Pular para o conteúdo
Publicidade

Obediência aos pais

Por Bíblia Online

A obediência aos pais é mandamento divino com promessa de vida longa. A Bíblia valoriza a honra filial e ensina os filhos a respeitar e obedecer aos pais com amor.

Honrar pai e mãe

O quinto mandamento ordena honrar pai e mãe. É o primeiro mandamento com promessa: para que vá bem e vivas muito na terra.

"Lemekeza abambo ako ndi amayi ako kuti ukhale ndi moyo wautali mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.

"Lemekeza abambo ako ndi amayi ako monga Yehova Mulungu wako wakulamulira iwe kuti ukhale ndi moyo wautali ndi kuti zikuyendere bwino mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.

Pakuti Mulungu anati, Lemekeza abambo ako ndi amayi akondipo aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa.

Ana ndi Makolo Awo

Inu ana, mverani makolo anu mwa Ambuye, pakuti zimenezi ndi zoyenera. "Lemekeza abambo ndi amayi ako." Limeneli ndi lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo. Ngati ulemekeza abambo ako ndi amayi ako, "zinthu zidzakuyendera bwino ndipo udzasangalala ndi moyo wautali pa dziko lapansi." Abambo musakwiyitse ana anu; mʼmalo mwake, muwalere mʼchiphunzitso ndi mʼchilangizo cha Ambuye.

Obedecer e respeitar

Filhos, obedecei a vossos pais no Senhor. A obediência filial é expressão de amor e temor a Deus.

Inu ana, mverani makolo anu mu zonse pakuti izi zimakondweretsa Ambuye.

Malangizo kuti Asunge Nzeru

Malangizo kwa Achinyamata

Mwana wanga, mvera malangizo a abambo ako

ndipo usakane mawu okuwongolera a amayi ako.

Ali ngati sangamutu yokongola ya maluwa pamutu pako

ndiponso ali ngati mkanda mʼkhosi mwako.

Chenjezo pa za Chigololo

Mwana wanga, usunge malamulo a abambo ako;

ndipo usataye zimene anakuphunzitsa amayi ako.

Zimenezi uzimatirire pa mtima pako masiku onse,

uzimangirire mʼkhosi mwako.

Ukamayenda, zidzakulozera njira;

ukugona, zidzakulondera;

ukudzuka, zidzakuyankhula.

Paja malamulo awa ali ngati nyale,

malangizowa ali ngati kuwunika,

ndipo chidzudzulo cha mwambo ndiwo

moyo weniweni,

Nzeru Iposa Zonse

Ananu, mverani malangizo a abambo anu;

tcherani khutu kuti mupeze nzeru zodziwira zinthu.

Zimene ndikukuphunzitsani ndi zabwino.

Choncho musasiye malangizo anga.

Paja ndinalinso mwana mʼnyumba mwa abambo anga;

mwana mmodzi yekha wapamtima pa amayi anga.

Ndipo abambo anandiphunzitsa ndi mawu akuti,

"Ugwiritse mawu anga pa mtima pako,

usunge malamulo anga kuti ukhale ndi moyo.

Upeze nzeru, upeze nzeru zomvetsa zinthu;

usayiwale mawu anga kapena kutayana nawo.

Usasiye nzeru ndipo idzakusunga.

Uziyikonda ndipo idzakuteteza.

Mwana wanzeru amamvera malangizo a abambo ake,

koma mwana wonyoza samamvetsera chidzudzulo.

Mwana muzimuphunzitsa njira yake,

ndipo akadzakalamba sadzachokamo.

Disciplina e consequências

A vara e a repreensão dão sabedoria. A Bíblia adverte sobre as consequências sérias da rebeldia e desonra aos pais.

Ndodo ndi chidzudzulo zimapatsa nzeru

koma mwana womulekerera amachititsa amayi ake manyazi.

Mwana wochita ndewu ndi abambo ake ndi kuthamangitsa amayi ake,

ndi mwana wochititsa manyazi ndi wonyozetsa.

Aliyense amene amanyoza abambo ake,

ndi kunyozera kumvera amayi ake,

makwangwala a ku chigwa adzamukolowola maso

ndipo mphungu zidzadya mnofu wake.

"Munthu aliyense amene amenya abambo ake kapena mayi ake ayenera kuphedwa.

Mwana Wamwamuna Wowukira

Ngati munthu ali ndi mwana wamwamuna wosamvera ndi wowukira amene samvera a abambo ake ndi amayi ake akamuweruza, abambo ndi amayi ake amugwire ndi kupita naye kwa akuluakulu ku chipata cha mzinda wake ndipo akawawuze akuluakuluwo kuti, "Mwana wathu wamwamunayu ndi wosamva ndi wowukira. Iyeyu satimvera. Ndi mwana wadyera komanso ndi chidakwa." Pamenepo anthu onse a mu mzinda wake adzamuphe ndi miyala. Muyenera kuchotsa zoyipa pakati panu. Aisraeli onse adzamva zimenezi ndipo adzachita mantha.

Ngati munthu atemberera abambo ake kapena amayi ake,

moyo wake udzazimitsidwa ngati nyale mu mdima wandiweyani.

Pamene mukupirira masautso monga chilango, Mulungu achitira inu monga ana ake. Kodi ndi mwana wotani amene abambo ake samulanga?

Koma ngati mkazi wamasiye ali ndi ana ndi zidzukulu, anawo ayambe aphunzira kukwaniritsa udindo wawo pa banja lawo moopa Mulungu, potero akubweza zabwino kwa makolo awo ndi agogo awo. Pakuti zimenezi ndiye zimakondweretsa Mulungu.

Seja o primeiro