Pular para o conteúdo
Publicidade

Reino dos céus

Por Bíblia Online

O Reino dos Céus é comparado por Jesus a tesouros, sementes e redes. Através de parábolas, Ele revelou os mistérios de um Reino que já está entre nós, mas que se consumará na eternidade.

O valor incomparável do Reino

O Reino dos Céus é como um tesouro escondido ou uma pérola de grande valor. Quem o encontra, vende tudo para possuí-lo.

Fanizo la Chuma Chobisika ndi la Ngale

"Ufumu wakumwamba ufanana ndi chuma chobisika mʼmunda. Munthu atachipeza anachibisanso ndipo ndi chimwemwe anapita nakagulitsa zonse anali nazo, nakagula mundawo.

"Komanso Ufumu wakumwamba ufanana ndi wogulitsa malonda amene amafuna ngale zabwino. Atapeza imodzi ya mtengowapatali, iye anapita nakagulitsa chilichonse anali nacho ndi kukayigula."

Fanizo la Mbewu ya Mpiru ndi Yisiti

Iye anawawuza fanizo lina kuti, "Ufumu wakumwamba uli ngati mbewu ya mpiru, imene munthu anatenga ndi kudzala mʼmunda mwake. Ngakhale mbewuyi ndi yayingʼono mwa mbewu zanu zonse za mʼmunda, imakula ndi kukhala mtengo kotero kuti mbalame zamlengalenga zimabwera ndi kupumula mʼnthambi zake."

Iye anawawuzanso fanizo lina nati: "Ufumu wakumwamba ufanana ndi yisiti amene mayi anatenga ndi kusakaniza mu ufa wambiri mpaka wonse unafufuma."

Parábolas do Reino

Jesus ensinou sobre o Reino mediante parábolas que revelam seu crescimento, seu juízo e a separação final entre justos e injustos.

Fanizo la Namsongole

Yesu anawawuza fanizo lina kuti: "Ufumu wakumwamba ufanana ndi munthu amene anafesa mbewu zabwino mʼmunda mwake. Koma aliyense akugona usiku mdani wake anabwera ndi kufesa namsongole pakati pa tirigu ndipo anachoka. Pamene tirigu anamera ndi kutulutsa ngala, namsongole anaonekanso.

"Antchito ake anabwera kwa iye ndi kuti, Bwana, kodi simunafese mbewu zabwino mʼmunda mwanu? Nanga namsongole wachokera kuti?

"Iye anayankha kuti, Ndi mdani amene anachita izi.

"Antchito anamufunsa iye kuti, Kodi mufuna kuti tipite tikamuzule?

"Iye anakana nati, Ayi. Chifukwa pamene mukuzula namsongoleyo mwina inu mungazulire pamodzi ndi tirigu. Zisiyeni zonse zikulire pamodzi mpaka nthawi yokolola. Pa nthawi imeneyo ndidzawuza okolola kuti: Poyamba sonkhanitsani namsongole ndi kumumanga mʼmitolo kuti atenthedwe, kenaka sonkhanitsani tirigu ndi kumuyika mʼnkhokwe yanga.’ "

Yesu Awatanthauzira Fanizo la Namsongole

Kenaka Iye anasiya gulu la anthu ndi kukalowa mʼnyumba. Ophunzira ake anapita kwa Iye nati, "Timasulireni fanizo la namsongole mʼmunda."

Iye anayankha nati, "Munthu amene anafesa mbewu yabwino ndi Mwana wa Munthu. Munda ndi dziko lapansi ndipo mbewu yabwino ndi ana a ufumu. Namsongole ndi ana a woyipayo. Ndipo amene anafesa namsongole ndi Satana. Kukolola ndiko kutha kwa dzikoli ndipo otuta ndi angelo.

"Monga momwe namsongole azulidwa ndi kutenthedwa ndi moto, momwemonso kudzakhala pakutha kwa dziko. Mwana wa Munthu adzatumiza angelo ake ndipo iwo adzachotsa mu ufumu wake chilichonse chochimwitsa ndi onse amene amachita zoyipa. Adzawaponya mʼngʼanjo yamoto kumene kudzakhala kulira ndi kukuta mano. Pamenepo olungama adzawala ngati dzuwa mu ufumu wa Atate awo. Amene ali ndi makutu amve."

Fanizo la Khoka

"Komanso Ufumu wakumwamba ufanana ndi khoka limene linaponyedwa mʼnyanja ndipo linakola mitundu yonse ya nsomba. Litadzaza, asodzi analikokera ku mtunda. Pomwepo anakhala pansi nasonkhanitsa nsomba zabwino mʼmadengu koma zoyipa anazitaya. Umu ndi mmene kudzakhalira pakutha kwa dziko. Angelo adzabwera ndi kulekanitsa oyipa ndi olungama. Ndipo oyipa adzawaponya mʼngʼanjo ya moto kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano."

Quem herda o Reino

Os humildes, os pobres de espírito e as crianças são herdeiros do Reino. Mas é difícil para os ricos entrarem nele.

"Odala ndi amene ali osauka mu mzimu,

chifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo.

Odala ndi amene ali achisoni,

chifukwa adzatonthozedwa.

Odala ndi amene ali ofatsa,

chifukwa adzalandira dziko lapansi.

Odala ndi amene akumva njala ndi ludzu la chilungamo,

chifukwa adzakhutitsidwa.

Odala ndi amene ali ndi chifundo,

chifukwa adzawachitira chifundo.

Odala ndi amene ali oyera mtima,

chifukwa adzaona Mulungu.

Ndi odala amene amabweretsa mtendere,

chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.

Odala ndi amene akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo,

pakuti ufumu wakumwamba ndi wawo."

"Inu ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani, kukunenerani zoyipa zilizonse ndi kukunamizirani chifukwa cha Ine. Sangalalani, kondwerani chifukwa mphotho yanu ndi yayikulu kumwamba, chifukwa moterenso ndi mmene anazunzira aneneri inu musanabadwe.

Wamkulu mu Ufumu Wakumwamba

Pa nthawi imeneyo ophunzira anabwera kwa Yesu ndipo anamufunsa kuti, "Wamkulu woposa onse ndani mu ufumu wakumwamba?"

Iye anayitana kamwana kakangʼono ndi kukayimiritsa pakati pawo. Ndipo Iye anati, "Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati simusintha ndi kukhala ngati tiana tatingʼono, simudzalowa konse mu ufumu wakumwamba. Chifukwa chake, aliyense amene adzichepetsa yekha ngati kamwana aka, ameneyo ndiye wamkulu koposa onse mu ufumu wakumwamba.

Yesu anati, "Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse pakuti ufumu wakumwamba ndi wa iwo onga anawa."

Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake, "Zoonadi, ndikuwuzani kuti nʼkovuta kuti olemera akalowe mu ufumu wakumwamba. Komanso ndikuwuzani kuti, nʼkwapafupi kuti ngamira idzere pa kabowo ka zingano kusiyana ndi kuti wolemera akalowe mu ufumu wa Mulungu."

Ophunzira atamva zimenezi, anadabwa kwambiri ndipo anamufunsa kuti, "Nanga angapulumuke ndani?"

Yesu anawayangʼana iwo nati, "Ndi anthu, izi nʼzosatheka, koma ndi Mulungu zinthu zonse zimatheka."

Tamverani abale anga okondedwa, kodi Mulungu sanasankhe amene dziko lapansi limawaona ngati amphawi kuti akhale olemera mʼchikhulupiriro ndi kulowa ufumu umene Iye analonjeza kwa amene amamukonda?

Koma oyera mtima a Wammwambamwamba adzalandira ufumu ndipo udzakhala nawo mpaka muyaya, inde ku nthawi zonse.

Buscar o Reino acima de tudo

Jesus ensinou que devemos buscar primeiro o Reino e sua justiça. Nem todo que diz 'Senhor, Senhor' entrará — só quem faz a vontade do Pai.

Ophunzira Owona ndi Onyenga

"Si munthu aliyense amene amanena kwa Ine, Ambuye, Ambuye,adzalowe mu ufumu wakumwamba, koma ndi yekhayo amene amachita chifuniro cha Atate anga amene ali kumwamba.

Chifukwa chake aliyense amene aphwanya limodzi la malamulowa ngakhale lalingʼonongʼono ndi kuphunzitsa ena kuti achite chimodzimodzi, adzakhala wotsirizira mu ufumu wakumwamba, koma aliyense amene achita ndi kuphunzitsa malamulo awa adzakhala wamkulu mu ufumu wakumwamba. Chifukwa chake ndikuwuzani kuti ngati chilungamo chanu sichiposa cha Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo, zoonadi, simudzalowa mu ufumu wakumwamba.

"Chifukwa chake pempherani motere:

" Atate athu akumwamba,

dzina lanu lilemekezedwe,

Ufumu wanu ubwere,

chifuniro chanu chichitike

pansi pano monga kumwamba.

Yohane Mʼbatizi

Mʼmasiku amenewo, Yohane Mʼbatizi anadza nalalikira mʼchipululu cha Yudeya kuti, "Tembenukani mtima chifukwa ufumu wakumwamba wayandikira."

Kuyambira nthawi imeneyo, Yesu anayamba kulalikira nati, "Tembenukani mtima ufumu wakumwamba wayandikira."

Pamene mukupita, muzikalalikira uthenga uwu: Ufumu wakumwamba wayandikira.

Ndikuwuzani kuti ambiri adzabwera kuchokera kummawa ndi kumadzulo, nadzakhala nawo pa phwando pamodzi ndi Abrahamu, Isake ndi Yakobo mu ufumu wakumwamba.

Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti pakati pa obadwa ndi mkazi sipanaoneke wina aliyense wamkulu woposa Yohane Mʼbatizi; komatu amene ndi wamngʼono kwambiri mu ufumu wakumwamba ndi wamkulu koposa iye. Kuyambira masiku a Yohane Mʼbatizi mpaka tsopano, ufumu wakumwamba ndi wolimbirana ndipo anthu amphamvu okha ndi amene akuwulanda.

A herança eterna

O Reino dos Céus é inabalável e eterno. Deus nos chama a fazer firme a nossa vocação e eleição para entrar nesse Reino.

Popeza tikulandira ufumu umene sungagwedezeke, tiyeni tikhale oyamika ndi kupembedza Mulungu movomerezeka ndi mwaulemu ndi mantha. Pakuti Mulungu wathu ndi moto wonyeketsa.

Iwo adzafotokoza za ulemerero wa ufumu wanu

ndi kuyankhula za mphamvu yanu,

kuti anthu onse adziwe za machitidwe anu amphamvu

ndi ulemerero wokongola wa ufumu wanu.

Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya,

ndipo ulamuliro wanu ndi wosatha pa mibado yonse.

Yehova ndi wokhulupirika pa malonjezo ake onse

ndi wokonda zonse zimene Iye anazipanga.

Nʼchifukwa chake abale anga, funitsitsani kuti mayitanidwe ndi masankhidwe anu akhale otsimikizika. Pakuti ngati muchita zinthu izi, simudzagwa konse. Mudzalandiridwa bwino kwambiri mu ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.

Ambuye adzandilanditsa ku chilichonse chofuna kundichita choyipa ndipo adzandisamalira bwino mpaka kundilowetsa chonse mu ufumu wake wakumwamba. Kwa Iye kukhale ulemerero mpaka muyaya.

Chuma cha Kumwamba

"Musachite mantha, inu kagulu kankhosa, pakuti zinakondweretsa Atate anu kuti akupatseni ufumu.

Dziwani ichi, palibe wadama, wochita zonyansa kapena waumbombo, munthu wotero ali ngati wopembedza mafano, amenewa alibe malo mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu.

Seja o primeiro