A segunda vinda de Cristo
A segunda vinda de Cristo é a esperança suprema da Igreja. Jesus prometeu que voltará com poder e grande glória para julgar os vivos e os mortos e estabelecer seu Reino eterno.
A promessa do retorno
Jesus prometeu voltar. Os anjos declararam que Ele virá da mesma forma como ascendeu. A Igreja aguarda esse dia glorioso com expectativa.
Iwo anati, "Inu, anthu a ku Galileya, chifukwa chiyani mukuyima ndi kumayangʼana mʼmitambo? Yesu amene wachotsedwa pakati panu ndi kupita kumwamba, adzabweranso mʼnjira yomweyi mwamuona akupita kumwamba."
Yesu akukwera kumwamba, ophunzira ake anayangʼanitsitsa ndi chidwi mʼmitambo. Mwadzidzidzi anaona anthu awiri ovala zoyera atayimirira pambali pawo. Iwo anati, "Inu, anthu a ku Galileya, chifukwa chiyani mukuyima ndi kumayangʼana mʼmitambo? Yesu amene wachotsedwa pakati panu ndi kupita kumwamba, adzabweranso mʼnjira yomweyi mwamuona akupita kumwamba."
Yesu Atonthoza Ophunzira Ake
"Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu; khulupirirani Inenso. Mʼnyumba mwa Atate anga muli zipinda zambiri. Kukanakhala kuti mulibemo ndikanakuwuzani. Ine ndikupita kumeneko kukakukonzerani malo. Ndipo ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengani, kuti kumene kuli Ineko, inunso mukakhale komweko.
Iye amene akuchitira umboni pa zinthu izi akuti, "Inde, Ine ndikubwera posachedwa."
Ameni. Bwerani Ambuye Yesu.
Iye amene akuchitira umboni pa zinthu izi akuti, "Inde, Ine ndikubwera posachedwa."
Ameni. Bwerani Ambuye Yesu.
Mawu Otsiriza: Kuyitanidwa ndi Chenjezo
"Taonani, ndikubwera posachedwa! Ndikubwera ndi mphotho zanga kuti ndidzapereke kwa aliyense malinga ndi zimene anachita.
Os sinais dos tempos
Jesus descreveu os sinais que precederão sua volta: falsos profetas, guerras, fome, terremotos e tribulação. Devemos discernir os tempos sem nos alarmar.
Pamene Yesu anakhala pansi pa phiri la Olivi, ophunzira ake anabwera kwa Iye mwamseri nati, "Tiwuzeni, kodi izi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro cha kubwera kwanu ndi zizindikiro za kutha kwa dziko zidzakhala chiyani?"
Yesu anayankha kuti, "Onetsetsani kuti wina asakunyengeni. Pakuti ambiri adzabwera mʼdzina langa nadzati, ‘Ndine Khristu,’ ndipo adzanyenga ambiri. Mudzamva za nkhondo ndi mbiri za nkhondo, koma onetsetsani kuti musadzidzimuke nazo. Zotere ziyenera kuchitika, koma chimaliziro sichinafike.
"Pamenepo adzakuperekani kuti mukazunzidwe ndi kuphedwa, ndipo mitundu yonse idzakudani chifukwa cha Ine. Pa nthawi imeneyo ambiri adzasiya chikhulupiriro ndipo adzadana ndi kuperekana wina ndi mnzake, ndipo aneneri onama ambiri adzaoneka ndi kunyenga anthu ambiri.
Chifukwa cha kuchuluka kwa zoyipa, chikondi cha ambiri chidzazirala, koma wopirira kufikira chimaliziro adzapulumuka.
Ndipo uthenga wa ufumu udzalalikidwa ku dziko lonse lapansi ngati umboni kwa mitundu yonse, ndipo pomwepo chimaliziro chidzafika."
Popeza kudzakhala masautso aakulu, omwe safanana ndi ena ali onse chiyambireni cha dziko lapansi mpaka lero lino ndipo sadzafanananso ndi ena. Ngati masiku amenewo sakanafupikitsidwa, palibe mmodzi akanapulumuka, koma chifukwa cha osankhidwawo masiku amenewo adzafupikitsidwa.
Pa nthawi imeneyo ngati wina adzati kwa inu, ‘Onani, Khristu ali pano!’ Kapena, ‘Uyo ali ukoyo!’ Musakhulupirire. Chifukwa akhristu onama ndi aneneri onama adzaoneka ndipo adzachita zizindikiro zazikulu ndi zodabwitsa kuti akanyenge ngakhale osankhidwawo ngati kukanakhala kotheka kutero. Onani, ndakuwuzani izi nthawi isanafike.
Pa nthawi imeneyo ngati wina adzati kwa inu, ‘Onani, Khristu ali pano!’ Kapena, ‘Uyo ali ukoyo!’ Musakhulupirire. Chifukwa akhristu onama ndi aneneri onama adzaoneka ndipo adzachita zizindikiro zazikulu ndi zodabwitsa kuti akanyenge ngakhale osankhidwawo ngati kukanakhala kotheka kutero. Onani, ndakuwuzani izi nthawi isanafike.
"Ndiye ngati wina akuwuzani inu kuti, ‘Uyo ali ku chipululu,’ inu musapiteko; kapena akati, ‘Uyu ali kuno mʼchipinda chamʼkati,’ musakhulupirire.
Aneneri Owona ndi Onyenga
"Chenjerani nawo aneneri onyenga. Amabwera kwa inu atavala zikopa zankhosa, koma mʼkati mwawo ali mimbulu yolusa.
Mtundu udzawukira mtundu unzake, ndi ufumu kuwukira ufumu unzake. Kudzakhala zivomerezi mʼmalo osiyanasiyana, ndi njala. Izi ndi chiyambi chabe cha zowawa monga mayi pobereka.
"Muyenera kukhala tcheru. Mudzaperekedwa ku mabwalo oweruza ndi kukwapulidwa mwankhanza mʼmasunagoge. Mudzayima pamaso pa abwanamkubwa ndi mafumu monga mboni kwa iwo chifukwa cha Ine. Ndipo Uthenga Wabwino uyenera kuyamba walalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.
"Mʼbale adzapereka mʼbale kuti aphedwe, ndipo abambo adzapereka mwana wawo. Ana adzawukira makolo awo ndi kuwapereka kuti aphedwe. Anthu onse adzakudani chifukwa cha Ine, koma amene adzalimbika mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke.
Kudzakhala zivomerezi zazikulu, njala ndi miliri mʼmalo osiyanasiyana, ndi zinthu zoopsa ndi zizindikiro zamphamvu kuchokera kumwamba.
A vinda gloriosa
Cristo virá nas nuvens com poder e grande glória, enviará seus anjos e reunirá seus escolhidos dos quatro ventos.
"Akadzangotha mavuto a masiku amenewo,
" ‘dzuwa lidzadetsedwa,
ndipo mwezi sudzawala;
nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba,
ndipo mphamvu za mmwamba zidzagwedezeka.’
"Pa nthawi imeneyo chizindikiro cha Mwana wa Munthu chidzaoneka mlengalenga, ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzalira. Idzaona Mwana wa Munthu akubwera ndi mitambo, mphamvu ndi ulemerero waukulu. Ndipo adzatuma angelo ake, ndi kulira kwa lipenga kwakukulu, nadzasonkhanitsa osankhidwa ake kuchokera ku mphepo zinayi, ndi kuchokera kumathero a thambo kufika mbali ina.
"Tsopano kuchokera ku mtengo wamkuyu phunzirani ichi: Pamene uyamba kuphukira, masamba ake akatuluka, mumadziwa kuti dzinja layandikira. Momwemonso, pamene mudzaona zinthu zonsezi mudzadziwe kuti ali pafupi pa khomo penipeni.
Pakuti Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate ake ndi angelo ake ndipo pamenepo Iye adzapereka mphotho kwa munthu mofanana ndi zimene anachita.
"Padzakhala zizindikiro zodabwitsa pa dzuwa, mwezi ndi nyenyezi. Pa dziko lapansi, mitundu ya anthu idzakhala mʼmasautso ndipo idzathedwa nzeru pakumva mkokomo ndi mafunde a mʼnyanja. Anthu adzakomoka chifukwa cha mantha, akadzamva za zimene zikubwera pa dziko lapansi, pakuti zinthu zamlengalenga zidzagwedezeka. Nthawi imeneyo adzaona Mwana wa Munthu akubwera ndi mitambo, mphamvu ndi ulemerero waukulu. Zinthu izi zikadzayamba kuchitika, mudzayimirire ndi kutukula mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chayandikira."
Nthawi imeneyo adzaona Mwana wa Munthu akubwera ndi mitambo, mphamvu ndi ulemerero waukulu.
"Nthawi imeneyo anthu adzaona Mwana wa Munthu akubwera mʼmitambo ndi mphamvu yayikulu ndi ulemerero. Ndipo adzatuma angelo ake kukasonkhanitsa osankhidwiratu ake ku mphepo zinayi, kuyambira kumalekezero a dziko lapansi mpaka ku malekezero ake enanso.
Pakuti Ambuye mwini adzatsika kuchokera kumwamba, ndi mfuwu waulamuliro, ndi liwu la mngelo wamkulu, ndi kulira kwa lipenga la Mulungu, ndipo akufa amene ali mwa Yesu adzauka poyamba. Kenaka, ife amene tili ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa pamodzi ndi iwo mʼmitambo kukakumana ndi Ambuye mlengalenga. Tsono ife tidzakhala ndi Ambuye mpaka muyaya. Nʼchifukwa chake tsono muzilimbikitsana ndi mawu amenewa.
Vigilância e preparo
Ninguém sabe o dia nem a hora. Jesus nos ordena a vigiar, orar e estar prontos, pois Ele virá quando menos esperamos.
"Chifukwa chake yangʼanirani, popeza simudziwa tsiku lanji limene Ambuye anu adzabwera.
"Chifukwa chake yangʼanirani, popeza simudziwa tsiku lanji limene Ambuye anu adzabwera.
Inunso tsono muyenera kukhala okonzeka, chifukwa Mwana wa Munthu adzabwera pa nthawi imene inu simukumuyembekezera.
Za Kukhala Tcheru
"Samalani, kuti mitima yanu ingalemetsedwe ndi maphwando, kuledzera ndi kudera nkhawa za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingadzakupezeni modzidzimutsa ngati msampha. Pakuti lidzafika pa onse okhala pa dziko lonse lapansi. Khalani tcheru nthawi zonse ndi kupemphera kuti inu mudzathe kuthawa zonse zimene zili pafupi kuchitika, ndi kuti mudzathe kuyima pamaso pa Mwana wa Munthu."
Chimaliziro cha zinthu zonse chili pafupi. Choncho khalani maso ndi odziletsa kuti muthe kupemphera.
Mulungu mwini, Mulungu wamtendere, akuyeretseni kotheratu. Mzimu wanu wonse, moyo ndi thupi zisungidwe zopanda cholakwa mpaka kubwera kwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Choncho inu simusowa mphatso yauzimu iliyonse pamene mukudikira mofunitsitsa kuti Ambuye athu Yesu Khristu avumbulutsidwe. Adzakulimbikitsani mpaka kumapeto kuti mudzakhale wopanda mlandu pa tsiku lobwera Ambuye athu Yesu Khristu.
A esperança bendita
A aguardamos a bendita esperança e a manifestação da glória do nosso grande Deus e Salvador Jesus Cristo.
Pakuti chisomo cha Mulungu chimene chimapulumutsa chaonekera kwa anthu onse. Chisomo chimatiphunzitsa kukana moyo osalemekeza Mulungu komanso zilakolako za dziko lapansi. Ndipo chimatiphunzitsa kukhala moyo odziletsa, olungama ndi opembedza Mulungu nthawi ino, pamene tikudikira chiyembekezo chodala; kuonekera kwa ulemerero wa Mulungu wathu wamkulu ndi Mpulumutsi, Yesu Khristu, amene anadzipereka yekha chifukwa cha ife kutiwombola ku zoyipa zonse ndi kudziyeretsera yekha anthu amene ndi akeake, achangu pa ntchito yabwino.
Sindikukayika konse kuti Iye amene anayamba ntchito yabwino mwa inu adzayipitiriza ndi kuyimaliza mpaka pa tsiku la kubweranso kwa Khristu Yesu.
Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu amene mwasindikizidwa naye chizindikiro cha tsiku la kuwomboledwa.
momwemonso Khristu anadzipereka nsembe kamodzi kokha kuchotsa machimo a anthu ambiri. Ndipo Iye adzaonekanso kachiwiri, osati kudzachotsa tchimo, koma kudzapereka chipulumutso kwa amene akumudikira.
Tiziganizira mmene tingalimbikitsirane wina ndi mnzake pokondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tiyeni tisaleke kusonkhana kwathu pamodzi monga mmene ena amachitira, koma tizilimbikitsana makamaka poona kuti tsiku la Ambuye layandikira.
"Ine ndine Alefa ndi Omega," akutero Ambuye Mulungu Wamphamvuzonseyo "amene muli, amene munalipo, ndi amene mudzakhalapo."
Ine ndikubwera msanga. Gwiritsitsa chimene uli nacho kuti wina angakulande chipewa chako chaufumu.
Koma abale okondedwa, musayiwale chinthu chimodzi ichi: Kuti pamaso pa Ambuye tsiku limodzi lili ngati zaka 1,000, ndipo zaka 1,000 zili ngati tsiku limodzi!
Ana a Mulungu
Tsopano ana okondedwa, khalani mwa Yesu, kuti pamene adzaonekera, ife tidzakhale otsimikizika mu mtima ndi wopanda manyazi pamaso pake akamadzabwera.