Pular para o conteúdo
Publicidade

Não desista!

Por Bíblia Online

'Não desista!' é o grito do céu para a terra. Deus nos encoraja a perseverar na fé, na oração e na esperança, porque a vitória pertence aos que não se rendem.

Força na fraqueza

Os que esperam no Senhor renovam as forças. Deus não se cansa nem se fatiga — Ele dá poder aos fracos e vigor aos cansados.

Kodi simukudziwa?

Kodi simunamve?

Yehova ndiye Mulungu wamuyaya,

ndiyenso Mlengi wa dziko lonse lapansi.

Iye sadzatopa kapena kufowoka

ndipo palibe amene angadziwe maganizo ake.

Iye amalimbitsa ofowoka

ndipo otopa amawawonjezera mphamvu.

Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufowoka,

ndipo achinyamata amapunthwa ndi kugwa;

koma iwo amene amakhulupirira Yehova

adzalandira mphamvu zatsopano.

Adzawuluka ngati chiwombankhanga;

adzathamanga koma sadzalefuka,

adzayenda koma sadzatopa konse.

Inu anthu a ku Ziyoni, amene mukhala mu Yerusalemu simudzaliranso. Mulungu adzakukomerani mtima pamene adzamva kulira kwanu kopempha thandizo! Ndipo akadzamva, adzakuyankhani.

Yehova Yekha Mpulumutsi wa Israeli

Koma tsopano, Yehova

amene anakulenga, iwe Yakobo,

amene anakuwumba, iwe Israeli akuti,

"Usaope, pakuti ndakuwombola;

Ndinakuyitanitsa mokutchula dzina lako, ndiwe wanga.

Pamene ukuwoloka nyanja,

ndidzakhala nawe;

ndipo pamene ukuwoloka mitsinje,

sidzakukokolola.

Pamene ukudutsa pa moto,

sudzapsa;

lawi la moto silidzakutentha.

Chifukwa Ine Yehova, Mulungu wako,

Woyera wa Israeli, ndine Mpulumutsi wako.

Ndinapereka Igupto pofuna kuti ndiwombole iwe,

ndinapereka Kusi ndi Seba mʼmalo mwa iwe.

Ndimadziwa kusauka nʼkutani, ndipo ndimadziwa kulemera nʼkutani. Ndaphunzira chinsinsi chokhala wokhutitsidwa mwa njira ina iliyonse, kaya nʼkudya bwino kapena kukhala ndi njala, kaya kukhala ndi chuma kapena umphawi. Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu.

Nʼchifukwa chake ife sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifowokerafowokera, koma mʼkatimu tikulimbikitsidwa mwatsopano tsiku ndi tsiku. Pakuti masautso athu ndi opepuka ndi a kanthawi, koma akutitengera ulemerero wamuyaya umene ndi wopambana kwambiri. Motero sitiyangʼana zinthu zimene ndi zooneka ndi maso, koma zinthu zimene ndi zosaoneka. Pakuti zimene zimaoneka ndi zosakhalitsa, koma zimene sizioneka ndi zamuyaya.

Perseverança na fé

Não perca a confiança, pois ela tem grande recompensa. O justo viverá pela fé, e quem perseverar até o fim será salvo.

Tsono musataye kulimbika mtima kwanuko pakuti mudzalandira nako mphotho yayikulu.

Tiyeni tigwiritsitse mosagwedezeka zimene timaziyembekezera ndi kuzivomereza, pakuti amene anatilonjezayo ndi wokhulupirika. Tiziganizira mmene tingalimbikitsirane wina ndi mnzake pokondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tiyeni tisaleke kusonkhana kwathu pamodzi monga mmene ena amachitira, koma tizilimbikitsana makamaka poona kuti tsiku la Ambuye layandikira.

Ndipo popanda chikhulupiriro nʼkosatheka kukondweretsa Mulungu, chifukwa aliyense amene amabwera kwa Iye ayenera kukhulupirira kuti Mulungu alipodi ndi kuti Iye amapereka mphotho kwa amene akumufunitsitsa.

Paja Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amalowa mpaka molumikizirana moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana fundo ndi mafuta a mʼmafupa. Amaweruza malingaliro ndi zokhumba za mʼmitima.

Tisatope nʼkuchita zabwino, pakuti pa nthawi yoyenera tidzakolola ngati sititopa.

Ine ndikubwera msanga. Gwiritsitsa chimene uli nacho kuti wina angakulande chipewa chako chaufumu.

Pamenepa ndi pofunika kupirira kwa anthu oyera mtima amene amasunga malamulo a Mulungu ndi kukhalabe okhulupirika kwa Yesu.

Wodala ndi munthu amene amapirira mʼmayesero, chifukwa akapambana adzalandira chipewa cha ulemerero chimene Mulungu analonjeza anthu amene amamukonda.

Deus é refúgio

O Senhor é nosso refúgio e fortaleza. Ele ouve nossas orações, nos consola nas tribulações e transforma choro em dança.

Mulungu ndiye kothawira kwathu ndi mphamvu yathu,

thandizo lopezekeratu pa nthawi ya mavuto.

Tulani nkhawa zanu kwa Yehova

ndipo Iye adzakulimbitsani;

Iye sadzalola kuti wolungama agwe.

Yehova ndiye kothawirako kwa opsinjika mtima,

linga pa nthawi ya mavuto.

Iwo amene amadziwa dzina lanu adzadalira Inu,

pakuti Inu Yehova, simunawatayepo amene amafunafuna inu.

Iwo amene amafesa akulira,

adzakolola akuyimba nyimbo zachimwemwe.

Iye amene amayendayenda nalira,

atanyamula mbewu yokafesa,

adzabwerera akuyimba nyimbo zachimwemwe,

atanyamula mitolo yake.

Khalani ndi nyonga ndipo limbani mtima,

inu nonse amene mumayembekezera Yehova.

Mawu anu ndi nyale ya kumapazi kwanga

ndi kuwunika kwa pa njira yanga.

Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuyitana,

onse amene amamuyitana Iye mʼchoonadi.

Iye amakwaniritsa zokhumba za iwo amene amamuopa;

amamva kulira kwawo ndi kuwapulumutsa.

Vitória em Cristo

Jesus venceu o mundo e nos dá vitória. Para Deus nada é impossível, e Ele faz infinitamente mais do que pedimos ou pensamos.

"Ine ndakuwuzani izi kuti mwa Ine mukhale nawo mtendere. Mʼdziko lapansi mudzakhala nawo mavuto. Koma limbikani mtima! Ine ndaligonjetsa dziko lapansi."

Kuyambira nthawi imeneyi ophunzira ake ambiri anabwerera ndipo sanamutsatenso Iye.

Yesu anafunsa khumi ndi awiriwo kuti, "Kodi inu mukufuna kuchokanso?"

Simoni Petro anamuyankha Iye kuti, "Ambuye, ife tidzapita kwa yani? Inu muli ndi mawu amoyo wosatha. Ife tikhulupirira ndi kudziwa kuti Inu ndinu Woyerayo wa Mulungu."

Ine sindikusiyani nokha kuti mukhale ana amasiye. Ine ndidzabweranso kwa inu.

Pemphani, Funafunani, Gogodani

"Pemphani ndipo mudzapatsidwa; funafunani ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsekulirani. Pakuti wopempha aliyense amalandira; ndi wofuna amapeza; ndipo iye amene agogoda, adzamutsekulira.

"Idzani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa. Ndipo inu mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa ndi losavuta ndipo katundu wanga ndi wopepuka."

Yesu anawayangʼana iwo nati, "Ndi anthu, izi nʼzosatheka, koma ndi Mulungu zinthu zonse zimatheka."

Pakuti palibe chinthu chosatheka ndi Mulungu."

Esperança e transformação

O Senhor completa a boa obra que começou em nós. Ele faz novas todas as coisas e dá esperança para o futuro.

Sindikukayika konse kuti Iye amene anayamba ntchito yabwino mwa inu adzayipitiriza ndi kuyimaliza mpaka pa tsiku la kubweranso kwa Khristu Yesu.

Nʼchifukwa chake, ngati munthu aliyense ali mwa Khristu, ndi wolengedwa kwatsopano; zinthu zakale zapita taonani, zakhala zatsopano.

Kumwamba ndi Dziko Lapansi Zatsopano

Kenaka ndinaona kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano pakuti kumwamba koyamba ndi dziko lapansi loyamba zinapita ndipo kunalibenso nyanja ina iliyonse. Ndinaona mzinda wopatulika, Yerusalemu watsopano, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu, utakonzedwa ngati mkwatibwi wovala zokongola kukonzekera mwamuna wake. Ndipo ndinamva mawu ofuwula kuchokera ku Mpando Waufumu kuti, "Taonani! Malo wokhalapo Mulungu ali pakati pa anthu, ndipo Iye adzakhala ndi anthuwo. Iwo adzakhala anthu ake ndipo Mulungu mwini adzakhala nawo nakhala Mulungu wawo. Mulungu adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo. Sikudzakhalanso imfa kapena kukhuza maliro kapena kulira kapena ululu popeza zakale zapita.’ "

Yehova ndi wabwino,

ndiye kothawirako nthawi ya masautso.

Amasamalira amene amamudalira,

Pakuti Ine ndikudziwa zimene ndinakukonzerani," akutero Yehova, "ndimalingalira zabwino zokhazokha za inu osati zoyipa, ayi. Ndimalingalira zinthu zokupatsani chiyembekezo chenicheni pa za mʼtsogolo.

Koma inu, khalani amphamvu ndipo musataye mtima, pakuti mudzalandira mphotho ya ntchito yanu."

Permanecendo firme

Persevere na oração, firme-se na Palavra e fortaleça-se na graça de Cristo. A fé vem pelo ouvir, e o ouvir pela Palavra de Deus.

Musakhale aulesi mʼmachitidwe anu. Khalani achangu mu mzimu ndipo tumikirani Ambuye. Kondwerani mʼchiyembekezo, pirirani mʼmasautso ndiponso khulupirikani mʼpemphero.

Kondwerani mʼchiyembekezo, pirirani mʼmasautso ndiponso khulupirikani mʼpemphero.

Okondedwa anga, musabwezere choyipa, koma lekerani Mulungu. Pakuti kwalembedwa, "Kubwezera chilango nʼkwanga. Ndidzawalanga ndine," akutero Ambuye.

Motero, chikhulupiriro chimabwera pamene timva uthenga ndipo uthenga umamveka kuchokera ku mawu a Khristu.

Oposa Agonjetsi

Ndipo ife tikudziwa kuti zinthu zonse zimathandizana kuwachitira ubwino amene amakonda Mulungu, amene anayitanidwa monga mwa cholinga chake.

Malemba onse anawalembetsa ndi Mulungu, ndipo othandiza pophunzitsa, podzudzula, pokonza cholakwika ndi polangiza za chilungamo kuti munthu wa Mulungu akonzekere bwino lomwe kugwira ntchito iliyonse yabwino.

Zimene unamva kwa ine, uzisunge kuti zikhale chitsanzo cha chiphunzitso choona, mwa chikhulupiriro ndi chikondi mwa Khristu Yesu. Samalira bwino zokoma zimene anakusungitsa. Uzisamalire mothandizidwa ndi Mzimu Woyera amene amakhala mwa ife.

Ambuye athu Yesu Khristu mwini ndi Mulungu Atate wathu, amene anatikonda ife ndipo mwachisomo chake anatipatsa kulimba mtima kwamuyaya ndi chiyembekezo chabwino, akulimbikitseni ndi kukupatsani mphamvu yogwirira ntchito ndi kuyankhula zabwino zilizonse.

Koma tikavomereza machimo athu, Iye ndi wokhulupirika ndi wolungama ndipo adzatikhululukira machimo athu, nadzatiyeretsa ndi kutichotsera chosalungama chilichonse.

Ife timalimba mtima tikamafika pamaso pa Mulungu, popeza kuti ngati tipempha kanthu kalikonse monga mwa chifuniro chake, amatimvera. Ndipo ngati tikudziwa kuti amatimvera, chilichonse chimene timapempha, tikudziwanso kuti tili nacho chimene tamupempha Iye.

Chimatchinjiriza nthawi zonse, chimakhulupirika nthawi zonse, chimakhala ndi chiyembekezo nthawi zonse, chimapirira nthawi zonse.

Seja o primeiro