Publicidade

Sonhos

Por Bíblia Online

Sonhos aparecem em toda a Bíblia como meio de revelação divina. Deus falou através de sonhos a patriarcas, profetas e servos, mas também alertou contra falsos sonhadores.

Sonhos como revelação divina

Deus usou sonhos para comunicar sua vontade a homens e mulheres ao longo da história bíblica, revelando caminhos e mistérios.

Mulungu anati, "Mverani mawu anga:

"Pakakhala mneneri wa Yehova pakati panu,

ndimadzionetsera kwa iyeyo mʼmasomphenya,

ndimayankhula naye mʼmaloto.

Tsiku la Yehova

"Ndipo patapita nthawi,

ndidzakhuthulira Mzimu wanga pa anthu onse.

Ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzanenera,

nkhalamba zanu zidzalota maloto,

anyamata anu adzaona masomphenya.

Uthenga wa Petro

Koma Petro anayimirira pamodzi ndi atumwi khumi ndi mmodziwo ndipo anakweza mawu ake nayankhula kwa gulu la anthu nati: "Ayuda anzanga, ndi nonse amene muli mu Yerusalemu, mvetsetsani izi ndipo tcherani khutu ku zimene ndikunena. Kunena zoona, anthu awa sanaledzere ayi, monga momwe mukuganizira, pakuti ino ndi 9 koloko mmawa! Koma izi ndi zimene ananena Mneneri Yoweli kuti:

" Mulungu akuti, mʼmasiku otsiriza

ndidzakhuthulira Mzimu wanga pa anthu onse.

Ana anu aamuna ndi aakazi adzanenera,

anyamata anu adzaona masomphenya,

nkhalamba zanu zidzalota maloto.

Kwa anyamata anayiwa Mulungu anapereka chidziwitso ndi kuzindikira bwino mitundu yonse ya zolembedwa ndi za maphunziro. Ndipo Danieli ankatanthauzira masomphenya ndi maloto a mitundu yonse.

Mfumu inafunsa Danieli (wotchedwanso Belitesezara) kuti, "Kodi ukhoza kundiwuza zomwe ine ndinaona mʼmaloto anga ndi tanthauzo lake?"

Danieli anayankha kuti, "Palibe munthu wanzeru, wowombeza, wamatsenga kapena wamawula amene akhoza kufotokozera mfumu chinsinsi chimene mwafuna kudziwa, koma kuli Mulungu kumwamba amene amawulula zinsinsi. Iye waonetsera mfumu Nebukadinezara zimene zidzachitika mʼmasiku akutsogolo. Maloto ndi masomphenya anu amene munawaona mukugona pa bedi lanu ndi awa:

Sonhos na história da Bíblia

De José no Egito a José pai de Jesus, Deus guiou a história da salvação através de sonhos, protegendo e dirigindo seu povo.

Iwo anayankha, "Tonse awiri talota maloto, koma palibe wotitanthauzira malotowo."

Pamenepo Yosefe anawawuza kuti, "Ndi Mulungu yekha amene amapereka matanthauzo a maloto. Uzeni ine maloto anu."

Farao anati kwa Yosefe, "Ndinalota maloto ndipo palibe amene watha kunditanthauzira. Tsono ndawuzidwa kuti iwe ukamva loto umadziwanso kulimasulira."

Yosefe anamuyankha Farao kuti, "Sindingathe koma Mulungu apereka yankho limene Farao akufuna."

Koma akuganiza zimenezi, taonani, mngelo wa Ambuye anamuonekera mʼmaloto nati, "Yosefe mwana wa Davide, usaope kumutenga Mariya kukhala mkazi wako, chifukwa mwana akuyembekezerayo ndi wochokera kwa Mzimu Woyera. Ndipo adzabala mwana wamwamuna, udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo."

Pamene Pilato anakhala pa mpando woweruza, mkazi wake anamutumizira uthenga uwu, "Musachite kanthu ndi munthuyo, ndi wosalakwa pakuti ndavutika kwambiri lero mʼmaloto chifukwa cha munthuyo."

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

Yehova atabwezera akapolo ku Ziyoni,

tinali ngati amene akulota.

Sabedoria sobre sonhos

A Bíblia ensina discernimento: nem todo sonho vem de Deus. Devemos entregar nossos planos ao Senhor e confiar na direção dele.

Pereka ntchito zako zonse mʼmanja mwa Yehova,

ndipo zolinga zako zidzachitikadi.

Munthu amakonzekera zambiri mu mtima mwake,

koma cholinga cha Yehova ndiye chidzachitike.

Kupembedza Milungu Ina

Ngati mneneri kapena wina aliyense amene amanena zamʼtsogolo mwa maloto atuluka pakati panu, nalengeza za chizindikiro chozizwitsa kapena chodabwitsa, chinthu nʼkuchitikadi, tsono iyeyo nʼkunena kuti, "Tiyeni titsatire milungu ina, tiyeni tiyipembedze," (kunena milungu imene simunayidziwe), musamumvere mneneriyo kapena wolotayo. Yehova Mulungu wanu afuna akuyeseni kuti aone ngati mumamukonda ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. Muyenera kutsatira Yehova Mulungu wanu, ndipo ndi Iyeyo amene muyenera kumuopa. Muzisunga malamulo ake ndi kumamumvera, muzimutumikira ndipo kumukangamira Iyeyo.

"Ndamva zimene aneneri akuyankhula. Iwo amalosera zabodza mʼdzina langa nʼkumati, Ndalota! Ndalota!Kodi zabodzazi zidzakhalabe mʼmitima ya aneneriwa mpaka liti? Iwotu amalosera zonyenga za mʼmitima yawo.

Yehova akuti, "Ndithudi, Ine ndikudana ndi aneneri a maloto abodzawa. Iwo amafotokoza malotowo nʼkumasocheretsa anthu anga ndi bodza lawo losachita nalo manyazilo, chonsecho Ine sindinawatume kapena kuwalamula. Iwo sathandiza anthuwa ndi pangʼono pomwe," akutero Yehova.

Kuchuluka kwa mavuto mu mtima kumabweretsa maloto oyipa,

ndipo kuchuluka kwa mawu kumadzetsa uchitsiru.

Maloto ochuluka ndi mawu ochuluka ndi zinthu zopandapake. Kotero lemekeza Mulungu.

Seja o primeiro
Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-