Pão
O pão é símbolo central na Bíblia: do maná no deserto ao pão da vida — Jesus. A Escritura usa o pão para ensinar sobre provisão divina, comunhão e dependência espiritual.
O maná do céu
Deus alimentou Israel no deserto com pão do céu. O maná era diário, fiel e suficiente — retrato da provisão constante de Deus.
Yehova anati kwa Mose, "Ine ndamva kudandaula kwa Aisraeli. Awuze kuti, ‘Madzulo mudzadya nyama ndipo mmawa mudzakhuta buledi. Pamenepo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ "
Madzulo amenewo panatuluka zinziri zimene zinali ponseponse pa misasa yawo, ndipo mmawa panali mame kuzungulira misasa yawo. Mamewo atachoka, pa nthaka mʼchipululumo panaoneka tinthu tina topyapyala komanso totuwa ngati chipale. Aisraeli atationa anafunsana wina ndi mnzake nati, "Kodi timeneti nʼchiyani?" Popeza sanatidziwe.
Mose anawawuza kuti, "Uyu ndi buledi amene Yehova wakupatsani kuti mudye.
Aisraeli anatchula chakudyacho Mana. Chakudyacho chinkaoneka ngati mbewu zamapira, zoyera. Ndipo chinkakoma ngati chothira uchi.
Komabe Iye anapereka lamulo kwa mitambo mmwamba
ndi kutsekula makomo a mayiko akumwamba;
anagwetsa mana kuti anthu adye,
anawapatsa tirigu wakumwamba.
Anthu anadya buledi wa angelo,
Iye anawatumizira chakudya chonse chimene akanatha kudya.
Amameretsa udzu kuti ngʼombe zidye,
ndi zomera, kuti munthu azilima
kubweretsa chakudya kuchokera mʼdziko lapansi:
vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu,
mafuta amene amachititsa nkhope yake kuwala,
ndi buledi amene amapereka mphamvu.
O pão da vida
Jesus declarou: 'Eu sou o pão da vida.' Quem vem a Ele nunca terá fome, e quem nele crê jamais terá sede. Ele é o sustento eterno.
Yesu anawawuza kuti, "Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti si Mose amene ankakupatsani chakudya chochokera kumwamba, koma ndi Atate anga amene ankakupatsani chakudya chenicheni chochokera kumwamba. Pakuti chakudya cha Mulungu ndi Iye amene wabwera kuchokera kumwamba ndi kupereka moyo ku dziko la pansi."
Iwo anati, "Ambuye, kuyambira tsopano muzitipatsa buledi ameneyu."
Kenaka Yesu ananenetsa kuti, "Ine ndine chakudya chamoyo. Iye amene abwera kwa Ine sadzamva njala, ndipo iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu.
Ine ndine chakudya chamoyo. Makolo anu akale anadya mana mʼchipululu, komabe anafa. Koma pano pali chakudya chochokera kumwamba, chimene munthu akadya sangafe. Ine ndine chakudya chamoyo chochokera kumwamba. Ngati munthu adya chakudya ichi, adzakhala ndi moyo nthawi zonse. Chakudya chimenechi ndi thupi langa, limene Ine ndidzalipereka kuti anthu pa dziko lapansi akhale ndi moyo."
Iye anakutsitsani nakumvetsani njala kenaka nʼkukudyetsani mana amene anali osadziwika kwa inu kapena makolo anu, kuti akuphunzitseni kuti munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Yehova.
Yesu anayankha kuti, "Zalembedwa, ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Mulungu.’ "
Partilha e comunhão
O partir do pão une o corpo de Cristo. Na Ceia, na generosidade e na partilha, expressamos a comunhão com Deus e uns com os outros.
Ndipo Iye anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema, nagawira iwo nati, "Ili ndi thupi langa lomwe laperekedwa kwa inu; muzichita zimenezi pokumbukira Ine."
Pakuti nthawi zonse pamene mudya bulediyu ndikumwa chikhochi, mukulalikira imfa ya Ambuye mpaka Iye adzabweranso.
Pamene tidalitsa chikho cha Mgonero wa Ambuye, mothokoza Mulungu, kodi sitikugawana magazi a Khristu? Nanga buledi amene timanyemayo, kodi sitikugawana thupi la Khristu? Pakuti buledi ndi mmodzi yekha, ifenso ngakhale tili ambiri, ndife thupi limodzi, popeza tonse timagawana buledi mmodzi yemweyo.
"Chifukwa chake pempherani motere:
" ‘Atate athu akumwamba,
dzina lanu lilemekezedwe,
Ufumu wanu ubwere,
chifuniro chanu chichitike
pansi pano monga kumwamba.
Mutipatse chakudya chathu chalero.
Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsika,
pakuti iye amagawana chakudya chake ndi anthu osauka.
Koma Iye anayankha kuti, "Apatseni kanthu koti adye."
Iwo anati kwa Iye, "Apa pafunika ndalama za miyezi isanu ndi itatu zomwe munthu amalandira! Kodi tipite kukagwiritsa ntchito ndalama zotere kugulira buledi kuti tiwapatse adye?"
Iye anawafunsa kuti, "Muli ndi malofu a buledi angati? Pitani mukaone."
Ataona anati kwa Iye, "Asanu ndi nsomba ziwiri."
Pamenepo Yesu anawalamulira kuti awakhazike anthu pansi mʼmagulu pa msipu obiriwira. Ndipo anakhala pansi mʼmagulu a anthu 100 ndi gulu la anthu makumi asanu. Atatenga malofu a buledi asanu ndi nsomba ziwiri, nayangʼana kumwamba, Iye anayamika nagawa malofu a bulediwo. Kenaka anawapatsa ophunzira ake kuti awapatse anthu. Ndipo anagawanso nsomba ziwirizo kwa onse. Onse anadya ndipo anakhuta, ndipo ophunzira ake anatola buledi ndi nsomba zotsalira zokwanira madengu khumi ndi awiri.
Provisão divina
O justo não é desamparado e seus descendentes não mendigam pão. Deus provê com fidelidade o alimento de cada dia.
Ine ndinali wamngʼono ndipo tsopano ndakalamba
koma sindinaonepo olungama akusiyidwa
kapena ana awo akupempha chakudya.
Yisiti wa Afarisi ndi Asaduki
Koma atawoloka nyanja, ophunzira anayiwala kutenga buledi. Yesu anawawuza kuti, "Chenjerani, khalani tcheru ndi yisiti wa Afarisi ndi Asaduki."
Iwo anakambirana pakati pawo za izi ndipo anati, "Ichi nʼchifukwa chakuti sitinatenge buledi aliyense."
Yesu atadziwa zokambirana zawo, anawafunsa kuti, "Chifukwa chiyani mukukambirana zakuti, ‘mulibe buledi?’ Inu achikhulupiriro chochepa. Kodi inu simukumvetsetsabe? Kodi simukukumbukira za buledi musanu amene anadya anthu 5,000 ndi madengu amene munadzaza? Kapena buledi musanu ndi muwiri amene anadya anthu 4,000, nanga ndi madengu angati amene munadzaza? Zitheka bwanji kuti inu simukumvetsetsa kuti Ine sindinkayankhula nanu za buledi? Koma inu chenjerani ndi yisiti wa Afarisi ndi Asaduki." Kenaka iwo anazindikira kuti Iye samawawuza kuti achenjere ndi yisiti wa buledi koma ndi chiphunzitso cha Afarisi ndi Asaduki.
Kuponya Chakudya pa Madzi
Ponya chakudya chako pa madzi,
udzachipezanso patapita masiku ambiri.
Ndalama zako uzisungitse kwa anthu asanu ndi awiri, inde kwa anthu asanu ndi atatu,
pakuti sudziwa ndi tsoka lanji limene likubwera pa dziko.