Publicidade

Descansar no Senhor

Por Bíblia Online

Descansar no Senhor é um ato de fé. Em um mundo agitado, Deus nos convida a entregar nossas ansiedades, aquietar o coração e confiar plenamente em sua provisão e cuidado.

O convite ao descanso

Jesus convida os cansados e sobrecarregados a irem a Ele e encontrar descanso para as suas almas. O jugo dele é leve.

"Idzani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa. Ndipo inu mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa ndi losavuta ndipo katundu wanga ndi wopepuka."

Khala chete pamaso pa Yehova ndipo umudikire mofatsa;

usavutike pamene anthu apambana mʼnjira zawo,

pamene iwo achita zinthu zawo zoyipa.

Iye akuti, "Khala chete, ndipo dziwa kuti ndine Mulungu;

ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu;

ine ndidzakwezedwa mʼdziko lapansi."

Dalirani Iye nthawi zonse, inu anthu;

khuthulani mitima yanu kwa Iye,

pakuti Mulungu ndiye pothawirapo pathu.

Sela

Confiança e paz

Quem confia no Senhor encontra paz perfeita. A ansiedade perde o poder quando entregamos tudo nas mãos do Deus soberano.

Inu mudzamupatsa munthu

wa mtima wokhazikika

mtendere weniweni.

Zimene Ambuye Yehova, Woyerayo wa Israeli ananena ndi izi:

"Ngati mubwerera ndi kupuma mudzapulumuka,

ngati mukhala chete ndi kukhulupirira mudzakhala amphamvu,

koma inu munakana zimenezi.

Mtendere udzakhala chipatso chachilungamo;

zotsatira za chilungamo zidzakhala bata ndi kudzidalira mpaka muyaya.

koma iwo amene amakhulupirira Yehova

adzalandira mphamvu zatsopano.

Adzawuluka ngati chiwombankhanga;

adzathamanga koma sadzalefuka,

adzayenda koma sadzatopa konse.

Ndipo mtendere wa Mulungu, umene upambana nzeru zonse udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Tayani pa Iye nkhawa zanu zonse chifukwa ndiye amakusamalani.

Esperar no Senhor

Esperar no Senhor renova as forças. A Bíblia nos ensina que aquietar-se diante de Deus e confiar em seu tempo é marca da maturidade espiritual.

Dikirani pa Yehova;

khalani anyonga ndipo limbani mtima

nimudikire Yehova.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

Mofatsa ndinadikira Yehova

Iye anatembenukira kwa ine ndipo anamva kulira kwanga.

Tulani nkhawa zanu kwa Yehova

ndipo Iye adzakulimbitsani;

Iye sadzalola kuti wolungama agwe.

Kwiyani koma musachimwe;

pamene muli pa mabedi anu,

santhulani mitima yanu ndi kukhala chete.

Sela

Yehova ndi wabwino kwa amene amayembekezera Iye,

kwa munthu amene amafunafuna Iyeyo;

nʼkwabwino kudikira chipulumutso cha

Yehova modekha.

A fidelidade de Deus

Deus é fiel. Seus planos são de paz e esperança. Podemos descansar sabendo que Ele guarda e sustenta quem nele confia.

Pakuti Ine ndikudziwa zimene ndinakukonzerani," akutero Yehova, "ndimalingalira zabwino zokhazokha za inu osati zoyipa, ayi. Ndimalingalira zinthu zokupatsani chiyembekezo chenicheni pa za mʼtsogolo. Nthawi imeneyo mudzandiyitana, ndi kunditama mopemba ndipo ndidzakumverani. Mudzandifunafuna ndipo mudzandipeza. Mukadzandifuna ndi mtima wanu wonse

"Koma ndi wodala munthu amene amadalira Yehova,

amene amatsamira pa Iye.

Adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmphepete mwa madzi

umene umatambalitsa mizu yake mʼmbali mwa mtsinje.

Mtengowo suopa pamene kukutentha;

masamba ake amakhala obiriwira nthawi zonse.

Suchita mantha pa chaka cha chilala

ndipo sulephera kubereka chipatso."

Yehova anayankha kuti, "Ine ndemwe ndidzapita pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakupatsa mpumulo."

Nʼchifukwa chake ndikuvutika monga ndililimu. Komabe zimenezi sizikundichititsa manyazi, popeza ndikumudziwa amene ndamukhulupirira ndipo ndikutsimikiza mtima kuti akhoza kusamalira chimene ndinamusungitsa mpaka tsiku lijalo.

Iye anati kwa Yuda "Tiyeni timange mizinda iyi ndipo timange makoma ndi nsanja, zitseko ndi zotchinga. Dzikoli likanali lathu chifukwa tafuna Yehova Mulungu wathu; tinamufuna Iye ndipo watipatsa mpumulo mbali zonse." Kotero iwo anamanga ndi kukhala pa ulemerero.

Atakafika ku mathero a mzindawo, Samueli anati kwa Sauli, "Muwuzeni mnyamata wanu kuti atsogole, koma inuyo muyime pangʼono kuti ndikuwuzeni mawu ochokera kwa Mulungu."

Seja o primeiro
Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-