O pão da vida
Jesus se declarou o Pão da Vida — o alimento espiritual que satisfaz a fome mais profunda da alma humana. Quem come deste pão viverá para sempre.
Eu sou o Pão da Vida
Jesus disse: 'Eu sou o pão da vida; quem vem a mim nunca terá fome.' Ele é o sustento que sacia a alma eternamente.
Kenaka Yesu ananenetsa kuti, "Ine ndine chakudya chamoyo. Iye amene abwera kwa Ine sadzamva njala, ndipo iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu.
Ine ndine chakudya chamoyo.
Pamenepo Ayuda anayamba kungʼungʼudza chifukwa anati, "Ine ndine chakudya chotsika kuchokera kumwamba."
Gwirani ntchito, osati chifukwa cha chakudya chimene chimawonongeka koma chifukwa cha chakudya chimene sichiwonongeka mpaka ku moyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani. Mulungu Atate anamusindikiza chizindikiro chomuvomereza."
O pão que dá vida ao mundo
Jesus é o pão vivo que desceu do céu. Quem come da sua carne e bebe do seu sangue tem a vida eterna e será ressuscitado no último dia.
Ine ndine chakudya chamoyo chochokera kumwamba. Ngati munthu adya chakudya ichi, adzakhala ndi moyo nthawi zonse. Chakudya chimenechi ndi thupi langa, limene Ine ndidzalipereka kuti anthu pa dziko lapansi akhale ndi moyo."
Yesu anawawuza kuti, "Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti ngati simungadye thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa magazi ake, simungakhale ndi moyo mwa inu.
Yesu anayankha kuti, "Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate popanda kudzera mwa Ine.
Saciar a fome da alma
Bem-aventurados os que têm fome e sede de justiça, porque serão fartos. Nem só de pão vive o homem, mas de toda palavra que sai da boca de Deus.
Odala ndi amene akumva njala ndi ludzu la chilungamo,
chifukwa adzakhutitsidwa.
Yesu anayankha kuti, "Zalembedwa, ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Mulungu.’ "
Musade Nkhawa
"Nʼchifukwa chake ndikuwuzani kuti musadere nkhawa za moyo wanu kuti mudzadya chiyani kapena mudzamwa chiyani; kapenanso za thupi lanu kuti mudzavala chiyani. Kodi moyo suposa chakudya? Kodi thupi siliposa zovala? Onani mbalame zamlengalenga sizifesa kapena kukolola kapena kusunga mʼnkhokwe komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Kodi inu simuziposa kwambiri?