Publicidade

Obediência

Por Bíblia Online

A obediência a Deus é a resposta natural do amor. Jesus disse: 'Se me amais, guardareis os meus mandamentos.' A obediência abre portas de bênção e nos aproxima do coração de Deus.

Obedecer é melhor que sacrificar

Deus deseja obediência acima de rituais. O sacrifício sem submissão ao Senhor é vazio de significado espiritual.

Koma Samueli anayankha kuti,

"Kodi Yehova amakondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zina

kapena kumvera mawu a ake?

Taona, kumvera ndi kwabwino kuposa nsembe,

ndipo kutchera khutu ndi kwabwino kuposa kupereka mafuta a nkhosa.

Petro ndi atumwi enawo anayankha kuti, "Ife tiyenera kumvera Mulungu osati anthu!

Ife ndife mboni za zimenezi, ndiponso Mzimu Woyera amene Mulungu anapereka kwa iwo akumvera Iye."

Ngakhale Iye anali Mwana wa Mulungu anaphunzira kumvera pomva zowawa. Atasanduka wangwiro kotheratu, anakhala gwero la chipulumutso chosatha kwa onse omvera Iye.

Obedecer aos mandamentos de Cristo

Jesus vinculou amor a obediência. Quem ama a Deus guarda seus mandamentos, e seus mandamentos não são pesados.

Lonjezo la Mzimu Woyera

"Ngati mundikonda Ine, sungani malamulo anga.

Yesu anamuyankha kuti, "Ngati wina aliyense andikonda Ine, adzasunga mawu anga. Atate wanga adzamukonda, ndipo Ife tidzabwera ndi kukhala naye.

Pakuti kukonda Mulungu ndiye kusunga malamulo ake. Ndipo malamulo ake siwolemetsa,

Anzanga okondedwa, ngati mitima yathu sikutitsutsa, tili nako kulimbika mtima pamaso pa Mulungu. Ndipo timalandira chilichonse chimene tichipempha kwa Iye, chifukwa timamvera malamulo ake ndi kuchita zimene zimamukondweretsa.

Womanga Nyumba Wanzeru ndi Wopusa

"Kodi nʼchifukwa chiyani munditchula kuti, Ambuye, Ambuyekoma simuchita zimene Ine ndinena?

Ndipo Iye anawuza onse kuti, "Ngati wina aliyense akufuna kutsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kusenza mtanda wake tsiku ndi tsiku nʼkumanditsata Ine.

Obedecer e praticar a Palavra

Sejam praticantes da Palavra. Quem ouve e pratica é como o homem sábio que construiu sobre a rocha firme — inabalável.

Musamangomvetsera chabe mawu, ndi kumadzinyenga nokha. Chitani zimene mawuwo amanena.

Musamangomvetsera chabe mawu, ndi kumadzinyenga nokha. Chitani zimene mawuwo amanena.

Dziperekeni nokha kwa Mulungu. Mukaneni Mdierekezi ndipo adzakuthawani.

Uziwerenga Buku la Malamuloli, uzilingalira zolembedwa mʼmenemo usana ndi usiku, kuti uchite zonse zimene zinalembedwamo. Ukamatero udzapeza bwino ndi kupambana.

Uziwerenga Buku la Malamuloli, uzilingalira zolembedwa mʼmenemo usana ndi usiku, kuti uchite zonse zimene zinalembedwamo. Ukamatero udzapeza bwino ndi kupambana.

Chenjezo pa za Chigololo

Mwana wanga, usunge malamulo a abambo ako;

ndipo usataye zimene anakuphunzitsa amayi ako.

Wosamalira malangizo amayenda mʼnjira ya moyo,

koma wonyoza chidzudzulo amasochera.

Bênçãos da obediência

A obediência abre caminho de bênçãos e prosperidade. Deus promete vida, saúde e vitória aos que andam em seus caminhos.

Madalitso Akumvera

Ngati mumvera Yehova Mulungu wanu ndi kutsatira mosamalitsa malamulo ake onse amene ndikukupatsani lero lino, Yehova Mulungu wanu adzakukwezani pamwamba pa mitundu yonse ya pa dziko lapansi.

Zikanakhala bwino akanakhala ndi mtima wondiopa ndi kusunga malamulo anga nthawi zonse kuti zinthu ziziwayendera bwino, iwowo pamodzi ndi ana awo kwamuyaya.

Muyende mʼnjira yonse imene Yehova Mulungu wanu wakulamulirani kuti mukhale ndi moyo ndi kupambana, ndi kuti masiku anu achuluke mʼdziko limene mudzatengelo.

Chifukwa chake aliyense amene aphwanya limodzi la malamulowa ngakhale lalingʼonongʼono ndi kuphunzitsa ena kuti achite chimodzimodzi, adzakhala wotsirizira mu ufumu wakumwamba, koma aliyense amene achita ndi kuphunzitsa malamulo awa adzakhala wamkulu mu ufumu wakumwamba.

Choncho, abale anga okondedwa imani njii. Musasunthike ndi chilichonse. Nthawi zonse mudzipereke kwathunthu ku ntchito ya Ambuye, chifukwa mukudziwa kuti ntchito zanu mwa Ambuye sizili zopanda phindu.

Pakuti kusamvera kwa munthu mmodzi kunasandutsa anthu ambiri kukhala ochimwa, chimodzimodzinso anthu ambiri adzasanduka olungama kudzera mwa munthu mmodzinso.

Malamulo a Mulungu anaperekedwa ndi cholinga chakuti anthu onse azindikire kuchuluka kwa machimo awo. Koma pamene machimo anachuluka, chisomo chinachuluka koposa.

Submissão e consagração

Apresentar o corpo como sacrifício vivo é o culto racional. A obediência se expressa em submissão, serviço e consagração total a Deus.

Nsembe za Moyo

Nʼchifukwa chake ine ndikukupemphani abale, mwa chifundo cha Mulungu, kuti mupereke matupi anu monga nsembe yamoyo, yopatulika ndi yokondweretsa Mulungu. Nsembeyi ndiye kupembedza kwanu kwa uzimu.

Musafanizidwenso ndi makhalidwe a dziko lino koma musandulike pokonzanso maganizo anu. Ndipo mudzadziwa ndi kuzindikira chifuniro chabwino cha Mulungu chomwe ndi chokondweretsa ndi changwiro.

Musakhale aulesi mʼmachitidwe anu. Khalani achangu mu mzimu ndipo tumikirani Ambuye.

Onse amene amatsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu ndi ana a Mulungu.

Kumvera Aulamuliro

Aliyense ayenera kumvera akulu olamulira, chifukwa palibe ulamuliro umene sunachokere kwa Mulungu. Olamulira amene alipo anayikidwa ndi Mulungu.

Kumvera Aulamuliro

Aliyense ayenera kumvera akulu olamulira, chifukwa palibe ulamuliro umene sunachokere kwa Mulungu. Olamulira amene alipo anayikidwa ndi Mulungu. Kotero kuti, iwo amene awukira ulamuliro atsutsana ndi chimene Mulungu anakhazikitsa. Ndipo amene atero adzibweretsera okha chilango.

Kuti mwachifuniro cha Mulungu ndibwere kwa inu ndi chimwemwe kuti ndidzapumule pamodzi ndi inu.

ndipo lilime lililonse livomereze kuti Yesu Khristu ndi Ambuye

kuchitira ulemu Mulungu Atate.

Monga ana omvera, musatsatenso zilakolako zoyipa zomwe munali nazo pamene munali osadziwa.

Iye anayankha kuti, "Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse ndi nzeru zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini."

Kukonda Adani

"Koma Ine ndikuwuza inu amene mukundimva: Kondani adani anu, chitirani zabwino amene amakudani. Dalitsani amene amakutembererani, apempherereni amene amakusautsani.

ndipo uzichita zimene Yehova Mulungu wako amafuna, uziyenda mʼnjira zake, uzisunga malangizo ndi malamulo ake monga momwe zinalembedwera mʼMalamulo a Mose, kuti zonse zimene udzachite zidzakuyendere bwino kulikonse kumene udzapite.

Alendo amadzipereka okha pamaso panga;

akangomva za ine amandigonjera.

Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani kuti mupite ndi kukabereka zipatso, zipatso zake za nthawi yayitali. Choncho Atate adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa.

Yehova Wamphamvuzonse akuti, "Ngati simumvera, ndipo ngati simulemekeza dzina langa mʼmitima mwanu, ndidzakutembererani ndipo madalitso onse munawalandira ndidzawatemberera. Ndithu, ndawatemberera kale, chifukwa simunalemekeze Ine mʼmitima mwanu."

Seja o primeiro
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-07-05_12-11-46-