Pular para o conteúdo
Publicidade

O papel da mulher

Por Bíblia Online

A Bíblia honra a mulher como colaboradora essencial no plano de Deus. De Provérbios 31 às mulheres do Novo Testamento, a Escritura celebra a sabedoria, a força e a fé feminina.

A mulher virtuosa

Mulher virtuosa, quem a achará? Seu valor excede o de rubis. Ela é sábia, trabalhadora, generosa e temida pelo Senhor.

Mathero: Mkazi Wangwiro

Kodi mkazi wangwiro angathe kumupeza ndani?

Ndi wokwera mtengo kuposa miyala yamtengowapatali.

Mtima wa mwamuna wake umamukhulupirira

ndipo mwamunayo sasowa phindu.

Masiku onse a moyo wake

mkaziyo amachitira mwamuna wake zabwino zokhazokha osati zoyipa.

Iye amafunafuna ubweya ndi thonje;

amagwira ntchito ndi manja ake mwaufulu.

Iye ali ngati sitima zapamadzi za anthu amalonda,

amakatenga chakudya chake kutali.

Iye amadzuka kusanache kwenikweni;

ndi kuyamba kukonzera a pa banja pake chakudya

ndi kuwagawira ntchito atsikana ake antchito.

Iye amalingalira za munda ndi kuwugula;

ndi ndalama zimene wazipeza amalima munda wamphesa.

Iye amavala zilimbe

nagwira ntchito mwamphamvu ndi manja ake.

Iye amaona kuti malonda ake ndi aphindu,

choncho nyale yake sizima usiku wonse.

Iye amadzilukira thonje

ndipo yekha amagwira chowombera nsalu.

Iye amachitira chifundo anthu osauka

ndipo amapereka chithandizo kwa anthu osowa.

Iye amasoka nsalu zabafuta nazigulitsa;

amaperekanso mipango kwa anthu amalonda.

Mphamvu ndi ulemu zimakhala ngati chovala chake;

ndipo amaseka osaopa zamʼtsogolo.

Iye amayankhula mwanzeru,

amaphunzitsa anthu mwachikondi.

Iye amayangʼanira makhalidwe a anthu a pa banja lake

ndipo sachita ulesi ndi pangʼono pomwe.

Mkazi wanzeru amamanga banja lake,

koma mkazi wopusa amalimasula ndi manja ake omwe.

Malangizo kuti Asunge Nzeru

Malangizo kwa Achinyamata

Mwana wanga, mvera malangizo a abambo ako

ndipo usakane mawu okuwongolera a amayi ako.

Beleza interior

A beleza verdadeira não é exterior, mas o caráter incorruptível de um espírito manso e tranquilo. Isso tem grande valor diante de Deus.

Akazi ndi Amuna

Momwemonso, akazi inu gonjerani amuna anu kuti ngati ena a iwo sakhulupirira Mawu a Mulungu, akopeke ndi makhalidwe a akazi awo ndipo sipadzafunikanso mawu pamene aona moyo wanu wachiyero ndi moyo woopa Mulungu. Kudzikongoletsa kwanu kusakhale kwa maonekedwe akunja, monga kuluka tsitsi ndi kuvala zokometsera zagolide ndi zovala zamberewere. Mʼmalo mwake kudzikongoletsa kwanu kukhale kwa munthu wa mʼkatimo, kukongola kosatha kwa mtima ofatsa ndi mzimu wachete, zimene ndi za mtengowapatali pamaso pa Mulungu. Pakuti umo ndi mmene akazi oyera mtima akale amene anali ndi chiyembekezo pa Mulungu anadzikongoletsera. Iwo ankagonjera amuna awo, monga Sara, amene anamvera Abrahamu namutcha iye mbuye wake. Akazi inu ndinu ana ake ngati muchita zoyenera, ndipo musaope choopsa chilichonse.

Momwemonso amuna inu, khalani mwanzeru ndi akazi anu, ndipo muwachitire ulemu monga anzanu ofowoka ndiponso olandira nanu pamodzi mphatso ya moyo wosatha, kuti pasakhale kanthu kotsekereza mapemphero anu.

Ndikufunanso kuti amayi azivala mwaulemu, modzilemekeza ndi moyenera. Adzikongoletse koma osati ndi tsitsi loluka mowonjeza muyeso kapena zokongoletsa zagolide kapena mikanda yamtengowapatali kapena ndi zovala zamtengowapatali.

Momwemonso, akazi akhale olemekezeka, osasinjirira koma oganiza bwino ndi odalirika pa chilichonse.

Parceria e dignidade

Deus criou homem e mulher à sua imagem. A mulher não é inferior, mas parceira e co-herdeira da graça da vida.

Ndipo Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake.

Anawalengadi mʼchifanizo cha Mulungu;

analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.

Mulungu anawadalitsa nati kwa iwo, "Muberekane, muchulukane, mudzaze dziko lapansi ndipo muligonjetse. Mulamulire nsomba zamʼnyanja, mbalame zamlengalenga ndi cholengedwa chamoyo chilichonse chimene chimayenda mokwawa pa dziko lapansi."

Ndipo Yehova Mulungu anati, "Sibwino kuti munthu akhale yekha. Ndidzamupangira mnzake womuthandiza."

Kwa mkaziyo Iye anati,

"Ndidzachulukitsa ululu wako kwambiri pamene uli ndi pakati;

ndipo udzamva ululu pa nthawi yako yobereka ana.

Udzakhumba mwamuna wako,

ndipo adzakulamulira."

Komabe mwa Ambuye, mkazi amadalira mwamuna ndipo mwamuna amadalira mkazi. Pakuti monga mkazi anachokera kwa mwamuna, momwemonso mwamuna anabadwa mwa mkazi. Koma zonse zichokera kwa Mulungu.

Inu akazi, muzigonjera amuna anu, monga mumagonjera kwa Ambuye. Pakuti mwamuna ndi mutu wa mkazi monga momwe Khristu ali mutu wa mpingo, thupi lake, limene Iyeyo ndi Mpulumutsi wake. Tsono monga mpingo umagonjera Khristu, momwemonso akazi akuyenera kugonjera amuna awo mu zonse.

Chimodzimodzinso, phunzitsa amayi achikulire kuti akhale aulemu mʼmakhalidwe awo, asakhale osinjirira anzawo kapena zidakwa, koma akhale alangizi abwino. Tsono atha kulangiza amayi achichepere kukonda amuna awo ndi ana awo. Kuwaphunzitsa kukhala odziletsa ndi oyera mtima, osamala bwino mabanja awo, okoma mtima, ndi ogonjera amuna awo. Choncho palibe amene adzanyoze mawu a Mulungu.

Seja o primeiro