Publicidade

Proximidade

Por Bíblia Online

Deus é próximo dos que o buscam. Ele não é um Deus distante, mas presente, íntimo e acessível a todo o que o invoca com sinceridade de coração.

Buscar a presença de Deus

A Bíblia nos exorta a buscar a face do Senhor continuamente. Quem se aproxima dele encontra plenitude de alegria e delícias perpétuas.

Dalirani Yehova ndi mphamvu zake;

funafunani nkhope yake nthawi yonse.

Dalirani Yehova ndi mphamvu zake;

funafunani nkhope yake nthawi zonse.

Funafunani Yehova pamene Iye akupezeka.

Mupemphere kwa Iye pamene ali pafupi.

Chinthu chimodzi chokha chimene ndipempha kwa Yehova,

ichi ndi chimene ndidzachifunafuna:

kuti ndikhale mʼNyumba ya Yehova

masiku onse a moyo wanga,

ndi kuyangʼana kukongola kwa Yehova,

ndi kumufunafuna Iye mʼNyumba yake.

Nʼkwabwino kukhala mʼmabwalo anu tsiku limodzi

kuposa kukhala kwina kwake kwa zaka 1,000;

Ine ndingakonde kukhala mlonda wa pa khomo la Nyumba ya Mulungu wanga

kuposa kukhala mʼmatenti a anthu oyipa.

Inu mwandidziwitsa njira ya moyo;

mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu,

ndidzasangalala mpaka muyaya pa dzanja lanu lamanja.

Deus está perto

O Senhor está perto dos que o invocam, dos quebrantados de coração e dos que clamam por socorro. Sua presença nos sustenta.

Olungama amafuwula, ndipo Yehova amawamva;

Iye amawalanditsa ku mavuto awo onse.

Yehova ali pafupi kwa osweka mtima

ndipo amapulumutsa iwo amene asweka mu mzimu.

Kufatsa kwanu kuzioneka pamaso pa anthu onse. Ambuye anu ali pafupi.

Koma tsopano mwa Khristu Yesu, inu amene nthawi ina munali kutali, mwabweretsedwa pafupi kudzera mʼmagazi a Khristu.

Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsata

masiku onse a moyo wanga,

ndipo ndidzakhala mʼNyumba ya Yehova

kwamuyaya.

A presença que nunca abandona

Deus promete nunca nos deixar. Ele permanece fiel, está conosco em todo tempo e envia o Espírito para habitar em nossos corações.

Ine sindikusiyani nokha kuti mukhale ana amasiye. Ine ndidzabweranso kwa inu.

Yehova Mulungu wathu akhale nafe monga momwe anakhalira ndi makolo athu; asatisiye kapena kutitaya.

Komabe mwachifundo chanu chachikulu simuwatheretu kapena kuwataya pakuti ndinu Mulungu wokoma mtima ndi wachifundo.

Tsopano Ambuye mwini mtendere akupatseni mtendere nthawi zonse mwa njira iliyonse. Ambuye akhale ndi inu nonse.

Potsiriza abale, ndikuti tsalani bwino. Yesetsani kukhala angwiro, mvetsetsani pempho langa, khalani a mtima umodzi, khalani mwamtendere. Ndipo Mulungu wachikondi ndi mtendere adzakhala nanu.

Ife tikudziwa kuti timakhala mwa Iye ndipo Iyeyo amakhala mwa ife chifukwa anatipatsa Mzimu wake.

Palibe munthu amene anaona Mulungu, koma Mwana mmodzi yekhayo amene ali wa pamtima pa Atate, ndiye anafotokoza za Iye.

Mose anakhala kumeneko pamodzi ndi Yehova masiku 40, usana ndi usiku, wosadya kanthu kapena kumwa madzi. Ndipo iye analemba pa miyala ija mawu a pangano, malamulo khumi.

Chiritsani odwala amene ali kumeneko ndipo muwawuze kuti, ‘Ufumu wa Mulungu wayandikira.’

Asa Akonza Chipembedzo

Mzimu wa Mulungu unabwera pa Azariya mwana wa Odedi. Iye anapita kukakumana ndi Asa ndipo anati kwa iye, "Tandimverani, inu Asa ndi Ayuda onse ndi Benjamini. Yehova ali ndi inu, inunso mukakhala naye. Ngati inu mumufunafuna Iye mudzamupeza, koma ngati mumusiya, Iye adzakusiyani. Kwa nthawi yayitali Israeli anali wopanda Mulungu weniweni, wopanda wansembe wophunzitsa ndi wopanda malamulo. Koma pamene anali pa mavuto anatembenukira kwa Yehova, Mulungu wa Israeli ndi kufunafuna Iye, ndipo anamupeza. Masiku amenewo sikunali kwabwino kuyenda ulendo, pakuti anthu onse okhala mʼdziko anali pa mavuto aakulu. Mtundu umodzi umakanthidwa ndi mtundu wina ndipo mzinda wina umakanthidwa ndi mzinda wina, pakuti Mulungu amawasautsa ndi mazunzo a mtundu uliwonse. Koma inu, khalani amphamvu ndipo musataye mtima, pakuti mudzalandira mphotho ya ntchito yanu."

Asa atamva mawu awa ndiponso uneneri wa Azariya mwana wa Odedi, analimba mtima. Iye anachotsa mafano onse onyansa mʼdziko lonse la Yuda ndi Benjamini ndi mʼmizinda yonse imene analanda a ku mapiri a Efereimu. Iye anakonzetsa guwa lansembe la Yehova limene linali kutsogolo kwa khonde la Nyumba ya Mulungu.

Kenaka anasonkhanitsa anthu onse a ku Yuda ndi Benjamini ndiponso anthu ochokera ku Efereimu, Manase ndi Simeoni amene ankakhala pakati pawo, pakuti gulu lalikulu linabwera kwa iye kuchokera ku Israeli litaona kuti anali ndi Yehova Mulungu wake.

Iwo anasonkhana mu Yerusalemu mwezi wachitatu wa chaka cha 15 cha ulamuliro wa Asa. Pa nthawi imeneyi anapereka nsembe kwa Yehova, ngʼombe 700 ndiponso nkhosa ndi mbuzi 7,000 zochokera pa zolanda ku nkhondo zimene anabweretsa. Iwo anachita pangano loti azifunafuna Yehova, Mulungu wa makolo awo, ndi mtima ndi moyo wawo wonse. Aliyense wosafunafuna Yehova Mulungu wa Israeli aziphedwa, kaya ndi wamngʼono kapena wamkulu, mwamuna kapena mkazi. Iwo analumbira kwa Yehova, mokweza mawu, akuyimba malipenga ndi mbetete. Anthu onse a ku Yuda anakondwera pa kulumbirako chifukwa analumbira ndi mtima wawo wonse. Iwo anafunafuna Mulungu mwachidwi, ndipo anamupeza Iye. Kotero Yehova anawapatsa mpumulo mbali zonse.

Mfumu Asa anachotsanso Maaka agogo ake pa udindo wa amayi a mfumu chifukwa anapanga fano lonyansa la Asera. Asa anagwetsa fanolo, naliswa ndipo kenaka anakaliwotcha ku chigwa cha Kidroni. Ngakhale kuti sanachotse malo opembedzerako mafano mu Israeli, mtima wa Asa unali wodzipereka kwathunthu kwa Yehova, masiku onse a moyo wake. Iye anabweretsanso mʼNyumba ya Mulungu zipangizo zasiliva, golide ndi ziwiya zina zimene iyeyo ndi abambo ake anazipatula.

Panalibenso nkhondo mpaka chaka cha 35 cha ufumu wa Asa.

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-22_10-02-25-