Publicidade

Pecado

Por Bíblia Online

O pecado é a realidade que separa a humanidade de Deus. Mas a Bíblia também revela a solução: o sangue de Cristo que nos purifica e a graça que nos liberta de toda condenação.

A universalidade do pecado

Todos pecaram e carecem da glória de Deus. Não há justo, nem sequer um. O pecado entrou no mundo por um homem, mas a graça veio por Jesus.

pakuti onse anachimwa naperewera pa ulemerero wa Mulungu

pakuti onse anachimwa naperewera pa ulemerero wa Mulungu ndipo onse alungamitsidwa mwaulere mwa chisomo chake chifukwa cha Khristu Yesu amene anawawombola.

Chifukwa chake palibe mmodzi amene adzayesedwa wolungama pamaso pake chifukwa chosunga Malamulo, kuti ife timazindikira tchimo kupyolera mu Malamulo.

Pakuti malipiro a tchimo ndi imfa, koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Tonsefe takhala ngati anthu amene ndi odetsedwa,

ndipo ntchito zathu zili ngati sanza za msambo;

tonse tafota ngati tsamba,

ndipo machimo athu akutiwuluzira kutali ngati mphepo.

Aliyense amene amachimwa amaphwanya lamulo; pakuti tchimo ndi kuphwanya lamulo.

Liberdade da condenação

Não há condenação para os que estão em Cristo Jesus. Ele nos libertou da lei do pecado e da morte para vivermos em novidade de vida.

Moyo Watsopano mwa Khristu

Choncho, tsopano amene ali mwa Khristu Yesu alibe mlandu owatsutsa chifukwa mwa Khristu Yesu, lamulo la Mzimu Woyera amene amapereka moyo, lawamasula ku lamulo la tchimo ndi la imfa.

Nʼchifukwa chake, musalole tchimo lilamulire matupi anu amene anafa kuti mumvere zilakolako zonyansa. Musapereke ziwalo zathupi lanu ku tchimo, ngati zipangizo zamakhalidwe oyipa. Mʼmalo mwake, mudzipereke kwa Mulungu, ngati amene achoka ku imfa kupita ku moyo. Ndipo mupereke ziwalo zathupi lanu ngati zipangizo zachilungamo. Tchimo silidzakhalanso ndi mphamvu pa inu, chifukwa Malamulo sakulamulira moyo wanu koma chisomo.

Ife Ndife Akapolo a Mulungu

Nʼchiyani tsono? Kodi tidzichimwa chifukwa sitikulamulidwa ndi Malamulo koma chisomo? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Kodi inu simudziwa kuti pamene mudzipereka kwa wina wake, kumumvera ngati akapolo, ndinu akapolo a amene mumumvera? Ngati ndinu akapolo a tchimo mudzafa. Koma ngati ndinu akapolo akumvera, mudzakhala olungama pamaso pake. Koma ayamikidwe Mulungu pakuti ngakhale munali akapolo a tchimo, munamvera ndi mtima wonse chiphunzitso chimene munalandira. Inu munamasulidwa ku tchimo ndipo tsopano mwasanduka akapolo achilungamo.

Ife Ndife Akapolo a Mulungu

Nʼchiyani tsono? Kodi tidzichimwa chifukwa sitikulamulidwa ndi Malamulo koma chisomo? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi!

Ife tikudziwa kuti Malamulo ndi auzimu; koma ine ndine munthu wofowoka chabe, wogulitsidwa ngati kapolo ku uchimo. Ine sindizindikira zimene ndimachita. Pakuti zimene ndimafuna kuchita sindizichita koma zimene ndimadana nazo ndi zimene ndimazichita. Ndipo ngati ndimachita zimene sindimafuna kuzichita, ndiye kuti ndikuvomereza kuti lamulo ndi labwino. Monga mmene zililimu, si inenso mwini amene ndimazichita zimenezi, koma tchimo limene lili mʼkati mwanga.

Yesu anayankha kuti, "Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense wochita tchimo ndi kapolo wa tchimolo.

Confissão e perdão

Se confessarmos os nossos pecados, Deus é fiel e justo para nos perdoar e purificar de toda injustiça. A confissão liberta a alma.

Kuwulula Machimo ndi Kukhululukidwa

Tikanena kuti tilibe tchimo, tikudzinyenga tokha ndipo mwa ife mulibe choonadi. Koma tikavomereza machimo athu, Iye ndi wokhulupirika ndi wolungama ndipo adzatikhululukira machimo athu, nadzatiyeretsa ndi kutichotsera chosalungama chilichonse.

Koma tikavomereza machimo athu, Iye ndi wokhulupirika ndi wolungama ndipo adzatikhululukira machimo athu, nadzatiyeretsa ndi kutichotsera chosalungama chilichonse.

Tikanena kuti timayanjana naye, koma nʼkumayendabe mu mdima, tikunama ndipo sitikuchita choonadi.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Pamene Mneneri Natani anabwera kwa iye atachita chigololo ndi Batiseba.

Mundichitire chifundo, Inu Mulungu,

molingana ndi chikondi chanu chosasinthika;

molingana ndi chifundo chanu chachikulu

mufafanize mphulupulu zanga.

Munditsuke zolakwa zanga zonse

ndipo mundiyeretse kuchotsa tchimo langa.

Motsutsana ndi Inu, Inu nokha, ndachimwa

ndipo ndachita zoyipa pamaso panu,

Kotero kuti inu mwapezeka kuti ndinu wolungama

pamene muyankhula ndi pamene muweruza.

Zoonadi ine ndinali wochimwa pomwe ndimabadwa,

wochimwa kuyambira pa nthawi imene amayi anga anakhala woyembekezera ine.

Zoonadi inu mumafuna choonadi mu ziwalo zamʼkati mwanga;

mumandiphunzitsa nzeru mʼkati mwanga mwenimweni.

Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera,

munditsuke ndipo ndidzayera kuposa matalala

Mundilole ndimve chimwemwe ndi chisangalalo,

mulole kuti mafupa amene mwawamphwanya akondwere.

Mufulatire machimo anga

ndi kufafaniza zolakwa zanga zonse.

Kotero ine ndinavomereza tchimo langa kwa Inu,

sindinabise mphulupulu zanga.

Ndinati, "Ine ndidzawulula

zolakwa zanga kwa Yehova,

ndipo Inu munandikhululukira

mlandu wa machimo anga."

Sela

Salimo la Davide. Malangizo.

Ngodala munthu

amene zolakwa zake zakhululukidwa;

amene machimo ake aphimbidwa.

Chifukwa cha dzina lanu, Inu Yehova,

khululukireni mphulupulu zanga, ngakhale kuti ndi zochuluka.

Kumbukirani Inu Yehova chifundo ndi chikondi chanu chachikulu,

pakuti ndi zakalekale.

Musakumbukire machimo a ubwana wanga

ndi makhalidwe anga owukira;

molingana ndi chikondi chanu ndikumbukireni ine,

pakuti Inu Yehova ndinu wabwino.

Ndani angathe kudziwa zolakwa zake?

Mundikhululukire zolakwa zanga zobisika.

Wobisa machimo ake sadzaona mwayi,

koma aliyense amene awulula ndi kuleka machimowo, adzalandira chifundo.

Vencendo o pecado

Cristo nos resgatou e nos restaurou. Devemos mortificar as obras da carne, fugir do pecado e prosseguir em santidade.

Iye mwini anasenza machimo athu mʼthupi lake pa mtanda, kuti ife tife kutchimo ndi kukhala ndi moyo potsata chilungamo, ndipo ndi mabala ake munachiritsidwa.

Ndipo adzabala mwana wamwamuna, udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo."

Chifukwa cha ife, Mulungu anasandutsa wopanda tchimoyo kukhala tchimo, kuti mwa Iye ife tikakhale chilungamo cha Mulungu.

momwemonso Khristu anadzipereka nsembe kamodzi kokha kuchotsa machimo a anthu ambiri. Ndipo Iye adzaonekanso kachiwiri, osati kudzachotsa tchimo, koma kudzapereka chipulumutso kwa amene akumudikira.

Iye amene amachimwa ndi wa Satana, chifukwa mdierekezi wakhala akuchimwa kuyambira pa chiyambi. Mwana wa Mulungu anaonekera kuti awononge ntchito za mdierekezi.

Tikudziwa kuti aliyense amene ndi mwana wa Mulungu sachimwirachimwirabe. Yesu, Mwana wa Mulungu, amamusunga ndipo woyipa uja sangamukhudze.

Choncho, iphani zilakolako za dziko lapansi mwa inu, monga: dama, zodetsa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoyipa ndi umbombo, pakuti umbombo ndiko kupembedza mafano.

Koma pakati panu pasamveke nʼpangʼono pomwe zadama, kapena za mtundu wina uliwonse wa chodetsa, kapena za umbombo, chifukwa izi ndi zosayenera kwa anthu oyera a Mulungu.

Musayanjane nazo ntchito zosapindulitsa za mdima, koma mʼmalo mwake muzitsutse. Pakuti ndi zochititsa manyazi ngakhale kutchula zomwe zimachitika mseri.

Kwiyani koma musachimwe. Dzuwa lisalowe mukanali chikwiyire.

Responsabilidade e restauração

O pecado tem consequências, mas Deus restaura o arrependido. Devemos corrigir uns aos outros com mansidão e cobrir o pecado com amor.

Kuchita Zabwino kwa Onse

Abale, ngati munthu agwa mʼtchimo lililonse, inu amene Mzimu amakutsogolerani, mumuthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe.

Kuchita Zabwino kwa Onse

Abale, ngati munthu agwa mʼtchimo lililonse, inu amene Mzimu amakutsogolerani, mumuthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe. Thandizanani kusenza zolemetsa zanu, ndipo mʼnjira imeneyi mudzakwanitsa lamulo la Khristu.

Za Mʼbale Amene Akuchimwirani

"Ngati mʼbale wako akuchimwira, pita kamuwuze cholakwa chake pa awiri. Ngati akumvera, wamubweza mʼbale wakoyo.

Za Mʼbale Amene Akuchimwirani

"Ngati mʼbale wako akuchimwira, pita kamuwuze cholakwa chake pa awiri. Ngati akumvera, wamubweza mʼbale wakoyo.

Za Kuchimwitsa Ena

"Koma ngati wina aliyense achimwitsa mmodzi wa ana awa, amene akhulupirira Ine, kuti achimwe, kukanakhala bwino kuti iye amangiriridwe chimwala chachikulu mʼkhosi mwake ndi kumizidwa pansi pa nyanja.

"Chifukwa chiyani iwe uyangʼana kachitsotso ka mʼdiso la mʼbale wako koma susamalira chimtengo chili mʼdiso mwako?

Ngati inu mukhululukira anthu pamene akuchimwirani, Atate anu akumwamba adzakukhululukirani.

Choncho, ululiranani machimo anu ndi kupemphererana wina ndi mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama ndi lamphamvu ndipo limagwira ntchito.

Aliyense amene amadziwa zabwino zimene amayenera kuchita koma osazichita, ndiye kuti wachimwa.

Sendezani kufupi ndi Mulungu ndipo Iye adzasendeza kwa inu. Sambani mʼmanja mwanu, inu anthu ochimwa. Yeretsani mitima yanu, inu anthu okayikira.

Inu anthu achigololo, kodi simukudziwa kuti kuchita ubwenzi ndi dziko lapansi ndi kudana ndi Mulungu? Choncho, aliyense wosankha kukhala bwenzi la dziko lapansi amasanduka mdani wa Mulungu.

Mʼkamwa momwemo mutuluka matamando ndi kulalata. Abale anga, zisamatero ayi.

Koposa zonse muzikondana wina ndi mnzake kwambiri, chifukwa chikondi chimaphimba machimo ambiri.

Fuga do pecado

Bem-aventurado o que não anda no conselho dos ímpios. O caminho do justo é guardado pelo Senhor, e sua Palavra nos protege da queda.

Wodala munthu

amene satsatira uphungu wa anthu ochimwa,

kapena kuyima mʼnjira ya anthu oyipa,

kapena kukhala mʼmagulu a anthu onyoza.

Tsogolerani mayendedwe anga molingana ndi mawu anu;

musalole kuti tchimo lizindilamulira.

Munthu woyenda mwangwiro amayenda mosatekeseka;

koma amene amayenda njira yokhotakhota adzadziwika.

Munthu wabwino amatulutsa zinthu zabwino zosungidwa mu mtima mwake, koma munthu oyipa amatulutsa zinthu zoyipa zosungidwa mu mtima mwake. Pakamwa pake pamayankhula zimene zadzaza mu mtima mwake.

Kodi simukudziwa kuti munthu woyipa sadzalowa mu ufumu wa Mulungu? Musanyengedwe: achigololo, kapena opembedza mafano, kapena achiwerewere, kapena amuna adama, kapena ogonana ndi amuna okhaokha; kapena akuba, kapena aumbombo, kapena oledzera, kapena achipongwe, kapena opeza ndalama mwachinyengo sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.

Pilato anatulukanso ndipo anati kwa Ayuda, "Taonani, ine ndikumubweretsa kuti inu mudziwe kuti ine sindikupeza chifukwa chomuyimbira mlandu." Pamenepo Yesu anatuluka atavala nkhata yaminga ndi mkanjo wapepo ndipo Pilato anawawuza kuti, "Nayu munthu uja!"

Atangomuona Iye akulu a ansembe ndi akuluakulu ena anafuwula kuti, "Mpachikeni! Mpachikeni!"

Koma Pilato anayankha kuti, "Inu mutengeni ndi kumupachika. Koma ine sindikupeza chifukwa chomuyimbira mlandu."

Ngati mukhululukira aliyense machimo ake, iwo akhululukidwa; ngati simuwakhululukira, iwo sanakhululukidwe."

Ukanachita zabwino sindikanakulandira kodi? Koma tsopano wachita zoyipa ndipo tchimo likukudikira pa khomo pako, likufuna kukugwira; koma iwe uyenera kugonjetsa tchimolo."

Seja o primeiro
Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-