Pai da mentira
A Bíblia revela que o diabo é o pai da mentira. Ele engana, acusa e tenta destruir. Mas Cristo veio para desfazer as obras do maligno e nos dar vitória.
O caráter do diabo
Jesus disse que o diabo é mentiroso e homicida desde o princípio. Não há verdade nele — a mentira é sua natureza.
Inu ndinu ana a mdierekezi. Iye ndiye abambo anu ndipo mukufuna kuchita zimene abambo anuwo amakhumba. Iye anali wakupha kuyambira pachiyambi, sanasunge choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene Iye anena bodza, amayankhula chiyankhulo chobadwa nacho, popeza ndi wabodza ndipo ndi bambo wa mabodza.
Atayamba kudya mgonero, mdierekezi anali atalowa kale mu mtima wa Yudasi Isikarioti mwana wa Simoni, kuti amupereke Yesu.
Chinjoka chachikulu chija chinagwetsedwa pansi. Ichocho ndiye njoka yakalekale ija yotchedwa Mdierekezi kapena Satana, amene amasocheretsa anthu a pa dziko lonse lapansi. Chinaponyedwa pa dziko la pansi pamodzi ndi angelo ake.
Kenaka ndinamva mawu ofuwula kumwamba akunena kuti,
"Tsopano chipulumutso, mphamvu,
ufumu wa Mulungu wathu
ndi ulamuliro wa Khristu wake zabwera.
Pakuti woneneza abale athu uja,
amene amangokhalira kuwaneneza pamaso pa Mulungu usana ndi usiku,
wagwetsedwa pansi.
Sizododometsa zimenezi, pakuti Satana mwini amadzizimbayitsa kuoneka ngati mngelo wowunikira anthu.
Mulungu wa dziko lapansi anachititsa khungu anthu osakhulupirira, kuti asathe kuona kuwala kwa Uthenga Wabwino umene umaonetsa ulemerero wa Khristu, amene ndi chifaniziro cha Mulungu.
As obras do inimigo
O diabo rouba a Palavra semeada, cega o entendimento dos incrédulos e anda em derredor como leão rugidor buscando a quem devorar.
Pamene aliyense akumva uthenga wa ufumu koma sawuzindikira, woyipayo amabwera ndi kuchotsa zimene zafesedwa mu mtima mwake. Iyi ndi mbewu yofesedwa mʼmbali mwa njira.
Munda ndi dziko lapansi ndipo mbewu yabwino ndi ana a ufumu. Namsongole ndi ana a woyipayo. Ndipo amene anafesa namsongole ndi Satana. Kukolola ndiko kutha kwa dzikoli ndipo otuta ndi angelo.
Khalani odziretsa ndi atcheru. Mdani wanu mdierekezi amayendayenda monga mkango wobangula kufunafuna wina kuti amumeze.
Woyipitsitsayo adzabwera ndi mphamvu za Satana. Adzaonetsa mphamvu zake pochita zizindikiro ndi zodabwitsa zachinyengo.
Ine sindiyankhulanso nanu zambiri nthawi yayitali popeza wolamulira dziko lapansi akubwera. Iye alibe mphamvu pa Ine,
Vitória em Cristo
Cristo apareceu para destruir as obras do diabo. Quem está em Deus é protegido, e o maligno não o toca.
Iye amene amachimwa ndi wa Satana, chifukwa mdierekezi wakhala akuchimwa kuyambira pa chiyambi. Mwana wa Mulungu anaonekera kuti awononge ntchito za mdierekezi.
Tikudziwa kuti aliyense amene ndi mwana wa Mulungu sachimwirachimwirabe. Yesu, Mwana wa Mulungu, amamusunga ndipo woyipa uja sangamukhudze. Tikudziwa kuti ndife ana a Mulungu ndi kuti dziko lonse lapansi lili pansi pa ulamuliro wa woyipayo.
kuti ukatsekule maso awo kuti atembenuke mtima kuchoka ku mdima ndi kulowa mʼkuwala, kuchoka ku mphamvu za Satana ndi kupita kwa Mulungu, kuti alandire chikhululukiro cha machimo awo ndi kukhala mʼgulu la amene akuyeretsedwa chifukwa chokhulupirira Ine.
Ndipo Mdierekezi amene anawanyenga, anaponyedwa mʼnyanja ya sulufule wotentha, kumene kunaponyedwa chirombo chija ndi mneneri wonama uja. Iwo adzazunzika usiku ndi usana kwamuyaya.
Dziperekeni nokha kwa Mulungu. Mukaneni Mdierekezi ndipo adzakuthawani.
Yesu anayankha kuti, "Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate popanda kudzera mwa Ine.