Pais
Deus é nosso Pai celestial — amoroso, provedor, disciplinador e fiel. As Escrituras também honram os pais terrenos e os chamam a criar os filhos na instrução do Senhor.
O Pai celestial
Deus é Pai de misericórdias. Ele nos adotou como filhos, nos ama incondicionalmente e cuida de cada detalhe da nossa vida.
Taonani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate anatikonda nacho, kuti titchedwe ana a Mulungu! Ndipo nʼchimene ife tili! Nʼchifukwa chake dziko lapansi silitidziwa chifukwa silinamudziwe Iye.
Taonani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate anatikonda nacho, kuti titchedwe ana a Mulungu! Ndipo nʼchimene ife tili! Nʼchifukwa chake dziko lapansi silitidziwa chifukwa silinamudziwe Iye.
Mzimu amene inu munalandira samakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha, koma Mzimu amakusandutsani ana. Ndipo mwa Iye ife timafuwula kuti, "Abba, Atate." Mzimu mwini amavomerezana ndi mzimu wathu kuti ife ndife ana a Mulungu.
Koma kwa onse amene anamulandira Iye, kwa amene anakhulupirira mʼdzina lake, Iye anawapatsa mphamvu yokhala ana a Mulungu;
Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale nanu.
Monga bambo amachitira chifundo ana ake,
choncho Yehova ali ndi chifundo ndi iwo amene amamuopa;
Monga bambo amachitira chifundo ana ake,
choncho Yehova ali ndi chifundo ndi iwo amene amamuopa;
pakuti Iye amadziwa momwe tinawumbidwira,
amakumbukira kuti ndife fumbi.
Atate wa ana amasiye, mtetezi wa akazi amasiye,
ndiye Mulungu amene amakhala mʼmalo oyera.
Komabe, Inu Yehova ndinu Atate athu.
Ife ndife chowumba, Inu ndinu wowumba;
ife tonse ndi ntchito ya manja anu.
Koma Inu ndinu Atate athu,
ngakhale Abrahamu satidziwa
kapena Israeli kutivomereza ife;
Inu Yehova, ndinu Atate athu,
kuyambira kale dzina lanu ndinu Mpulumutsi wathu.
Chifukwa mwana watibadwira,
mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife,
ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake.
Ndipo adzamutcha dzina lake lakuti
Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu,
Atate Amuyaya, ndi Mfumu ya Mtendere.
Chifukwa mwana watibadwira,
mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife,
ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake.
Ndipo adzamutcha dzina lake lakuti
Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu,
Atate Amuyaya, ndi Mfumu ya Mtendere.
O cuidado paterno de Deus
O Pai celestial sabe do que precisamos antes de pedirmos. Ele dá boas dádivas aos filhos que pedem e cuida até dos passarinhos.
Onani mbalame zamlengalenga sizifesa kapena kukolola kapena kusunga mʼnkhokwe komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Kodi inu simuziposa kwambiri?
Kodi suja amagulitsa mbalame ziwiri ndi ndalama imodzi? Koma palibe imodzi ya izo imene idzagwa pansi wopanda chifuniro cha Atate anu. Ndipo ngakhale tsitsi la mʼmutu mwanu linawerengedwa kale. Potero musaope; inu ndinu a mtengo woposa mbalame zambiri.
Koma pamene mupemphera, lowani mʼchipinda chanu chamʼkati, ndi kutseka chitseko ndipo mupemphere kwa Atate anu amene saoneka. Ndipo Atate anu, amene amaona zochitika mseri, adzakupatsani mphotho.
Koma pamene ukusala kudya, samba mʼmaso nudzole mafuta kumutu, kuti usaonekere kwa anthu kuti ukusala kudya koma kwa Atate ako ali mseri; ndipo Atate ako amene amaona za mseri adzakupatsa mphotho.
"Ndani mwa inu abambo, kodi mwana wanu atapempha nsomba, mʼmalo mwake mungamupatse njoka? Kapena atapempha dzira, kodi mungamupatse chinkhanira? Tsono ngati inu, anthu oyipa, mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, koposa kotani Atate anu akumwamba, angalephere bwanji kupereka Mzimu Woyera kwa amene awapempha!"
Chuma cha Kumwamba
"Musachite mantha, inu kagulu kankhosa, pakuti zinakondweretsa Atate anu kuti akupatseni ufumu.
Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba, kwa Atate mwini kuwala, amene sasintha ngati mthunzi woyendayenda.
Iye amene sanatimane Mwana wake wa Iye yekha, koma anamupereka chifukwa cha ife tonse. Iye adzalekeranjinso pamodzi naye kutipatsa ife zinthu zonse mwaulere?
Conhecer o Pai
Jesus é o caminho para o Pai. Ninguém conhece o Pai senão o Filho e aquele a quem o Filho quiser revelar.
Yesu anayankha kuti, "Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate popanda kudzera mwa Ine.
Mʼnyumba mwa Atate anga muli zipinda zambiri. Kukanakhala kuti mulibemo ndikanakuwuzani. Ine ndikupita kumeneko kukakukonzerani malo.
Ndipo Ine ndidzachita chilichonse chimene inu mudzapempha mʼdzina langa kuti Atate alemekezedwe mwa Mwana.
Iye amene amadziwa malamulo anga ndi kuwasunga ndiye amene amandikonda. Wokonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga ndipo Inenso ndidzamukonda ndikudzionetsa ndekha kwa iye."
Yesu anamuyankha kuti, "Ngati wina aliyense andikonda Ine, adzasunga mawu anga. Atate wanga adzamukonda, ndipo Ife tidzabwera ndi kukhala naye.
Palibe munthu amene anaona Mulungu, koma Mwana mmodzi yekhayo amene ali wa pamtima pa Atate, ndiye anafotokoza za Iye.
Ine ndimazipatsa moyo wosatha ndipo sizidzawonongeka. Palibe amene adzazikwatula mʼdzanja langa. Atate anga, amene anandipatsa Ine, ndi akulu kuposa onse. Palibe amene angazikwatule mʼdzanja la Atate anga. Ine ndi Atate ndife amodzi."
"Atate, Ine ndikufuna kuti anthu amene mwandipatsa Ine adzakhale ndi Ine kumene kuli Ine, ndi kuona ulemerero wanga, ulemerero umene munandipatsa chifukwa Inu munandikonda dziko lapansi lisanalengedwe.
"Zinthu zonse zapatsidwa kwa Ine ndi Atate anga. Palibe mmodzi amene adziwa Mwana kupatula Atate ndipo palibe mmodzi amene adziwa Atate kupatula Mwana ndi kwa iwo amene Mwana awasankha kuwawululira.
Nʼchifukwa chake, inu khalani angwiro monga Atate anu akumwamba ali wangwiro."
"Koma inu simuyenera kutchulidwa ‘Aphunzitsi,’ popeza muli naye Mbuye mmodzi ndipo inu nonse ndinu abale. Ndipo musamatchule wina aliyense pansi pano kuti ‘Atate,’ pakuti muli ndi Atate mmodzi, ndipo ali kumwamba.
Kodi mukuganiza kuti sindingathe kupempha Atate anga ndipo nthawi yomweyo nʼkundipatsa magulu a angelo oposa khumi ndi awiri?
Khalani achifundo, monga momwe Atate anu ali achifundo."
Kwa Mulungu ndi Atate athu, kukhale ulemerero mpaka muyaya. Ameni.
Disciplina e amor paterno
O Pai disciplina os filhos que ama. A correção divina produz fruto de justiça e paz para aqueles que foram exercitados por ela.
Pamene mukupirira masautso monga chilango, Mulungu achitira inu monga ana ake. Kodi ndi mwana wotani amene abambo ake samulanga? Ngati inu simulangidwa, komatu aliyense amalangidwa, ndiye kuti sindinu ana enieni koma amʼchigololo. Komanso, tonsefe tinali ndi abambo athu otibala amene amatilanga ndipo timawapatsa ulemu. Nanga kodi sitidzagonjera Atate a mizimu yathu kuti tikhale ndi moyo? Abambo athu ankatilanga kwa kanthawi kochepa monga amaonera kufunika kwake, koma Mulungu amatilanga kuti tipindule, kuti tikhale oyera mtima.
Mwana wanga usanyoze malangizo a Yehova,
ndipo usayipidwe ndi chidzudzulo chake.
Paja Yehova amadzudzula amene amamukonda,
monga abambo achitira mwana amene amakondwera naye.
Mwana wanga usanyoze malangizo a Yehova,
ndipo usayipidwe ndi chidzudzulo chake.
Paja Yehova amadzudzula amene amamukonda,
monga abambo achitira mwana amene amakondwera naye.
Pais terrenos
A Bíblia honra os pais que criam os filhos nos caminhos de Deus. Honrar pai e mãe é mandamento com promessa de vida longa.
Ana ndi Makolo Awo
Inu ana, mverani makolo anu mwa Ambuye, pakuti zimenezi ndi zoyenera. "Lemekeza abambo ndi amayi ako." Limeneli ndi lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo. Ngati ulemekeza abambo ako ndi amayi ako, "zinthu zidzakuyendera bwino ndipo udzasangalala ndi moyo wautali pa dziko lapansi." Abambo musakwiyitse ana anu; mʼmalo mwake, muwalere mʼchiphunzitso ndi mʼchilangizo cha Ambuye.
Abambo musakwiyitse ana anu; mʼmalo mwake, muwalere mʼchiphunzitso ndi mʼchilangizo cha Ambuye.
"Lemekeza abambo ako ndi amayi ako kuti ukhale ndi moyo wautali mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.
Malangizo kuti Asunge Nzeru
Malangizo kwa Achinyamata
Mwana wanga, mvera malangizo a abambo ako
ndipo usakane mawu okuwongolera a amayi ako.
Ali ngati sangamutu yokongola ya maluwa pamutu pako
ndiponso ali ngati mkanda mʼkhosi mwako.
Abambo a munthu wolungama ali ndi chimwemwe chachikulu;
Wobala mwana wanzeru adzakondwera naye.
Chitsiru chimanyoza mwambo wa abambo ake,
koma wochenjera amasamala chidzudzulo.
Zidzukulu ndiye ulemu wa anthu okalamba,
ndipo makolo ndiye ulemerero wa ana.
Ngati munthu atemberera abambo ake kapena amayi ake,
moyo wake udzazimitsidwa ngati nyale mu mdima wandiweyani.
Inu ana, mverani makolo anu mu zonse pakuti izi zimakondweretsa Ambuye.
Inu abambo, musakwiyitse ana anu, kuti angataye mtima.
Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova,
ana ndi mphotho yochokera kwa Iye.
Ana a pa unyamata ali ngati mivi mʼmanja
mwa munthu wankhondo.
Wodala munthu
amene motengera mivi mwake mwadzaza.
Iwo sadzachititsidwa manyazi
pamene alimbana ndi adani awo pa zipata.
Amoyo, amoyo okha ndiwo amakutamandani,
monga mmene ndikuchitira ine lero lino;
abambo amawuza ana awo za
kukhulupirika kwanu.
Makolo asaphedwe chifukwa cha ana awo, ndipo ana asaphedwe chifukwa cha makolo awo, koma aliyense ayenera kufa chifukwa cha zolakwa zake.
Pakuti chilengedwe chikudikira ndi chiyembekezo kuonetsedwa poyera kwa ana a Mulungu.
Inu abambo, ndikukulemberani
popeza kuti munamudziwa Iye amene analipo kuyambira pachiyambi.
Inu anyamata, ndikukulemberani
popeza kuti munagonjetsa woyipayo.
Ana okondedwa, ndikukulemberani
chifukwa mumawadziwa Atate.
Abambo, ndikukulemberani
chifukwa munamudziwa Iye amene analipo kuyambira pachiyambi.
Inu anyamata, ndikukulemberani
chifukwa ndinu amphamvu.
Mawu a Mulungu amakhala mwa inu
ndipo mumamugonjetsa woyipayo.
Musakonde Dziko Lapansi
Musamakonde dziko lapansi kapena chilichonse cha dziko lapansi. Ngati munthu wina aliyense akonda dziko lapansi, mwa iyeyo mulibe chikondi chokonda Atate.