Órfãos
Deus tem um cuidado especial pelos órfãos. Ele se apresenta como pai dos que não têm pai e defensor dos desamparados, e ordena a seu povo que faça o mesmo.
Deus, pai dos órfãos
O Senhor é pai dos órfãos e protetor das viúvas. Ele sustenta os que perderam amparo humano e cuida deles com ternura.
Imbirani Mulungu imbirani dzina lake matamando,
mukwezeni Iye amene amakwera pa mitambo;
dzina lake ndi Yehova ndipo sangalalani pamaso pake.
Atate wa ana amasiye, mtetezi wa akazi amasiye,
ndiye Mulungu amene amakhala mʼmalo oyera.
Yehova amasamalira alendo
ndipo amathandiza ana ndi akazi amasiye,
koma amasokoneza njira za anthu oyipa.
Tetezani anthu ofowoka ndi amasiye;
mukhazikitse ufulu wa anthu osauka ndi ozunzika.
Ine sindikusiyani nokha kuti mukhale ana amasiye. Ine ndidzabweranso kwa inu.
O chamado da justiça
A religião pura é visitar órfãos e viúvas em suas aflições. Deus ordena a defesa do necessitado e o cuidado com os mais frágeis.
Chipembedzo chimene Mulungu Atate athu amachivomereza kuti ndi changwiro ndi chopanda zolakwika ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto awo, ndi kudzisunga bwino kuopa kudetsedwa ndi dziko lapansi.
phunzirani kuchita zabwino!
Funafunani chilungamo,
thandizani oponderezedwa.
Tetezani ana amasiye,
muwayimirire akazi amasiye pa milandu yawo."
"Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Muziweruza molungama; muzichitirana chifundo ndi kumverana chisoni. Musamazunze akazi amasiye kapena ana amasiye, alendo kapena osauka. Musamaganizirane zoyipa mʼmitima mwanu.’
"Musazunze mkazi wamasiye kapena mwana wamasiye. Ngati muwazunza ndipo iwo nʼkulirira kwa Ine, ndidzamva kulira kwawo. Ine ndidzakukwiyirani ndipo ndidzakuphani ndi lupanga. Akazi anu adzakhala amasiye ndiponso ana anu adzakhala wopanda abambo.
chifukwa ndinkapulumutsa mʼmphawi wofuna chithandizo,
ndiponso mwana wamasiye amene analibe aliyense womuthandiza.
Munthu amene anali pafupi kufa ankandidalitsa;
ndinkasangalatsanso mkazi wamasiye.