Natal
O Natal celebra o maior milagre da história: Deus se fez homem. O menino Jesus, nascido em Belém, é Emanuel — Deus conosco — a esperança do mundo inteiro.
O nascimento do Salvador
O anjo anunciou: hoje vos nasceu um Salvador, que é Cristo, o Senhor! A virgem concebeu pelo Espírito Santo e deu à luz o Filho de Deus.
Koma mngeloyo anawawuza kuti, "Musachite mantha. Ine ndakubweretserani Uthenga Wabwino wachimwemwe chachikulu umene udzakhala wa anthu onse.
Lero mʼmudzi wa Davide wakubwadwirani Mpulumutsi; Iye ndi Khristu Ambuye.
Choncho Yosefe anachoka ku Nazareti ku Galileya kupita ku Yudeya, ku Betelehemu ku mudzi wa Davide, chifukwa anali wa banja ndi fuko la Davide. Iye anapita kumeneko kukalembetsa pamodzi ndi Mariya, amene anapalana naye ubwenzi kuti akwatirane ndipo anali woyembekezera.
Ali kumeneko, nthawi inakwana yakuti mwana abadwe, ndipo anabereka mwana wake woyamba, wamwamuna. Iye anamukulunga mʼnsalu ndi kumuyika modyera ngʼombe, chifukwa kunalibe malo mʼnyumba ya alendo.
A profecia cumprida
Isaías profetizou: a virgem conceberá e dará à luz um filho que se chamará Emanuel. Em Jesus, essa promessa se cumpriu perfeitamente.
Nʼchifukwa chake Ambuye mwini adzakupatsani chizindikiro: Onani, namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli.
Koma akuganiza zimenezi, taonani, mngelo wa Ambuye anamuonekera mʼmaloto nati, "Yosefe mwana wa Davide, usaope kumutenga Mariya kukhala mkazi wako, chifukwa mwana akuyembekezerayo ndi wochokera kwa Mzimu Woyera.
Ndipo adzabala mwana wamwamuna, udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo."
Zonsezi zinachitika kukwaniritsa zimene Ambuye ananena mwa mneneri kuti, "Onani namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli," kutanthauza kuti, "Mulungu ali nafe."
Glória a Deus nas alturas
Os pastores glorificaram a Deus e os anjos cantaram: 'Glória a Deus nas alturas e paz na terra entre os homens a quem Ele quer bem!'
"Ulemerero kwa Mulungu mmwambamwamba,
ndi mtendere kwa anthu pa dziko lapansi amene Iye akondwera nawo."
Abusa anabwerera, akulemekeza ndi kuyamika Mulungu chifukwa cha zonse anazimva ndi kuziona, zomwe zinali monga anawuzidwira ndi angelo aja.