Pular para o conteúdo
Publicidade

Planejamento

Por Bíblia Online

O planejamento é sábio, mas deve sempre se submeter à vontade de Deus. A Bíblia ensina que devemos planejar com prudência, mas confiar que Deus dirige nossos passos.

Planejar com sabedoria

Contar nossos dias nos ensina a ter coração sábio. O planejamento prudente é elogiado na Escritura como expressão de bom senso.

Tiphunzitseni kuwerenga masiku athu molondola,

kuti tikhale ndi mtima wanzeru.

"Taganizani, ngati wina mwa inu akufuna kumanga nsanja, kodi iye sayamba wakhala pansi ndi kuganizira za mtengo wake kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kuti atsirizire?

Popanda uphungu zolinga zako munthu zimalephereka,

koma pakakhala aphungu ambiri zolinga zimatheka.

Pereka ntchito zako zonse mʼmanja mwa Yehova,

ndipo zolinga zako zidzachitikadi.

Usadzitopetse wekha ndi kufuna chuma,

ukhale ndi nzeru ya kudziretsa.

Deus dirige os passos

O coração do homem planeja, mas a resposta certa vem do Senhor. Seus caminhos são mais altos que os nossos, e seus planos prevalecem.

Mtima wa munthu umalingalira zochita,

koma Yehova ndiye amakhazikitsa njira zake.

Munthu amakonzekera zambiri mu mtima mwake,

koma cholinga cha Yehova ndiye chidzachitike.

"Pakuti maganizo anga siwofanana ndi maganizo anu,

ngakhale njira zanu si njira zanga,"

akutero Yehova.

"Monga momwe mlengalenga muli kutali ndi dziko lapansi,

momwemonso zochita zanga nʼzolekana kutali ndi zochita zanu,

ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.

Izinso zimachokera kwa Yehova Wamphamvuzonse,

wa uphungu wodabwitsa ndi wa nzeru zopambana.

Confiança no plano de Deus

Os planos do Senhor são de paz e esperança. Ele revela seus segredos aos seus servos e guia com fidelidade cada caminho confiado a Ele.

Pakuti Ine ndikudziwa zimene ndinakukonzerani," akutero Yehova, "ndimalingalira zabwino zokhazokha za inu osati zoyipa, ayi. Ndimalingalira zinthu zokupatsani chiyembekezo chenicheni pa za mʼtsogolo.

Zoonadi Ambuye Yehova sachita kanthu

asanawulule zimene akufuna kuchita

kwa atumiki ake, aneneri.

Akupatse chokhumba cha mtima wako

ndipo akuthandize kuti zonse wakonza zichitike.

Lolani kuti mmawa ubweretse mawu achikondi chanu chosasinthika,

pakuti ine ndimadalira Inu.

Mundisonyeze njira yoti ndiyendemo,

pakuti kwa Inu nditukulira moyo wanga.

Chilichonse Chili ndi Nthawi

Chinthu chilichonse chili ndi nthawi yake,

ndi nyengo yake yomwe anayika Mulungu:

koma Mulungu waululira ife mwa Mzimu wake.

Mzimu amafufuza zinthu zonse, ndi zozama za Mulungu zomwe.

Usachite naye nsanje munthu wachiwawa

kapena kutsanzira khalidwe lake lililonse.

Pakuti Yehova amanyansidwa ndi munthu woyipa

koma amayanjana nawo anthu olungama.

Seja o primeiro