Publicidade

Salvação

Por Bíblia Online

A salvação é a obra suprema de Deus. Pela graça, mediante a fé, somos salvos — não por obras, para que ninguém se glorie. É o presente mais precioso que a humanidade pode receber.

A salvação pela graça

A salvação é dom de Deus, não resultado de esforço humano. Somos justificados pela fé em Cristo Jesus e reconciliados com Deus pelo seu amor.

Pakuti mwapulumutsidwa mwachisomo, kudzera mʼchikhulupiriro ndipo izi sizochokera mwa inu eni, koma ndi mphatso ya Mulungu, osati ndi ntchito, kuti wina aliyense asadzitamandire.

Iye anatipulumutsa, osati chifukwa cha ntchito zathu zolungama zimene tinachita koma chifukwa cha chifundo chake. Anatipulumutsa potisambitsa, kutibadwitsa kwatsopano ndi kutikonzanso mwa Mzimu Woyera

Iye anatipulumutsa ndipo anatiyitanira ku moyo oyera mtima, osati chifukwa cha chilichonse chimene tinachita, koma chifukwa cha chikonzero ndi chisomo chake. Chisomo chimenechi anatipatsa ife mwa Khristu Yesu nthawi isanayambe.

Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino chifukwa ndiwo mphamvu za Mulungu zopulumutsa aliyense amene akhulupirira, poyamba Myuda, kenaka Mhelene.

pakuti onse anachimwa naperewera pa ulemerero wa Mulungu

Sizichitika kawirikawiri kuti munthu wina afere munthu wolungama, ngakhale kuti chifukwa cha munthu wabwino wina atha kulimba mtima kumufera. Koma Mulungu anaonetsa chikondi chake kwa ife chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu anatifera.

Pakuti malipiro a tchimo ndi imfa, koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

O caminho da salvação

Quem confessa Jesus como Senhor e crê em sua ressurreição será salvo. A fé em Cristo é o único caminho para a salvação.

kuti ngati udzavomereza ndi pakamwa pako kuti, "Yesu ndiye Ambuye," ndi kukhulupirira mu mtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka. Pakuti ndi mtima wanu mukhulupirira ndi kulungamitsidwa, ndipo ndi pakamwa panu muvomereza ndi kupulumutsidwa.

Pakuti ndi mtima wanu mukhulupirira ndi kulungamitsidwa, ndipo ndi pakamwa panu muvomereza ndi kupulumutsidwa.

Iwo anayankha kuti, "Khulupirira Ambuye Yesu ndipo udzapulumuka, iwe ndi a mʼbanja lako."

Iwo anayankha kuti, "Khulupirira Ambuye Yesu ndipo udzapulumuka, iwe ndi a mʼbanja lako."

Chipulumutso sichipezeka mwa wina aliyense; pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo limene lapatsidwa kwa anthu limene tiyenera kupulumutsidwa nalo."

Ndipo aliyense amene adzayitana

pa dzina la Ambuye adzapulumuka.

Yesu anayankha kuti, "Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate popanda kudzera mwa Ine.

"Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha.

Koma kwa onse amene anamulandira Iye, kwa amene anakhulupirira mʼdzina lake, Iye anawapatsa mphamvu yokhala ana a Mulungu;

Nova vida em Cristo

Quem está em Cristo é nova criação. A salvação não é apenas perdão, mas transformação completa — de dentro para fora, para a glória de Deus.

Nʼchifukwa chake, ngati munthu aliyense ali mwa Khristu, ndi wolengedwa kwatsopano; zinthu zakale zapita taonani, zakhala zatsopano.

Poyankha Yesu ananena kuti, "Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti, ngati munthu sabadwanso mwatsopano sangathe kuona ufumu wa Mulungu."

Ndipo Iye anati, "Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati simusintha ndi kukhala ngati tiana tatingʼono, simudzalowa konse mu ufumu wakumwamba.

Koma tikavomereza machimo athu, Iye ndi wokhulupirika ndi wolungama ndipo adzatikhululukira machimo athu, nadzatiyeretsa ndi kutichotsera chosalungama chilichonse.

Ambuye sazengereza kuchita zimene analonjeza, monga ena amaganizira. Iwo akukulezerani mtima, sakufuna kuti aliyense awonongeke, koma akufuna kuti aliyense alape.

Taonani ndayima pa khomo ndikugogoda. Ngati wina amva mawu anga natsekula chitseko, Ine ndidzalowamo ndi kudya naye, Ine ndi iyeyo.

Segurança eterna

O crente tem a certeza da salvação. Ninguém pode arrebatar da mão de Deus aqueles que Ele chamou, justificou e glorificou.

Ine ndimazipatsa moyo wosatha ndipo sizidzawonongeka. Palibe amene adzazikwatula mʼdzanja langa.

Aliyense wokhulupirira Mwanayo ali ndi moyo wosatha, koma iye amene samvera Mwanayo sadzawuona moyo, pakuti mkwiyo wa Mulungu umakhala pa iye."

Ngakhale kuti simunamuone, mumamukonda; ndipo ngakhale kuti simukumuona tsopano, mumamukhulupirira ndipo mumakondwera ndi chimwemwe chachikulu ndi chosaneneka. Motero mukulandira mphotho ya chikhulupiriro chanu, ndiyo chipulumutso cha moyo wanu.

Aliyense amene akakhulupirire nabatizidwa adzapulumuka, koma amene sakakhulupirira adzalangidwa.

A salvação presente e futura

A salvação é passada (justificação), presente (santificação) e futura (glorificação). Deus nos salva, nos guarda e nos conduz à vida eterna.

Pakuti chisomo cha Mulungu chimene chimapulumutsa chaonekera kwa anthu onse. Chisomo chimatiphunzitsa kukana moyo osalemekeza Mulungu komanso zilakolako za dziko lapansi. Ndipo chimatiphunzitsa kukhala moyo odziletsa, olungama ndi opembedza Mulungu nthawi ino,

Monga mwa malamulo titha kunena kuti, pafupifupi zinthu zonse zimayeretsedwa ndi magazi ndipo popanda kukhetsa magazi palibe kukhululukidwa machimo.

momwemonso Khristu anadzipereka nsembe kamodzi kokha kuchotsa machimo a anthu ambiri. Ndipo Iye adzaonekanso kachiwiri, osati kudzachotsa tchimo, koma kudzapereka chipulumutso kwa amene akumudikira.

Pakuti pamene tinali adani a Mulungu, tinayanjanitsidwa ndi Iye kudzera mu imfa ya Mwana wake. Nanga tidzapulumutsidwa bwanji kudzera mʼmoyo wake, titayanjanitsidwa naye?

Pakuti monga mwa Adamu onse amafa, chomwechonso mwa Khristu onse adzakhala ndi amoyo.

Nada é impossível para Deus

Aos homens é impossível, mas para Deus tudo é possível. Ele deseja que todos sejam salvos e cheguem ao conhecimento da verdade.

Yesu anawayangʼana ndipo anati, "Kwa munthu zimenezi nʼzosatheka, koma osati ndi Mulungu; zinthu zonse zimatheka ndi Mulungu."

Yesu anayankha kuti, "Zinthu zosatheka ndi anthu zimatheka ndi Mulungu."

Pajatu Mwana wa Munthu anabwera kudzafunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho."

Pakuti izi ndi zimene Ambuye anatilamula ife:

" Ine ndakuyika iwe ukhale kuwunika kwa anthu a mitundu ina,

kuti ukafikitse chipulumutso ku malekezero a dziko lapansi!’ "

Zipata Ziwiri ndi Njira Ziwiri

"Lowani pa chipata chopapatiza. Pakuti chipata cholowera kuchiwonongeko nʼchachikulu ndipo msewu wake ndi waukulunso. Ndipo anthu ambiri amalowera pamenepo. Koma chipata ndi chopapatiza ndi msewu ndi waungʼono umene utsogolera anthu ku moyo wosatha ndipo ndi owerengeka okha amene ayipeza njirayo.

Kodi simukudziwa kuti munthu woyipa sadzalowa mu ufumu wa Mulungu? Musanyengedwe: achigololo, kapena opembedza mafano, kapena achiwerewere, kapena amuna adama, kapena ogonana ndi amuna okhaokha; kapena akuba, kapena aumbombo, kapena oledzera, kapena achipongwe, kapena opeza ndalama mwachinyengo sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.

Yesu anati, "Pita, chikhulupiriro chako chakuchiritsa!" Nthawi yomweyo anapenya, nʼkumatsatira Yesu pa ulendowo.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Kutsata mayimbidwe a Yedutuni. Salimo la Davide.

Moyo wanga umapeza mpumulo mwa Mulungu yekha;

chipulumutso changa chimachokera kwa Iye.

Inu mumandipatsa chishango chachipambano,

ndipo dzanja lanu lamanja limandichirikiza;

mumawerama pansi kundikuza.

Munakulitsa njira yoyendamo ine,

kuti mapazi anga asaguluke.

Ngakhale mtengo wa mkuyu usachite maluwa,

ndipo mipesa ikhale yopanda mphesa.

Ngakhale mitengo ya olivi isabereke zipatso,

ndipo mʼminda musatuluke kanthu.

Ngakhale nkhosa

ndi ngʼombe zithe mʼkhola,

komabe ine ndidzakondwera mwa Yehova,

ndidzasangalala mwa Mulungu Mpulumutsi wanga.

Popeza kuti ndiwe wamtengowapatali wolemekezeka ndi wapamtima panga,

ndipo chifukwa ndimakukonda,

ndidzapereka anthu mʼmalo mwa iwe,

ndidzapereka mitundu ya anthu pofuna kuwombola moyo wako.

Seja o primeiro
Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-