Preservação das escrituras
A Palavra de Deus permanece para sempre. As Escrituras foram preservadas por Deus ao longo dos milênios para instrução, consolação e guia de todas as gerações.
A Palavra eterna
Céus e terra passarão, mas as palavras de Deus jamais passarão. Sua Palavra é eterna, infalível e imutável — a verdade que sustenta tudo.
Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha."
Ine ndikukuwuzani zoonadi kuti, kufikira kutha kwa thambo ndi dziko lapansi, chilichonse chimene chinalembedwa mʼmalamulo, ngakhale kalemba kakangʼonongʼono, chidzakwaniritsidwa.
Udzu umanyala ndipo maluwa amafota,
koma mawu a Mulungu wathu adzakhalapo mpaka muyaya."
Pakuti,
"Anthu onse ali ngati udzu,
ndipo ulemerero wawo uli ngati duwa la kuthengo.
Udzu umafota ndipo duwa limathothoka,
koma mawu a Ambuye adzakhala mpaka muyaya."
Ndipo awa ndi mawu amene tinalalikira kwa inu.
Popeza mwabadwanso, osati ndi mbewu imene imawonongeka, koma imene siwonongeka, ndiye kuti ndi Mawu a Mulungu amoyo ndi okhalitsa. Pakuti,
"Anthu onse ali ngati udzu,
ndipo ulemerero wawo uli ngati duwa la kuthengo.
Udzu umafota ndipo duwa limathothoka,
koma mawu a Ambuye adzakhala mpaka muyaya."
Ndipo awa ndi mawu amene tinalalikira kwa inu.
A inspiração divina
Toda Escritura é inspirada por Deus. Homens santos falaram da parte do Senhor, e a Palavra escrita é a expressão fiel da vontade divina.
Kuposa zonse, inu muyenera kuzindikira kuti palibe mawu a uneneri amene amatanthauzidwa pa okha. Pakuti mawu a uneneri sanadze mwa kufuna kwa anthu, koma anthu anayankhula zochokera kwa Mulungu, Mzimu Woyera atawayankhulitsa.
Khristu Mwana wa Mulungu Aposa Angelo
Kale lija Mulungu ankayankhula ndi makolo athu pa nthawi zosiyanasiyana ndiponso mwa njira zosiyanasiyana kudzera mwa aneneri. Koma masiku otsiriza ano, Mulungu wayankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Mwanayu anamusankha kuti akhale mwini wa zinthu zonse, ndiponso Mulungu analenga dziko lonse kudzera mwa Iye. Mwanayo ndiye kuwala kwa ulemerero wa Mulungu, chithunzithunzi chenicheni cha khalidwe lake. Iyeyu amachirikiza zinthu zonse ndi mphamvu ya mawu ake. Iye atayeretsa anthu kuchoka ku machimo awo, anakhala pansi kumwamba kudzanja lamanja la Mulungu waulemerero.
Mawu anasandulika thupi ndipo anakhala pakati pathu. Ife tinaona ulemerero wake, ulemerero wa Iye amene ndi Mwana mmodzi yekhayo wa Atate, wodzaza ndi chisomo ndi choonadi.
Ndikudziwa kuti chilichonse chimene Mulungu amachita chidzakhala mpaka muyaya; palibe zimene zingawonjezedwe kapena kuchotsedwa. Mulungu amazichita kuti anthu azimuopa.
A Palavra como guia e tesouro
A Palavra de Deus é lâmpada para os pés, espada do Espírito e tesouro para o coração. Guardá-la e meditá-la nos protege do pecado.
Ndasunga mawu anu mu mtima mwanga
kuti ndisakuchimwireni.
Zakumwamba zimalengeza za ulemerero wa Mulungu;
thambo limalalikira ntchito za manja ake.
Tsiku ndi tsiku zimayankhula mawu ambiri,
usiku ndi usiku zimaonetsa poyera nzeru.
Palibe kuyankhula, palibe mawu aliwonse;
liwu lawo silimveka.
Koma uthenga wawo umapita pa dziko lonse lapansi,
mawuwo amafika mpaka
kumalekezero a dziko lapansi.
Dzuwa lili ngati mkwatibwi wobwera kuchokera ku nsanja yake,
ngati katswiri wokondwerera kuthamanga pa mpikisano.
Limatuluka kuyambira mbali ina ya thambo
ndi kuzungulira mpaka mbali inanso;
palibe chinthu chotha kupewa kutentha kwake.
Lamulo la Yehova ndi langwiro,
kutsitsimutsa moyo.
Maumboni a Yehova ndi odalirika,
amapereka nzeru kwa wopanda nzeru.
Malangizo a Yehova ndi olungama,
amapereka chimwemwe mu mtima.
Malamulo a Yehova ndi onyezimira,
amapereka kuwala.
Ndipo mawu a Yehova ndi angwiro
monga siliva oyengedwa mʼngʼanjo yadothi,
oyengedwa kasanu nʼkawiri.
Inu Yehova mudzatitchinjiriza ndipo
mudzatiteteza kwa anthu otere kwamuyaya.
Nanga akuti chiyani? "Mawu ali pafupi ndi inu. Ali mʼkamwa mwanu ndi mu mtima mwanu." Ndiwo mawu achikhulupiriro amene ife tikuwalalikira,
Motero, chikhulupiriro chimabwera pamene timva uthenga ndipo uthenga umamveka kuchokera ku mawu a Khristu. Koma ndikufunsa kuti kodi iwo anamva? Inde, iwo anamva kuti,
"Liwu lawo linamveka ponseponse pa dziko lapansi.
Mawu awo anafika ku malekezero a dziko lonse."
Pakuti zilizonse zimene zinalembedwa kale zinalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembawo amatilimbikitsa kupirira kuti tikhale ndi chiyembekezo.
Malamulo amene ndakupatsani lero ayenera kukhala mu mtima mwanu. Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu. Muzikamba za malamulowa pamene muli mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mukugona ndi pamene mukudzuka. Muwamange ngati zizindikiro pa manja anu ndi kuwamangirira pa zipumi zanu. Muwalembe pa mphuthu za nyumba zanu ndi pa zipata zanu.
Ndikukupemphererani kuti mudziwe chikondi chija cha Khristu chopitirira nzeru za anthu, kuti mudzazidwe kwathunthu ndi moyo wa Mulungu mwini.
Izi ndi zabwino ndipo zimakondweretsa Mulungu Mpulumutsi wathu, amene amafuna kuti anthu onse apulumutsidwe ndipo kuti adziwe choonadi.