O Senhor é o meu pastor
O Salmo 23 é a expressão máxima da confiança em Deus como Pastor. Jesus se declarou o Bom Pastor que conhece suas ovelhas, cuida delas e dá a própria vida por elas.
O Senhor é o meu Pastor
Davi declarou com confiança que o Senhor é seu pastor e nada lhe faltará. Ele nos guia, nos restaura e nos conduz em caminhos de justiça.
Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
Amandigoneka pa msipu wobiriwira,
amanditsogolera ku madzi akumwa abwino,
amatsitsimutsa moyo wanga.
Amanditsogolera mʼnjira zachilungamo
chifukwa cha dzina lake.
Pulumutsani anthu anu ndipo mudalitse cholowa chanu;
mukhale mʼbusa wawo ndipo muwakweze kwamuyaya.
O Bom Pastor
Jesus é o Bom Pastor que conhece suas ovelhas pelo nome. Ele dá a vida por elas, as protege e nenhuma pode ser arrebatada de sua mão.
"Ine ndine Mʼbusa wabwino. Mʼbusa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa zake.
"Ine ndine mʼbusa wabwino. Ine ndimazidziwa nkhosa zanga ndipo nkhosa zangazo zimandidziwa, monga momwe Atate amandidziwa Ine, ndiponso Ine kudziwira Atatewo. Ndimapereka moyo wanga chifukwa cha nkhosa. Ine ndili ndi nkhosa zina zimene sizili za gulu ili. Ine ndiyenera kuzibweretsanso. Izonso zidzamvera mawu anga, ndipo zidzakhala gulu limodzi ndi mʼbusa mmodzi.
Munthu amene amalowera pa khomo ndi mʼbusa wankhosazo. Mlonda amamutsekulira khomo, ndipo nkhosa zimamvera mawu ake. Iye amaziyitana mayina nkhosa zakezo, nazitulutsa. Akazitulutsa nkhosa zake zonse, iye amazitsogolera, ndipo nkhosa zakezo zimamutsata chifukwa zimadziwa mawu ake.
Pakuti munali monga nkhosa zosochera, koma tsopano mwabwerera kwa mʼbusa ndi woyangʼanira miyoyo yanu.
Ndipo Mʼbusa wamkulu akadzaonekera, mudzalandira chipewa cha ulemerero chosafota.
O cuidado pastoral de Deus
Como pastor terno e forte, Deus carrega os cordeiros nos braços e guia com cuidado as ovelhas que amamentam.
Taonani, Ambuye Yehova akubwera mwamphamvu,
ndipo dzanja lake likulamulira,
taonani akubwera ndi mphotho yake
watsogoza zofunkha zako za ku nkhondo.
Iye adzasamalira nkhosa zake ngati mʼbusa:
Iye adzasonkhanitsa ana ankhosa aakazi mʼmanja mwake
ndipo Iye akuwanyamula pachifuwa chake
ndi kutsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.