Pular para o conteúdo
Publicidade

As 10 parábolas mais importantes de Jesus

Por Bíblia Online  - 

Jesus ensinou lições profundas por meio de parábolas, histórias curtas e simbólicas que comunicam verdades espirituais. Cada parábola tem um significado especial e atemporal, revelando o caráter de Deus e ensinando como viver como cristãos. Aqui estão 10 das parábolas mais marcantes e suas lições:

1. Parábola do Semeador (Mateus 13:3-9)

Pamenepo Iye anawawuza zinthu zambiri mʼmafanizo ndi kuti, "Mlimi anapita kukafesa mbewu zake. Akufesa, zina zinagwera mʼmbali mwa njira ndipo mbalame zinabwera ndi kuzidya. Zina zinagwa pamalo a miyala pamene panalibe dothi lambiri. Zinamera mofulumira chifukwa panalibe dothi lambiri. Koma dzuwa litakwera, mbewu zinapserera ndipo zinawuma chifukwa zinalibe mizu. Mbewu zina zinagwa pa minga ndipo mingayo inayanga ndi kuzirepheretsa kukula. Koma mbewu zina zinagwa pa nthaka yabwino ndipo zinabala zipatso 100, zina 60 ndipo zinanso makumi atatu mwa zimene zinafesedwa. Amene ali ndi makutu amve."

A parábola do semeador fala sobre a receptividade das pessoas à Palavra de Deus. Cada tipo de solo representa diferentes maneiras de receber e aplicar o Evangelho em nossas vidas. Somente um coração fértil e comprometido pode dar frutos espirituais abundantes.

2. O Bom Samaritano (Lucas 10:25-37)

Fanizo la Msamariya Wachifundo

Nthawi ina katswiri wa malamulo anayimirira kuti ayese Yesu. Iye anati, "Aphunzitsi, ndichite chiyani kuti ndikhale ndi moyo wosatha?"

Yesu anayankha kuti, "Mwalembedwa chiyani mʼMalamulo, ndipo iwe umawerenga zotani?"

Iye anayankha kuti, "Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse ndi nzeru zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini."

Yesu anayankha kuti, "Iwe wayankha bwino, chita zimenezi ndipo udzakhala ndi moyo."

Koma iye anafuna kudzilungamitsa yekha, ndipo anamufunsanso Yesu kuti, "Kodi mnansi wanga ndani?"

Yesu pomuyankha anati, "Munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Pa njira anavulazidwa ndi achifwamba. Anamuvula zovala zake, namumenya ndi kuthawa, namusiya ali pafupi kufa. Wansembe ankapita pa njira yomweyo, ndipo ataona munthuyo, analambalala. Chimodzimodzinso, Mlevi wina pamene anafika pa malopo ndi kumuona, analambalalanso. Koma Msamariya wina, ali pa ulendo wake, anafika pamene panali munthuyo; ndipo atamuona, anamva naye chisoni. Anapita panali munthu wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa zilonda zake, nʼkuzimanga. Kenaka anamukweza pa bulu wake, napita naye ku nyumba ya alendo, namusamalira. Mmawa mwake anatenga ndalama ziwiri zasiliva nazipereka kwa woyangʼanira nyumbayo, nati, Musamalireni munthuyu, ndipo pobwera ndidzakubwezerani zonse zimene mugwiritse ntchito.

"Kodi ukuganiza ndi ndani mwa atatuwa, amene anali mnansi wa munthu amene anavulazidwa ndi achifwambawo?"

Katswiri wa Malamulo uja anayankha kuti, "Amene anamuchitira chifundo."

Yesu anamuwuza kuti, "Pita, uzikachita chimodzimodzi."

Essa parábola nos ensina sobre o amor ao próximo, independentemente de raça ou religião. O samaritano ajudou um desconhecido, mostrando que a verdadeira fé se revela no amor ao próximo.

3. A Ovelha Perdida (Lucas 15:4-7)

"Tiyerekeze kuti mmodzi mwa inu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi yatayika, kodi iye sangasiye 99 zija kutchire ndi kupita kukafuna yotayikayo mpaka atayipeza? Ndipo iye akayipeza, amayinyamula pa phewa lake mwachimwemwe ndi kupita kwawo. Kenaka amayitana anzake ndi anansi pamodzi, ndi kuti, Kondwerani nane; ine ndayipeza nkhosa yanga yotayika ija. Ine ndikukuwuzani kuti momwemonso kudzakhala chikondwerero chachikulu kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi amene watembenuka mtima kusiyana ndi anthu olungama 99 amene ali otembenuka mtima kale."

Deus é como o pastor que busca incessantemente uma ovelha perdida. Essa parábola revela o amor incansável de Deus pelos pecadores, celebrando a alegria no céu quando alguém se arrepende.

4. O Filho Pródigo (Lucas 15:11-32)

Fanizo la Mwana Wolowerera

Yesu anapitiriza kunena kuti, "Panali munthu amene anali ndi ana aamuna awiri. Wamngʼonoyo anati kwa abambo ake, Abambo, patseni gawo langa la chuma chanu.Ndipo iye anawagawira awiriwo chuma chawo.

"Pasanapite nthawi, wamngʼonoyo anasonkhanitsa chuma chake chonse, napita ku dziko lakutali ndipo kumeneko anayamba kumwaza chuma chake mʼnjira zachitayiko. Iye atawononga zonse, kunagwa njala yoopsa mʼdziko lonselo ndipo anayamba kusauka. Iye anapita kwa nzika ina ya dzikolo nakakhala naye ndi kumagwira ntchito, amene anamutumiza ku munda kukadyetsa nkhumba. Iye analakalaka atakhutitsa mimba yake ndi makoko amene nkhumbazo zinkadya, koma panalibe wina amene anamupatsa kanthu.

"Maganizo ake atabweramo, iye anati, Ndi antchito angati a abambo anga amene ali ndi chakudya chimene amadya nʼkutsalako ndipo ine ndili pano kufa ndi njala! Ine ndinyamuka ndi kubwerera kwa abambo anga ndipo ndikati kwa iwo: abambo, ine ndachimwira kumwamba ndi kwa inu. Ndine wosayeneranso kutchedwa mwana wanu; munditenge ngati mmodzi wa antchito anu. Ndipo iye ananyamuka ndi kupita kwa abambo ake.

"Koma iye akanali patali, abambo ake anamuona ndipo anamvera chisoni; anathamangira mwanayo, namukumbatira ndi kupsompsona.

"Mwanayo anati, Abambo, ine ndachimwira kumwamba ndi inunso. Ine sindiyenera konse kutchedwa mwana wanu.

"Koma abambowo anati kwa antchito ake, Fulumirani! Bweretsani mkanjo wabwino kwambiri ndipo mumuveke. Muvekeni mphete ndi nsapato. Bweretsani mwana wangʼombe wonenepa ndipo iphani. Tiyeni tikhale ndi phwando ndi kukondwerera. Pakuti mwana wangayu anali wakufa, ndipo ali ndi moyonso; iye anatayika ndipo wapezeka.Chomwecho anayamba kukondwerera.

"Nthawi imeneyi, mwana wake wamkulu uja anali ku munda. Iye atafika pafupi ndi nyumba, anamva anthu akuyimba ndi kuvina. Ndipo iye anayitana mmodzi wa antchito, namufunsa chimene chimachitika. Iye anayankha kuti, Mʼbale wako wabwera ndipo abambo ako apha mwana wangʼombe wonenepa chifukwa wabwera wamoyo ndipo ali bwino.

"Mwana wamkulu anakwiya ndipo anakana kulowa. Chomwecho abambo ake anatuluka ndi kumudandaulira. Koma iye anayankha abambo ake kuti, Taonani! Zaka zonsezi ndakhala ndikukutumikirani kugwira ntchito yowawa ndipo palibe pamene sindinamvere malamulo anu. Koma inu simunandipatse ngakhale mwana wambuzi kuti ine ndichite phwando ndi anzanga. Koma pamene mwana wanu uyu amene wawononga chuma chanu ndi achiwerewere wabwera ku nyumba, inu mwamuphera mwana wangʼombe wonenepa.’ "

Abambowo anati, "Mwana wanga, iwe umakhala ndi ine nthawi zonse ndipo zonse ndili nazo ndi zako. Koma tinayenera kukondwera ndi kusangalala, chifukwa mʼbale wako uyu anali wakufa ndipo ali ndi moyonso; iye anali wotayika ndipo wapezeka."

A parábola do filho pródigo fala sobre o perdão e o amor incondicional de Deus por Seus filhos, mesmo quando se desviam.

5. A Pérola de Grande Valor (Mateus 13:45-46)

"Komanso Ufumu wakumwamba ufanana ndi wogulitsa malonda amene amafuna ngale zabwino. Atapeza imodzi ya mtengowapatali, iye anapita nakagulitsa chilichonse anali nacho ndi kukayigula."

Jesus ensina que o Reino de Deus é o bem mais precioso e devemos estar dispostos a renunciar tudo para possuí-lo.

6. O Fariseu e o Publicano (Lucas 18:9-14)

Fanizo la Mfarisi ndi Wolandira Msonkho

Yesu ananena fanizoli kwa amene amadzikhulupirira mwa iwo okha kuti anali wolungama nanyoza ena onse. "Anthu awiri anapita ku Nyumba ya Mulungu kukapemphera, wina Mfarisi ndi winayo wolandira msonkho. Mfarisiyo anayimirira ndipo anapemphera za iye mwini kuti, Mulungu, ine ndikuyamika kuti sindili ngati anthu ena onse, achifwamba, ochita zoyipa, achigololo, sindilinso ngati wolandira msonkhoyu. Ine ndimasala kudya kawiri pa Sabata ndipo ndimapereka chakhumi pa zonse ndimapeza.

"Koma wolandira msonkhoyo ali chiyimire potero, sanathe nʼkomwe kuyangʼana kumwamba; koma anadziguguda pachifuwa ndipo anati, Mulungu, chitireni chifundo, ine wochimwa.

"Ine ndikukuwuzani kuti munthu wolandira msonkhoyu, osati Mfarisiyu, anapita kwawo atalungamitsidwa pamaso pa Mulungu. Chifukwa chake, aliyense wodzikweza adzachepetsedwa, ndipo wodzichepetsa adzakwezedwa."

Essa parábola nos lembra que Deus valoriza um coração humilde e arrependido, em contraste com a arrogância espiritual. O publicano, ao reconhecer seus pecados, foi justificado diante de Deus.

7. Os Talentos (Mateus 25:14-30)

Fanizo la Kagwiritsidwe Ntchito ka Ndalama

"Komanso udzafanizidwa ndi munthu amene ankapita pa ulendo, ndipo anayitana antchito ake nawasiyira chuma chake. Wina anamupatsa ndalama 5,000, kwa wina 2,000 ndi kwa wina 1,000. Aliyense monga mwa nzeru zake. Pamenepo anapita pa ulendo wake. Munthu amene analandira ndalama 5,000 uja, anapita nthawi yomweyo nachita nazo malonda napindula 5,000 zina. Chimodzimodzinso amene analandira 2,000 uja anapindula 2,000 zina. Koma munthu amene analandira 1,000 uja, anapita nakumba dzenje nabisapo ndalama ya mbuye wake.

"Patapita nthawi yayitali, mbuye wa antchitowo anabwera nawayitana kuti afotokoze chimene anachita ndi ndalama zija. Munthu amene analandira ndalama 5,000 uja anabweretsa 5,000 zina nati, Ambuye munandisungitsa 5,000, taonani ndapindula 5,000 zinanso.

"Ambuye ake anayankha nati, Wachita bwino, wantchito wabwino ndi wokhulupirika iwe! Wakhala wokhulupirika pa zinthu zochepa; ndidzakuyika iwe kukhala woyangʼanira zinthu zambiri. Bwera, udzakondwere pamodzi ndi mbuye wako!

"Munthu amene anali ndi ndalama 2,000 uja anabweranso nati, Ambuye munandisungitsa 2,000, onani, ndapindula 2,000 zinanso.

"Mbuye wake anayankha nati, Wachita bwino, wantchito wabwino ndi wokhulupirika! Wakhala wokhulupirika pa zinthu zochepa; ndidzakuyika kukhala woyangʼanira zinthu zambiri. Bwera, udzakondwere pamodzi ndi mbuye wako!

"Kenaka munthu amene analandira ndalama 1,000 uja anabwera nati, Ambuye ndinadziwa kuti ndinu munthu wowuma mtima, amene mumakolola pamene simunadzale ndi kututa kumene simunafese. Choncho ndinachita mantha ndipo ndinapita ndi kukabisa ndalama yanuyo pa dzenje. Onani, si iyi ndalama yanu ija.

"Mbuye wake anayankha nati, Iwe wantchito woyipa ndi waulesi! Iwe umadziwa kuti ndimakolola pamene sindinadzale, ndi kututa kumene sindinafese. Bwanji sunayike ndalama yanga kwa osunga ndalama kuti ine pobwera ndidzalandire ndalama yangayo pamodzi ndi chiwongoladzanja?

" Mulandeni ndalamayo, ndipo patsani iye amene ali ndi ndalama 10,000. Pakuti aliyense amene ali nazo adzapatsidwa zambiri, ndipo adzakhala nazo zochuluka. Aliyense amene alibe adzalandidwa ngakhale chimene ali nacho. Ndipo muponyeni wantchito wopanda phinduyu kunja, ku mdima kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.’ "

Nesta história, Jesus ensina sobre a responsabilidade de usar bem os dons e recursos que Deus nos confiou. A fidelidade nas pequenas coisas abre portas para bênçãos maiores.

8. O Rico e Lázaro (Lucas 16:19-31)

Za Munthu Wachuma ndi Lazaro

"Panali munthu wachuma amene ankavala zovala zofiirira za mtengowapatali ndipo ankakhala moyo wachisangalalo tsiku lililonse. Pa khomo la mpanda wake ankagonekapo munthu wopempha wotchedwa Lazaro, wazilonda thupi lonse ndipo ankafunitsitsa atadya zomwe zinkagwa pansi kuchokera pamene munthu wolemerayo amadyerapo. Agalu ankabweranso ndi kumanyambita zilonda zake.

"Nthawi inafika imene wopemphayo anamwalira ndipo angelo anamunyamula nakamuyika mʼmanja mwa Abrahamu. Munthu wolemerayo anamwaliranso ndipo anayikidwa mʼmanda. Ali mʼgehena kuzunzika, anakweza maso ake ndipo anaona Abrahamu ali ndi Lazaro pambali pake. Ndipo anafuwula kwa iye kuti, Abambo Abrahamu, mundimvere chisoni ine ndipo mutumeni Lazaroyo kuti aviyike msonga ya chala chake mʼmadzi kuti aziziritse lilime langa, chifukwa ndikumva ululu mʼmoto muno.

"Koma Abrahamu anayankha kuti, Mwanawe kumbukira kuti nthawi yamoyo wako unalandira zinthu zako zabwino, pamene Lazaro analandira zinthu zoyipa, koma tsopano akusangalatsidwa kuno ndipo iwe uli mʼmazunzo. Ndipo kuwonjezera pa zonsezi, pakati pa inu ndi ife pali chiphompho chachikulu chimene chinayikidwa, kotero kuti amene akufuna kubwera kumeneko sangathe, kapena palibe amene angawoloke kuchokera kumeneko kudzafika kuno.

"Iye anayankha kuti, Ndipo ndikupemphani inu, abambo, mutumeni Lazaro ku nyumba ya abambo anga, pakuti ine ndili ndi abale asanu. Lolani iye akawachenjeze kotero kuti asadzabwere kumalo ano amazunzo.

"Abrahamu anayankha kuti, Ali ndi Mose ndi Aneneri; aleke amvere iwo.

"Iye anati, Ayi, bambo Abrahamu, koma ngati wina ochokera kwa akufa adzapita kwa iwo, adzatembenuka mtima.

"Anati kwa iye, Ngati iwo samvera Mose ndi Aneneri, sadzakhulupirira ngakhale wina atauka kwa akufa.’ "

A parábola alerta sobre as consequências de negligenciar os necessitados e viver para si mesmo. Também destaca a realidade do julgamento e da vida após a morte.

9. O Joio e o Trigo (Mateus 13:24-30)

Fanizo la Namsongole

Yesu anawawuza fanizo lina kuti: "Ufumu wakumwamba ufanana ndi munthu amene anafesa mbewu zabwino mʼmunda mwake. Koma aliyense akugona usiku mdani wake anabwera ndi kufesa namsongole pakati pa tirigu ndipo anachoka. Pamene tirigu anamera ndi kutulutsa ngala, namsongole anaonekanso.

"Antchito ake anabwera kwa iye ndi kuti, Bwana, kodi simunafese mbewu zabwino mʼmunda mwanu? Nanga namsongole wachokera kuti?

"Iye anayankha kuti, Ndi mdani amene anachita izi.

"Antchito anamufunsa iye kuti, Kodi mufuna kuti tipite tikamuzule?

"Iye anakana nati, Ayi. Chifukwa pamene mukuzula namsongoleyo mwina inu mungazulire pamodzi ndi tirigu. Zisiyeni zonse zikulire pamodzi mpaka nthawi yokolola. Pa nthawi imeneyo ndidzawuza okolola kuti: Poyamba sonkhanitsani namsongole ndi kumumanga mʼmitolo kuti atenthedwe, kenaka sonkhanitsani tirigu ndi kumuyika mʼnkhokwe yanga.’ "

Essa história simboliza o bem e o mal coexistindo no mundo até o julgamento final, quando Deus fará a separação entre os justos e os ímpios.

10. As Dez Virgens (Mateus 25:1-13)

Fanizo la Anamwali Khumi

"Nthawi imeneyo ufumu wakumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi amene anatenga nyale zawo napita kukakumana ndi mkwati. Asanu anali opusa ndipo asanu ena anali ochenjera. Opusawo anatenga nyale zawo koma sanatenge mafuta; koma ochenjerawo anatenga mafuta awo mʼmabotolo pamodzi ndi nyale zawo. Mkwati anachedwa ndipo onse anayamba kusinza nagona.

"Pakati pa usiku kunamveka kufuwula kuti, Onani Mkwati! Tulukani kuti mukakumane naye!

"Pamenepo anamwali onse anadzuka nayatsa nyale zawo. Opusawo anati kwa ochenjerawo, Tipatseniko mafuta anu; nyale zathu zikuzima.

"Ochenjerawo anayankha, nati, Ayi sangakwanire inu ndi ife. Pitani kwa ogulitsa mafuta ndi kukadzigulira nokha.

"Koma pamene ankapita kukagula mafutawo, mkwati anafika. Anamwali amene anali okonzeka aja analowa naye pamodzi mʼnyumba ya phwando la ukwati. Ndipo khomo linatsekedwa.

"Pambuyo pake enawo anabwera nati, Ambuye! Ambuye! Titsekulireni!

"Koma iye anayankha kuti, Zoonadi, ine ndikuwuzani kuti sindikukudziwani.

"Choncho khalani odikira, popeza simudziwa tsiku kapena nthawi."

Jesus enfatiza a necessidade de estarmos sempre preparados espiritualmente para Sua segunda vinda, pois ninguém sabe o momento exato.

As parábolas de Jesus continuam sendo fontes ricas de sabedoria e direção para a vida cristã. Ao aplicarmos esses ensinamentos, nos aproximamos mais de Deus e de Sua vontade.

Se este artigo te ajudou, faça sua parte e compartilhe a Palavra de Deus com aqueles que você ama.

Seja o primeiro