Protecção e segurança
Deus é nosso protetor e refúgio seguro. Em todas as circunstâncias, a Bíblia nos assegura que o Senhor guarda, sustenta e protege aqueles que nele confiam.
Deus, a nossa fortaleza
O Senhor é refúgio e fortaleza, socorro bem presente na angústia. Quem habita no esconderijo do Altíssimo descansa à sombra do Todo-Poderoso.
Mulungu ndiye kothawira kwathu ndi mphamvu yathu,
thandizo lopezekeratu pa nthawi ya mavuto.
Mulungu ndiye kothawira kwathu ndi mphamvu yathu,
thandizo lopezekeratu pa nthawi ya mavuto.
Iye amene amakhala mu mthunzi wa Wammwambamwamba
adzapuma mu mthunzi wa Wamphamvuzonse.
Ndidzanena za Yehova, "Iye ndiye pothawira panga ndi linga langa,
Mulungu wanga amene ndimadalira."
Adzakuphimba ndi nthenga zake,
ndipo udzapeza malo othawira mʼmapikomo;
kukhulupirika kwake kudzakhala chishango chako ndi lihawo.
Anthu 1,000 atha kufa pambali pako,
anthu 10,000 kudzanja lako lamanja,
koma zoopsazo sizidzafika pafupi ndi iwe.
Pakuti wasankha Wammwambamwamba kukhala malo ako okhalamo;
wavomera Yehova kukhala kothawira kwako.
Choncho palibe choyipa chimene chidzakugwera,
zoopsa sizidzafika pafupi ndi tenti yako.
Yehova ndiye kuwunika kwanga ndi chipulumutso changa;
ndidzaopa yani?
Yehova ndi linga la moyo wanga;
ndidzachita mantha ndi yani?
Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa;
Iye ndi linga langa, choncho sindidzagwedezeka.
Yehova ndiye kothawirako kwa opsinjika mtima,
linga pa nthawi ya mavuto.
O escudo do Senhor
Deus nos rodeia com sua proteção como um escudo. Ele é rocha, baluarte e libertador. Sua fidelidade nos cobre e nos guarda.
Koma Inu Yehova, ndinu chishango chonditeteza,
Inu mwandiveka ulemerero ndipo mwanditukula.
Inu Yehova, achulukadi adani anga!
Achulukadi amene andiwukira!
Ambiri akunena za ine kuti,
"Mulungu sadzamupulumutsa."
Sela
Koma Inu Yehova, ndinu chishango chonditeteza,
Inu mwandiveka ulemerero ndipo mwanditukula.
Kwa Yehova, Ine ndilira mofuwula
ndipo Iye amandiyankha kuchokera ku phiri lake loyera.
Sela
Ine ndimagona ndi kupeza tulo;
ndimadzukanso chifukwa Yehova amandichirikiza.
Sindidzaopa adani anga osawerengeka amene
abwera kulimbana nane kuchokera ku madera onse.
Kunena za Mulungu, zochita zake ndi zangwiro;
mawu a Yehova alibe cholakwika.
Iye ndi chishango
kwa onse amene amathawira kwa Iye.
Inu mumandipatsa chishango chachipambano,
ndipo dzanja lanu lamanja limandichirikiza;
mumawerama pansi kundikuza.
Munakulitsa njira yoyendamo ine,
kuti mapazi anga asaguluke.
Atamandike Yehova Thanthwe langa,
amene amaphunzitsa manja anga kuchita nkhondo;
zala zanga kumenya nkhondo.
Iye ndiye Mulungu wanga wachikondi ndi malo anga otetezedwa,
linga langa ndi mpulumutsi wanga,
chishango changa mmene ine ndimathawiramo,
amene amagonjetsa mitundu ya anthu pansi panga.
kwa Iye amene amapambanitsa mafumu,
amene amapulumutsa Davide mtumiki wake ku lupanga loopsa.
Koma lolani kuti onse amene apeza chitetezo mwa Inu akondwere;
lolani kuti aziyimba nthawi zonse chifukwa cha chimwemwe.
Aphimbeni ndi chitetezo chanu,
iwo amene amakonda dzina lanu akondwere mwa Inu.
Ndithu, Inu Yehova, mumadalitsa olungama;
mumawazungulira ndi kukoma mtima kwanu ngati chishango.
Ine ndikuyitana Inu, Mulungu wanga, pakuti mudzandiyankha;
tcherani khutu lanu kwa ine ndipo mumve pemphero langa.
Onetsani kudabwitsa kwa chikondi chanu chachikulu,
Inu amene mumapulumutsa ndi dzanja lanu lamanja
iwo amene amathawira kwa inu kuchoka kwa adani awo.
Mundisunge ine ngati mwanadiso;
mundibise mu mthunzi wa mapiko anu,
kuchoka kwa oyipa amene amandizinga ine,
kuchoka kwa anthu amene ndi adani anga, amene andizungulira ine.
Pakuti mfumu imadalira Yehova;
kudzera mʼchikondi chake chosatha cha Wammwambamwamba,
iyo sidzagwedezeka.
Dzanja lanu lidzayimitsa adani anu onse;
dzanja lanu lamanja lidzagwira adani anu.
Pa nthawi ya kuonekera kwanu
mudzawasandutsa ngʼanjo yamoto yotentha.
Mu ukali wake Yehova adzawameza,
ndipo moto wake udzawatha.
Inu ndi malo anga obisala;
muzinditeteza ku mavuto ndipo muzindizinga
ndi nyimbo zachipulumutso.
Sela
Segurança e provisão
O Senhor supre todas as necessidades dos seus filhos. Quem busca o Reino primeiro não precisa temer — nada faltará aos que temem ao Senhor.
Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
Mikango itha kulefuka ndi kumva njala
koma iwo amene amafunafuna Yehova sasowa kanthu kalikonse kabwino.
Khulupirira Yehova ndipo uzichita zabwino;
khazikika mʼdziko ndi kutsata zokhulupirika.
Ine ndinali wamngʼono ndipo tsopano ndakalamba
koma sindinaonepo olungama akusiyidwa
kapena ana awo akupempha chakudya.
Ndipo Mulungu wanga adzakwaniritsa zosowa zanu monga mwa chuma chake chaulemerero mwa Khristu Yesu.
Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu.
Koma muyambe mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake ndipo zinthu zonsezi zidzapatsidwa kwa inu.
Musakhale ngati iwo chifukwa Atate anu amadziwa zimene musowa musanapemphe.
"Pemphani ndipo mudzapatsidwa; funafunani ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsekulirani. Pakuti wopempha aliyense amalandira; ndi wofuna amapeza; ndipo iye amene agogoda, adzamutsekulira.
Tsono ngati inu woyipitsitsa mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanga Atate anu akumwamba sadzapereka mphatso zabwino kwa iwo amene amupempha?
Guarda e livramento
O anjo do Senhor acampa ao redor dos que o temem e os livra. Deus promete guardar todas as nossas saídas e entradas para sempre.
Mngelo wa Yehova amatchinjiriza amene amakonda Iye
ndi kuwalanditsa.
Yehova amawombola atumiki ake;
aliyense amene amathawira kwa Iye sadzapezeka wolakwa.
Ndikweza maso anga ku mapiri;
kodi thandizo langa limachokera kuti?
Thandizo langa limachokera kwa Yehova,
wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Sadzalola kuti phazi lako literereke;
Iye amene amakusunga sadzawodzera.
Taonani, Iye amene amasunga Israeli
sadzawodzera kapena kugona.
Yehova ndiye amene amakusunga;
Yehova ndiye mthunzi wako ku dzanja lako lamanja.
Dzuwa silidzakupweteka nthawi ya masana,
kapena mwezi nthawi ya usiku.
Yehova adzakuteteza ku zoyipa zonse;
adzasunga moyo wako.
Yehova adzayangʼanira kutuluka kwako ndi kulowa kwako;
kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Ndisungeni Inu Mulungu,
pakuti ine ndimathawira kwa Inu.
Ndisungeni Inu Mulungu,
pakuti ine ndimathawira kwa Inu.
Ndayika Yehova patsogolo panga nthawi zonse.
Popeza Iyeyo ali kudzanja langa lamanja,
sindidzagwedezeka.
Ndayika Yehova patsogolo panga nthawi zonse.
Popeza Iyeyo ali kudzanja langa lamanja,
sindidzagwedezeka.
Yehova akuyankhe pamene uli pa msautso;
dzina la Mulungu wa Yakobo likuteteze.
Iye atumize thandizo kuchokera ku malo ake opatulika;
akugwirizize kuchokera ku Ziyoni.
Tetezani moyo wanga ndi kundilanditsa;
musalole kuti ndichite manyazi,
pakuti ndimathawira kwa Inu.
Kukhulupirika ndi kulungama kwanga kunditeteze,
chifukwa chiyembekezo changa chili mwa Inu.
Kavalo ndi chiyembekezo cha chabechabe cha chipulumutso,
ngakhale ali ndi mphamvu yayikulu sangathe kupulumutsa.
Koma maso a Yehova ali pa iwo amene amaopa Iye;
amene chiyembekezo chawo chili mʼchikondi chake chosatha,
kuwawombola iwo ku imfa
ndi kuwasunga ndi moyo nthawi ya njala.
Ife timadikira kwa Yehova mwachiyembekezo;
Iye ndiye thandizo lathu ndi chishango chathu.
Confiança inabalável
Melhor é confiar no Senhor do que confiar no homem. Quem anda em integridade anda seguro, e a torre forte do nome do Senhor protege o justo.
Yehova ali nane; sindidzachita mantha.
Munthu angandichite chiyani?
Nʼkwabwino kuthawira kwa Yehova
kusiyana ndi kudalira munthu.
Dzina la Yehova lili ngati nsanja yolimba;
wolungama amathawiramo napulumuka.
Dzina la Yehova lili ngati nsanja yolimba;
wolungama amathawiramo napulumuka.
Amene amaopa Yehova ali ndi chitetezo chokwanira
ndipo iye adzakhala pothawira pa ana ake.
pakuti Yehova adzakulimbitsa mtima
ndipo adzasunga phazi lako kuti lisakodwe mu msampha.
Munthu woyenda mwangwiro amayenda mosatekeseka;
koma amene amayenda njira yokhotakhota adzadziwika.
"Mawu ali wonse a Mulungu ndi opanda cholakwika;
Iye ndi chishango kwa amene amathawira kwa Iye.
"Mawu ali wonse a Mulungu ndi opanda cholakwika;
Iye ndi chishango kwa amene amathawira kwa Iye.
Chilungamo chimateteza munthu wangwiro,
koma tchimo limagwetsa munthu wochimwa.
Munthu wolungama amakhala ndi zakudya zoti adye nʼkukhuta,
koma mʼmimba mwa munthu woyipa mumakhala pululu ndi njala.
Pakuti Yehova ndiye amapereka nzeru,
ndipo mʼkamwa mwake mumachokera chidziwitso ndi kumvetsa zinthu.
Anthu olungama zinthu zimawayendera bwino chifukwa Yehova amakhala nawo.
Paja Yehova ndiye chishango cha amene amayenda mwangwiro,
pakuti ndiye mlonda wa njira zolungama.
Iye amasamala mayendedwe a anthu ake okhulupirika.
Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala,
koma munthu wopusa amangopitirira ndipo amakumana ndi mavuto.
Kavalo amamukonzera tsiku la nkhondo,
koma ndi Yehova amene amapambanitsa.
Ndipotu mtima wako uziwuyangʼanira bwino ndithu
pakuti ndiwo magwero a moyo.
A presença protetora
O Senhor prometeu estar conosco e nunca nos desampara. Ele é como sombra à nossa direita e fortaleza em todo o tempo.
Khalani amphamvu ndi olimba mtima. Musachite nawo mantha kapena kunjenjemera pamaso pawo, chifukwa Yehova Mulungu wanu apita nanu. Sadzakusiyani kapena kukutayani."
Mulungu wamuyaya ndiye pothawirapo pathu,
ndipo pa dziko lapansi amakusungani ndi mphamvu zosatha.
Adzathamangitsa patsogolo panu mdani wanu,
adzanena kuti, ‘Muwonongeni!’
Za fuko la Benjamini anati:
"Wokondedwa wa Yehova akhale mwamtendere mwa Iye,
pakuti amamuteteza tsiku lonse,
ndipo amene Yehova amamukonda amawusa pa mapewa ake."
palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke,
ndipo onse okuneneza pa mlandu udzawatsutsa.
Umu ndimo adzapezekere atumiki a Yehova.
Chipambano chawo chichokera kwa Ine,"
akutero Yehova.
Inu mudzamupatsa munthu
wa mtima wokhazikika
mtendere weniweni.
Mpaka pamene mudzakalambe ndi kumera imvi
ndidzakusamalirani ndithu.
Ndinakulengani ndipo ndidzakunyamulani,
ndidzakusamalirani ndi kukulanditsani.
Monga mbalame zowuluka pamwamba pa zisa zake,
Yehova Wamphamvuzonse adzatchinjiriza Yerusalemu;
ndi kumupulumutsa,
iye adzawupitirira ndi kuwulanditsa."
phunzirani kuchita zabwino!
Funafunani chilungamo,
thandizani oponderezedwa.
Tetezani ana amasiye,
muwayimirire akazi amasiye pa milandu yawo."
Ngati muli okonzeka kundimvera
mudzadya zinthu zabwino za mʼdziko;
koma mukakana ndi kuwukira
mudzaphedwa ndi lupanga."
Pakuti Yehova wayankhula.
Yehova adzakumenyerani nkhondo. Inu mungokhala chete."
Yehova ndi wabwino,
ndiye kothawirako nthawi ya masautso.
Amasamalira amene amamudalira,
Promessas de cuidado
Deus garante que nem um fio de cabelo cairá sem sua permissão. Ele deseja que vivamos em paz, confiança e segurança total nele.
Kodi suja amagulitsa mbalame ziwiri ndi ndalama imodzi? Koma palibe imodzi ya izo imene idzagwa pansi wopanda chifuniro cha Atate anu. Ndipo ngakhale tsitsi la mʼmutu mwanu linawerengedwa kale. Potero musaope; inu ndinu a mtengo woposa mbalame zambiri.
Ngati mukhulupirira, mudzalandira chilichonse chimene muchipempha mʼpemphero."
Anthu onse adzakudani chifukwa cha Ine. Koma palibe tsitsi limodzi la mʼmutu mwanu lidzawonongeke. Mukadzalimbikira ndiye mudzapeze moyo.
Kenaka Yesu anawafunsa iwo kuti, "Ine nditakutumizani wopanda chikwama cha ndalama, thumba kapena nsapato, kodi inu munasowa kanthu?"
Iwo anayankha kuti, "Palibe chimene tinasowa."
Nanga tsono tidzanena chiyani pa izi? Ngati Mulungu ali mbali yathu, adzatitsutsa ife ndani?
Kotero ife tikunena molimba mtima kuti,
"Ambuye ndiye mthandizi wanga;
sindidzachita mantha. Munthu angandichitenji ine?"
Dziperekeni nokha kwa Mulungu. Mukaneni Mdierekezi ndipo adzakuthawani.
Chomwecho tsono, tisafanane ndi ena amene akugona koma tikhale maso ndi odzisunga.
Fidelidade e aliança
Deus é fiel à sua aliança. Ele protege cada promessa que faz e guarda os seus como a menina dos seus olhos.
Koma Ambuye ndi wokhulupirika, ndipo adzakulimbikitsani ndi kukutetezani kwa woyipayo.
Ndipo timalandira chilichonse chimene tichipempha kwa Iye, chifukwa timamvera malamulo ake ndi kuchita zimene zimamukondweretsa.
Ife timalimba mtima tikamafika pamaso pa Mulungu, popeza kuti ngati tipempha kanthu kalikonse monga mwa chifuniro chake, amatimvera. Ndipo ngati tikudziwa kuti amatimvera, chilichonse chimene timapempha, tikudziwanso kuti tili nacho chimene tamupempha Iye.
Tikudziwa kuti aliyense amene ndi mwana wa Mulungu sachimwirachimwirabe. Yesu, Mwana wa Mulungu, amamusunga ndipo woyipa uja sangamukhudze.
Ine sindikukhalanso mʼdziko lapansi nthawi yayitali, koma iwo akanali mʼdziko lapansi. Ine ndikubwera kwa Inu. Atate Woyera, atetezeni ndi mphamvu za dzina lanu. Dzina limene munandipatsa Ine, kuti iwo akhale amodzi monga Ife tili amodzi. Pamene ndinali nawo, ndinawateteza ndi kuwasunga mosamala mʼdzina limene munandipatsa. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatayika kupatula yekhayo amene anayenera kuwonongeka kuti malemba akwaniritsidwe.
Sindikupempha kuti muwachotse mʼdziko lapansi koma kuti muwateteze kwa woyipayo.
Mulungu wina ndi uti wofanana nanu Yehova?
Ndipo ndani amene ndi Thanthwe kupatula Mulungu wathu?
Ndipo tsopano chikukomereni kudalitsa banja la mtumiki wanu, kuti likhale mpaka muyaya pamaso panu. Pakuti Inu, Yehova Wamphamvuzonse, mwayankhula, ndipo ndi mʼdalitso wanu banja la mtumiki wanu lidzakhala lodalitsika mpaka muyaya."
Iye anakhazikitsa maboma mu ufumu wa Aramu wa ku Damasiko, ndipo Aaramu anakhala pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho. Yehova ankamupatsa chipambano Davide kulikonse kumene ankapita.
Ineyo ndinali nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndachotsa adani ako onse pamaso pako. Tsopano ndidzakuza dzina lako kuti likhale mʼgulu la mayina a anthu otchuka kwambiri pa dziko lapansi.
" ‘Tsatirani malangizo anga ndipo mverani mosamala malamulo anga ndipo mudzakhala mʼdzikomo mwamtendere.
Pangano langa ndi ili: Ine ndilonjeza kuti sindidzawononganso zamoyo ndi madzi a chigumula. Chigumula sichidzawononganso dziko lapansi."
Zoonadi Ambuye Yehova sachita kanthu
asanawulule zimene akufuna kuchita
kwa atumiki ake, aneneri.
Provisão diária
Deus satisfaz os desejos do coração dos seus filhos. Ele abençoa, renova as forças e sustenta dia após dia quem nele confia.
Musandichotsere chifundo chanu Yehova;
chikondi chanu ndi choonadi chanu zinditeteze nthawi zonse.
Tulani nkhawa zanu kwa Yehova
ndipo Iye adzakulimbitsani;
Iye sadzalola kuti wolungama agwe.
Koma ine ndidzayimba za mphamvu yanu,
mmawa ndidzayimba zachikondi chanu;
pakuti ndinu linga langa,
pothawirapo panga mʼnthawi ya mavuto.
Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu;
onse amene amalumbira mʼdzina la Mulungu adzalemekeza Mulunguyo,
koma pakamwa pa anthu onama padzatsekedwa.
Imbirani Mulungu imbirani dzina lake matamando,
mukwezeni Iye amene amakwera pa mitambo;
dzina lake ndi Yehova ndipo sangalalani pamaso pake.
Atate wa ana amasiye, mtetezi wa akazi amasiye,
ndiye Mulungu amene amakhala mʼmalo oyera.
Matamando akhale kwa Ambuye, kwa Mulungu Mpulumutsi wathu
amene tsiku ndi tsiku amasenza zolemetsa zathu.
Ine ndine Yehova Mulungu wanu,
amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto.
Yasamani kukamwa kwanu ndipo ndidzakudyetsani.
Pakuti Yehova Mulungu ndi dzuwa ndi chishango;
Yehova amapereka chisomo ndi ulemu;
Iye sawamana zinthu zabwino
iwo amene amayenda mwangwiro.
Iwo amene amakonda Yehova adane ndi zoyipa
pakuti Iye amayangʼanira miyoyo ya amene amamukhulupirira
ndipo amawapulumutsa mʼdzanja la anthu oyipa
Yehova amateteza munthu wodzichepetsa mtima;
pamene ndinali ndi chosowa chachikulu, Iye anandipulumutsa.
Pumula iwe moyo wanga,
pakuti Yehova wakuchitira zokoma.
Pakuti Inu Yehova mwapulumutsa moyo wanga ku imfa,
maso anga ku misozi,
mapazi anga kuti angapunthwe,
kuti ine ndiyende pamaso pa Yehova
mʼdziko la anthu amoyo.
Inu ndinu pothawirapo panga ndi chishango changa;
chiyembekezo changa chili mʼmawu anu.
Yehova akapanda kumanga nyumba,
omanga nyumbayo agwira ntchito pachabe.
Yehova akapanda kulondera mzinda,
mlonda akanangolondera pachabe.
"Pano ndidzachulukitsa mphamvu za Davide
ndi kuyikapo nyale ya wodzozedwa wanga.
Ndidzaveka adani ake manyazi,
koma chipewa chaufumu pamutu pake chidzakhala chowala."
Yehova adzakwaniritsa cholinga chake pa ine;
chikondi chanu chosasinthika Yehova, ndi chosatha
musasiye ntchito ya manja anu.
Mumatsekula dzanja lanu
ndi kukwaniritsa zokhumba za chamoyo chilichonse.
Iye amachitira chilungamo anthu oponderezedwa
ndipo amapereka chakudya kwa anthu anjala.
Yehova amamasula amʼndende,
Yehova amatsekula maso anthu osaona,
Yehova amadzutsa onse amene awerama pansi,
Yehova amakonda anthu olungama.
Yehova amasamalira alendo
ndipo amathandiza ana ndi akazi amasiye,
koma amasokoneza njira za anthu oyipa.
Ine ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere,
pakuti Inu nokha, Inu Yehova,
mumandisamalira bwino.
Valani zida zonse za Mulungu kuti muthe kuyima ndi kukana machenjerero a Satana.
Valani zida zonse za Mulungu kuti muthe kuyima ndi kukana machenjerero a Satana. Pakuti sitikulimbana ndi thupi ndi magazi, koma tikulimbana ndi maufumu, maulamuliro, mphamvu za dziko la mdima, ndi mphamvu zoyipa kwambiri zauzimu zamlengalenga.
"Kodi munthu angathe kuba za Mulungu? Komatu inu mumandibera.
"Koma inu mukufunsa kuti, ‘Kodi timakuberani motani?’
"Pa zakhumi ndi pa zopereka. Mtundu wanu wonse ndinu otembereredwa, chifukwa mukundibera. Bweretsani chakhumi chathunthu ku nyumba yosungira, kuti mukhale chakudya mʼnyumba mwanga." Akutero Yehova Wamphamvuzonse, "Tandiyesani, ndipo muone ngati sindidzatsekula zipata zakumwamba, ndi kukugwetserani madalitso ochuluka amene mudzasowe malo owayikamo.
Ndidzakhazika anthu anga pafupi ndi phiri langa loyera ndipo ndidzawadalitsa. Ndidzawagwetsera mvula pa nthawi yake ndipo idzakhala mvula ya madalitso.
Nzeru ndi chitetezo,
monganso ndalama zili chitetezo,
koma phindu la chidziwitso ndi ili:
kuti nzeru zimasunga moyo wa munthu amene ali nazo nzeruzo.
Chomwechonso Ambuye akulamula kuti wolalikira Uthenga Wabwino azilandira thandizo lawo polalikira Uthenga Wabwinowo.
Pakuti kukonda ndalama ndiye muzu wa zoyipa za mitundu yonse. Anthu ena ofunitsitsa ndalama, asochera ndipo asiya njira yachikhulupiriro ndipo adzitengera zowawitsa zambiri.
Ndidzatsitsimutsa anthu otopa ndipo ndidzadyetsa anthu anjala."
Nʼchifukwa chake ndikuvutika monga ndililimu. Komabe zimenezi sizikundichititsa manyazi, popeza ndikumudziwa amene ndamukhulupirira ndipo ndikutsimikiza mtima kuti akhoza kusamalira chimene ndinamusungitsa mpaka tsiku lijalo.