Publicidade

Repouso e férias

Por Bíblia Online

Deus criou o descanso como parte da vida. O sábado, o repouso e até as férias refletem a confiança de que Deus sustenta todas as coisas — mesmo quando paramos.

O descanso como ordenança

Deus descansou no sétimo dia e nos convidou a fazer o mesmo. O descanso sabático é um presente de Deus para restauração do corpo e da alma.

Kotero tsono kwatsala mpumulo wa Sabata kwa anthu a Mulungu; Pakuti aliyense amene analowa mu mpumulo wa Mulungu anapuma pa ntchito zake, monga momwe Mulungu anachitira.

"Muzisunga osaphwanya Sabata;

musamachite zimene mukufuna pa masiku anga opatulika,

tsiku la Sabata lizikhala tsiku lachisangalalo.

Tsiku lopatulika la Yehova muzililemekeza

posayenda mʼnjira zanu,

kapena kuchita zimene mukufuna ndi kuyankhula zopandapake,

mukatero mudzapeza chimwemwe mwa Yehova,

ndipo ndidzakukwezani ndi kukupambanitsani pa dziko lonse lapansi.

Mudzadyerera dziko limene ndinapatsa Yakobo kholo lanu."

Yehova wayankhula ndi pakamwa pake.

Nʼchifukwa chake chilichonse mungadye kapena kumwa, kapena chimene mungachite, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.

Sono e paz

Ditar-se em paz e dormir tranquilamente é bênção do Senhor. Quem confia nele dorme sem medo e acorda renovado.

Ine ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere,

pakuti Inu nokha, Inu Yehova,

mumandisamalira bwino.

Ine ndimagona ndi kupeza tulo;

ndimadzukanso chifukwa Yehova amandichirikiza.

Mumangodzivuta nʼkulawirira mmamawa

ndi kusagona msanga madzulo,

kuvutikira chakudya choti mudye,

pakuti Iye amapereka tulo kwa amene amawakonda.

Sudzachita mantha ndi zoopsa za usiku,

kapena muvi wowuluka masana,

pamene ugona pansi, sudzachita mantha;

ukadzagona pansi tulo tako tidzakhala tokoma.

Wantchito amagona tulo tabwino

ngakhale adye pangʼono kapena kudya kwambiri,

koma munthu wolemera, chuma

sichimulola kuti agone.

Descanso e segurança

No repouso, encontramos segurança. Deus guarda os justos, e mesmo no silêncio da noite, sua paz nos protege e restaura.

Udzalimba mtima popeza pali chiyembekezo;

ndipo udzayangʼana mbali zonse ndi kugona mosatekeseka.

Udzagona pansi, popanda wina wokuopseza

ndipo ambiri adzakupempha kuti uwachitire chifundo.

Iwo amene amakhala moyo wolungama

amafa mwamtendere;

amapeza mpumulo pamene agona mu imfa.

Seja o primeiro
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-07-04_23-13-58-