena zidakwa, koma akhale alangizi abwino. Tsono atha kulangiza amayi achichepere kukonda amuna awo ndi ana awo. Kuwaphunzitsa kukhala odziletsa ndi oyera mtima, osamala bwino mabanja awo, okoma mtima, ndi ogonjera amuna awo. Choncho palibe amene adzanyoze mawu a Mulungu.
Momwemonso, akazi akhale olemekezeka, osasinjirira koma oganiza bwino ndi odalirika pa chilichonse.
Fanizo la Anamwali Khumi
"Nthawi imeneyo ufumu wakumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi amene anatenga nyale zawo napita kukakumana ndi mkwati. Asanu anali opusa ndipo asanu ena anali ochenjera. Opusawo anatenga nyale zawo koma sanatenge mafuta; koma ochenjerawo anatenga mafuta awo mʼmabotolo pamodzi ndi nyale zawo. Mkwati anachedwa ndipo onse anayamba kusinza nagona.
"Pakati pa usiku kunamveka kufuwula kuti, ‘Onani Mkwati! Tulukani kuti mukakumane naye!’
"Pamenepo anamwali onse anadzuka nayatsa nyale zawo. Opusawo anati kwa ochenjerawo, ‘Tipatseniko mafuta anu; nyale zathu zikuzima.’
"Ochenjerawo anayankha, nati, ‘Ayi sangakwanire inu ndi ife. Pitani kwa ogulitsa mafuta ndi kukadzigulira nokha.’
"Koma pamene ankapita kukagula mafutawo, mkwati anafika. Anamwali amene anali okonzeka aja analowa naye pamodzi mʼnyumba ya phwando la ukwati. Ndipo khomo linatsekedwa.
"Pambuyo pake enawo anabwera nati, ‘Ambuye! Ambuye! Titsekulireni!’
"Koma iye anayankha kuti, ‘Zoonadi, ine ndikuwuzani kuti sindikukudziwani.’
"Choncho khalani odikira, popeza simudziwa tsiku kapena nthawi."