Publicidade

Não temas

Por Bíblia Online

'Não temas' é uma das frases mais repetidas na Bíblia. Deus a pronuncia nos momentos de maior temor, lembrando que sua presença e poder são maiores que qualquer ameaça.

Deus está contigo

Não temas, porque eu sou contigo. Deus repete essa promessa em cada crise, guerra e desafio que seus filhos enfrentam.

Tsono usaope, pakuti Ine ndili nawe;

usataye mtima chifukwa Ine ndine Mulungu wako.

Ndidzakupatsa mphamvu ndipo ndidzakuthandiza,

ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

Pakuti Ine Yehova, ndine Mulungu wako,

amene ndikukugwira dzanja lako lamanja

ndipo ndikuti, usaope;

ndidzakuthandiza.

Usachite mantha, iwe Yakobo wofowoka ngati nyongolotsi,

iwe wochepa mphamvu Israeli,

chifukwa Ine ndidzakuthandiza,"

akutero Yehova Mpulumutsi wako, Woyerayo wa Israeli.

Iwe amene ukulengeza nkhani yabwino ku Ziyoni,

kwera pa phiri lalitali.

Iwe amene ukulengeza nkhani yabwino ku Yerusalemu,

fuwula kwambiri,

kweza mawu, usachite mantha;

uza mizinda ya ku Yuda kuti,

"Mulungu wanu akubwera!"

Paja ndinakulamula kuti ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima. Choncho usamachite mantha kapena kutaya mtima popeza Ine Yehova Mulungu wako ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite."

Khalani amphamvu ndi olimba mtima. Musachite nawo mantha kapena kunjenjemera pamaso pawo, chifukwa Yehova Mulungu wanu apita nanu. Sadzakusiyani kapena kukutayani."

Pangano la Mulungu ndi Abramu

Zitatha izi, Yehova anayankhula ndi Abramu mʼmasomphenya nati:

"Usaope Abramu.

Ine ndili ngati chishango chokutchinjiriza.

Mphotho yako idzakhala yayikulu."

Coragem diante do perigo

Não tenhas medo — o Senhor teu Deus está no meio de ti, poderoso para salvar. Ele luta por nós e dá forças aos medrosos.

Pa tsiku limenelo adzanena kwa Yerusalemu kuti,

"Usaope, iwe Ziyoni;

usafowoke.

Yehova Mulungu wako ali pakati pako,

ali ndi mphamvu yopulumutsa.

Adzakondwera kwambiri mwa iwe,

adzakukhalitsa chete ndi chikondi chake,

adzayimba mokondwera chifukwa cha iwe."

Mneneri anamuyankha kuti, "Usachite mantha. Amene ali mbali yathu ndi ambiri kupambana amene ali mbali yawo."

Ndipo Elisa anapemphera kuti, "Inu Yehova tsekulani maso ake kuti aone." Pamenepo Yehova anatsekula maso a mtumikiyo, ndipo anayangʼana naona kuti phiri lonse linali lodzaza ndi akavalo ndi magaleta a moto atazungulira Elisa.

Iwe dziko usachite mantha;

sangalala ndipo kondwera.

Zoonadi Yehova wachita zinthu zazikulu.

Koma Yehova anandiwuza kuti, "Usanene kuti, Ndikanali wamngʼonopopeza udzapita kwa munthu aliyense kumene ndidzakutuma ndi kunena chilichonse chimene ndidzakulamulira. Usawaope, pakuti Ine ndili nawe, ndipo ndidzakupulumutsa," akutero Yehova.

Usiku wina Ambuye anaonekera kwa Paulo mʼmasomphenya namuwuza kuti, "Usaope, pitiriza kuyankhula, usakhale chete. Pakuti Ine ndili nawe, palibe aliyense amene adzakukhudza ndi kukuchitira choyipa, chifukwa mu mzinda muno ndili ndi anthu ambiri."

Tsono iwe mwana wa munthu, usachite nawo mantha kapena kuopa zimene azikanena. Usachite mantha, ngakhale minga ndi mkandankhuku zikuzinge ndipo ukukhala pakati pa zinkhanira. Usachite mantha ndi zimene akunena kapena kuopsedwa ndi nkhope zawo, popeza anthuwa ndi awupandu. Ukawawuze ndithu mawu anga, kaya akamva kaya sakamva. Paja anthuwa ndi awupandu.

Fé que vence o medo

O medo não vem de Deus. Jesus disse: não temas, crê somente! A fé dissipa o medo e nos conecta ao poder de Deus.

Posasamala zomwe ananena, Yesu anamuwuza mkulu wa sunagoge uja kuti, "Usachite mantha; ingokhulupirira."

Musachite mantha ndi zimene muti musauke nazo posachedwapa. Ndithu, Satana adzayika ena a inu mʼndende pofuna kukuyesani, ndipo mudzazunzika kwa masiku khumi. Khalani okhulupirika ngakhale zitafika pa imfa, ndipo Ine ndidzakupatsani chipewa cha ulemerero wamoyo.

Musamaope amene amapha thupi koma sangathe kuchotsa moyo. Koma muziopa Iye amene akhoza kupha mzimu ndi kuwononga thupi mu gehena.

Koma akuganiza zimenezi, taonani, mngelo wa Ambuye anamuonekera mʼmaloto nati, "Yosefe mwana wa Davide, usaope kumutenga Mariya kukhala mkazi wako, chifukwa mwana akuyembekezerayo ndi wochokera kwa Mzimu Woyera.

Koma mngeloyo anati kwa iye, "Usachite mantha Mariya, pakuti wapeza chisomo pamaso Mulungu.

Simoni Petro ataona izi, anagwa pa mawondo a Yesu nati, "Chokani kwa ine Ambuye: Ine ndine munthu wochimwa!"

Seja o primeiro
Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-28_14-13-17-