O papel do homem
A Bíblia define o papel do homem na família e na sociedade: líder servidor, provedor fiel, pai presente e marido amoroso, seguindo o exemplo de Cristo.
Marido e pai
O marido deve amar a esposa como Cristo amou a Igreja. O pai é chamado a criar os filhos na disciplina e instrução do Senhor.
Inu amuna, kondani akazi anu monga momwe Khristu anakondera mpingo nadzipereka yekha mʼmalo mwa mpingowo
Abambo musakwiyitse ana anu; mʼmalo mwake, muwalere mʼchiphunzitso ndi mʼchilangizo cha Ambuye.
Inu amuna, kondani akazi anu ndipo musawapsere mtima.
Momwemonso amuna inu, khalani mwanzeru ndi akazi anu, ndipo muwachitire ulemu monga anzanu ofowoka ndiponso olandira nanu pamodzi mphatso ya moyo wosatha, kuti pasakhale kanthu kotsekereza mapemphero anu.
Provedor e responsável
Quem não cuida dos seus é pior que o descrente. O homem deve trabalhar com diligência e prover para sua família com honra.
Ngati wina sasamalira abale ake, makamaka a mʼbanja mwake mwenimweni, ameneyo wakana chikhulupiriro ndipo ndi woyipa kuposa wosakhulupirira.
Pakuti ngakhale pamene tinali nanu, tinakupatsani lamulo lakuti, "Munthu wosafuna kugwira ntchito, asadye."
Chilichonse mungachite, muchite ndi mtima wanu onse, monga mmene mungagwirire ntchito ya Ambuye osati ya anthu.
Tsono woyangʼanira ayenera kukhala munthu wopanda chotsutsika nacho, mwamuna wa mkazi mmodzi yekha, woganiza bwino, wodziretsa, waulemu, wosamala bwino alendo, wodziwa kuphunzitsa. Asakhale chidakwa, asakhale wandewu, koma wofatsa, asakhale wokonda mikangano, kapena wokonda ndalama. Akhale wodziwa kusamala bwino banja lake ndi kulera ana ake bwino, kuti akhale omvera ndi aulemu weniweni.
Caráter e liderança
O homem de Deus é corajoso, íntegro e cheio do Espírito. Ele lidera pelo exemplo e guia sua casa nos caminhos do Senhor.
Khalani tcheru; khazikikani mʼchikhulupiriro chanu; limbani mtima; khalani amphamvu.
Pakuti ndasankha iyeyu kuti adzatsogolere ana ake ndi a pa banja lake, kuti asunge mawu a Yehova pochita zoyenera ndi zachilungamo. Choncho Yehova adzachita kwa Abrahamu chimene anamulonjeza iye."
Musaledzere ndi vinyo, chifukwa adzawononga moyo wanu. Mʼmalo mwake, mudzazidwe ndi Mzimu Woyera.