Orgulho
O orgulho é um dos pecados mais condenados na Bíblia. Deus resiste aos soberbos, mas dá graça aos humildes. A humildade é o caminho da honra verdadeira.
Deus resiste ao soberbo
A soberba precede a ruína e o orgulho antecede a queda. Deus abomina o coração altivo e promete humilhar quem se exalta.
Kunyada kumafikitsa ku chiwonongeko,
ndipo munthu wodzikuza adzagwa.
Munthu aliyense wodzikuza amamunyansa Yehova.
Koma dziwani izi: Iwo sadzakhala osalangidwa.
Pali njira ina yooneka ngati yowongoka kwa munthu
koma kumatsiriziro kwake ndi imfa.
Kuopa Yehova ndiko kudana ndi zoyipa.
Ine ndimadana ndi kunyada, kudzitama,
kuchita zoyipa, ndiponso kuyankhula zonyenga.
Kunyada kukalowa, pamafikanso manyazi,
koma pamene pali kudzichepetsa pameneponso pali nzeru.
Kunyada kukalowa, pamafikanso manyazi,
koma pamene pali kudzichepetsa pameneponso pali nzeru.
Kunyada kwa munthu kudzamutsitsa,
koma munthu wodzichepetsa amalandira ulemu.
Kunyada kwa munthu kudzamutsitsa,
koma munthu wodzichepetsa amalandira ulemu.
Chiwonongeko chisanafike, mtima wa munthu umakhala wonyada,
koma ulemu umatsatira kudzichepetsa.
Chiwonongeko chisanafike, mtima wa munthu umakhala wonyada,
koma ulemu umatsatira kudzichepetsa.
Yehova amapasula nyumba ya munthu wonyada
koma amasamalira malo a mkazi wamasiye.
Humildade como caminho
Humilhai-vos diante do Senhor e Ele vos exaltará. A grandeza no Reino vem pelo serviço humilde, não pela autopromoção.
Koma amatipatsa chisomo chochuluka. Nʼchifukwa chake Malemba amati,
"Mulungu amatsutsa odzikuza,
koma apereka chisomo kwa odzichepetsa."
Dzichepetseni pamaso pa Ambuye ndipo Iye adzakukwezani.
Abale omwe ndi anthu wamba anyadire pamene akwezedwa. Koma olemera anyadire pamene atsitsidwa, chifukwa adzatha ngati duwa lakuthengo.
Momwemonso, inu anyamata gonjerani amene ndi akulu. Inu nonse mukhale odzichepetsa kuti mutumikirane, chifukwa,
"Mulungu amatsutsana nawo odzikuza,
koma amapereka chisomo kwa odzichepetsa."
Choncho, mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthawi yake adzakukwezeni. Tayani pa Iye nkhawa zanu zonse chifukwa ndiye amakusamalani.
Pakuti aliyense wodzikuza adzamuchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamukweza."
Musachite kalikonse ndi mtima odzikonda chabe kapena odzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa ndipo aliyense aziona mnzake ngati womuposa iyeyo. Musamangofuna zokomera inu nokha koma aliyense azifuna zokomeranso ena.
Pa ubale wanu wina ndi mnzake, mukhale ndi mtima wofanana ndi wa Khristu Yesu:
Os perigos do orgulho
O orgulho cega, gera contendas e afasta de Deus. A Escritura adverte contra a soberba da vida e a vã glória mundana.
Pakuti zonse za mʼdziko lapansi, zilakolako za thupi, zinthu zimene maso amakhumbira ndiponso kuyandikira zinthu za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi.
Choncho, ngati mukuganiza kuti mwayima mwamphamvu, samalani mungagwe!
Ngati ndipereka zanga zonse kwa osauka ndi kupereka thupi langa kuti alitenthe, koma ngati ndilibe chikondi, ine sindipindula kanthu.
Anasankha zinthu zapansipansi ndi zopeputsidwa za dziko la pansi lino, zinthu zimene kulibe, kuti asukulutse zimene zilipo, kuti munthu asanyade pamaso pa Mulungu.
Koma, "Ngati munthu akufuna kunyadira, anyadire mwa Ambuye." Pakuti munthu amene amavomerezedwa, si amene amadziyenereza yekha, koma munthu amene Ambuye amuyenereza.
Anapitiriza kuti, "Chimene chichokera mwa munthu ndi chomwe chimamudetsa. Pakuti kuchokera mʼkati mwa mitima ya anthu, mumatuluka maganizo oyipa, chiwerewere, kuba, kupha, chigololo, dyera, nkhwidzi, chinyengo, machitidwe onyansa, kaduka, chipongwe, kudzikuza ndi kupusa. Zoyipa zonsezi zimatuluka mʼkati ndipo zimadetsa munthu."
Chipongwe chosamalabadirako za anthu ena chimadzetsa mikangano,
koma womva malangizo a anzawo ndiwo ali ndi nzeru.
Mphotho ya munthu wodzichepetsa
ndi woopa Yehova ndi chuma, ulemu ndi moyo.
Za Kudalira Chuma
Anthu onse amene ali ndi chuma uwalamule kuti asanyade kapena kuyika mitima yawo pa chuma chimene nʼchosadalirika. Koma chiyembekezo chawo chikhale mwa Mulungu amene amatipatsa mowolowamanja zonse zotisangalatsa.
O olhar de Deus
O Senhor não olha como o homem. Ele vê o coração e se agrada dos quebrantados de espírito e dos que tremem diante da sua Palavra.
Koma Yehova anati kwa Samueli, "Usaone maonekedwe ake kapena msinkhu wake, pakuti ndamukana iyeyu. Yehova sapenya zimene munthu amapenya. Anthu amapenya zakunja, koma Mulungu amapenya za mu mtima."
"Musandiyankhulenso modzitama,
pakamwa panu pasatuluke zonyada,
pakuti Yehova ndi Mulungu wanzeru,
ndipo ndiye amene amayesa ntchito za anthu onse.
Kodi si manja anga amene anapanga zinthu zonsezi,
motero zonsezi ndi zanga?"
Akutero Yehova.
"Koma munthu amene ndimakondwera naye ndi uyu:
amene ali wodzichepetsa ndi wosweka mtima,
ndipo amamvera mawu anga.
Tsopano ine Nebukadinezara, ndikutamanda, kukweza ndi kulemekeza Mfumu yakumwamba chifukwa zonse zimene amachita ndi zoyenera ndipo njira zake zonse ndi zachilungamo. Ndipo onse amene amayenda modzikuza adzawatsitsa.
Mfumu ya Israeli inayankha kuti, "Kamuwuzeni kuti, ‘Mwamuna mnzako nʼpachulu, nʼkulinga utakwerapo.’ "
Muyanjane wina ndi mnzake. Musakhale onyada, koma lolani kuyanjana ndi anthu wamba. Musaganize kuti mumadziwa zonse.
Koma chipatso cha Mzimu Woyera ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndi kudziretsa. Palibe lamulo loletsa zimenezi.