Publicidade

Páscoa

Por Bíblia Online

A Páscoa é a celebração suprema da redenção. Do cordeiro pascal no Egito ao Cordeiro de Deus que tira o pecado do mundo, ela aponta para o sacrifício e a vitória de Cristo.

A caminhada para a cruz

Jesus entrou em Jerusalém como Rei humilde, e a multidão o aclamou. Ele sabia do sofrimento que viria, mas caminhou em obediência até o fim.

Magulu amene anali patsogolo pake ndi amene amamutsatira anafuwula kuti,

"Hosana Mwana wa Davide!"

"Wodala Iye amene abwera mʼdzina la Ambuye!"

"Hosana mmwambamwamba!"

Inu Yehova, tipulumutseni;

Yehova, tipambanitseni.

Wodala amene akubwera mʼdzina la Yehova.

Tikukudalitsani kuchokera ku nyumba ya Yehova.

Sangalala kwambiri, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni!

Fuwula, mwana wamkazi wa Yerusalemu!

Taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe,

yolungama ndi yogonjetsa adani,

yodzichepetsa ndi yokwera pa bulu,

pa mwana wamphongo wa bulu.

"Tikupita ku Yerusalemu, ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo. Iwo adzamuweruza kuti aphedwe, ndipo adzamupereka kwa anthu a mitundu ina kuti amunyoze ndi kumukwapula ndi kumupachika. Pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa!"

A paixão de Cristo

Jesus foi zombado, açoitado e crucificado. Ele orou no Getsêmani e entregou sua vida voluntariamente, dizendo: 'Está consumado!'

Anamuvula malaya ake namuveka Iye malaya ofiira aufumu. Ndipo kenaka analuka chipewa chaminga nachiyika pa mutu pake. Anamugwiritsa ndodo mʼdzanja lake lamanja nagwada pamaso pake namuchitira chipongwe nati, "Tikulonjereni Mfumu ya Ayuda."

Pamwamba pa mutu wake analembapo mawu osonyeza mlandu wake akuti, "uyu ndi yesu, mfumu ya ayuda."

Iye anati, "Abba, Atate, zinthu zonse ndi zotheka ndi Inu. Chotsereni chikhochi. Komabe chitani zimene Inu mukufuna, osati zimene Ine ndikufuna."

Yesu anafuwula ndi mawu okweza kuti, "Atate, ndikupereka mzimu wanga mʼmanja mwanu." Atanena zimenezi, anamwalira.

Yesu atalandira chakumwachi anati, "Kwatha." Ndipo Iye anaweramitsa mutu wake napereka mzimu wake.

A ressurreição gloriosa

Ele não está aqui — ressuscitou! O túmulo vazio é a prova de que a morte foi derrotada e Cristo vive para sempre.

Mngelo anati kwa amayiwo, "Musachite mantha popeza ndikudziwa kuti mukufuna Yesu amene anapachikidwa. Iye muno mulibe, wauka monga mmene ananenera. Bwerani, dzaoneni malo amene anagona.

Iye anati, "Musaope. Kodi mukufuna Yesu wa ku Nazareti, amene anapachikidwa? Wauka! Sali muno. Onani malo amene anamugonekapo.

Iye sali muno ayi. Wauka! Kumbukirani zimene anakuwuzani pamene anali nanu ku Galileya: ‘Mwana wa Munthu ayenera kuperekedwa mʼmanja mwa anthu ochimwa, napachikidwa ndipo tsiku lachitatu adzaukitsidwanso.’ "

Pomaliza wophunzira winayo, amene anafika ku manda moyambirira, analowanso mʼkati, iye anaona ndi kukhulupirira. (Iwo sanazindikire kuchokera mʼmalemba kuti Yesu anayanera kuuka kuchokera kwa akufa).

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-22_10-02-25-