Superação
Superar desafios, dificuldades e tentações faz parte da caminhada cristã. A Bíblia nos garante que, em Cristo, somos mais que vencedores em todas as circunstâncias.
Vitória em Cristo
Jesus já venceu o mundo. Nele temos coragem, paz e a certeza de que nenhuma adversidade poderá nos derrotar definitivamente.
"Ine ndakuwuzani izi kuti mwa Ine mukhale nawo mtendere. Mʼdziko lapansi mudzakhala nawo mavuto. Koma limbikani mtima! Ine ndaligonjetsa dziko lapansi."
"Ine ndakuwuzani izi kuti mwa Ine mukhale nawo mtendere. Mʼdziko lapansi mudzakhala nawo mavuto. Koma limbikani mtima! Ine ndaligonjetsa dziko lapansi."
Ayi, mu zonsezi ife ndife oposa agonjetsi mwa Iye amene anatikonda.
Koma tiyamike Mulungu amene amatipambanitsa mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Koma tiyamike Mulungu amene amatipambanitsa mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
chifukwa aliyense amene ndi mwana wa Mulungu amagonjetsa dziko lapansi. Chikhulupiriro chathu ndicho timagonjetsera dziko lapansi.
Pakuti kukonda Mulungu ndiye kusunga malamulo ake. Ndipo malamulo ake siwolemetsa, chifukwa aliyense amene ndi mwana wa Mulungu amagonjetsa dziko lapansi. Chikhulupiriro chathu ndicho timagonjetsera dziko lapansi. Ndani amagonjetsa dziko lapansi? Yekhayo amene amakhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu.
Ndani amagonjetsa dziko lapansi? Yekhayo amene amakhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu.
Abale athuwo anamugonjetsa
ndi magazi a Mwana Wankhosa
ndiponso mawu a umboni wawo.
Iwo anadzipereka kwathunthu,
moti sanakonde miyoyo yawo.
Superando o mal com o bem
O cristão vence o mal não com violência, mas com o bem. O amor, a fé e a perseverança são as armas da superação.
Musagonjetsedwe ndi choyipa, koma gonjetsani choyipa pochita chabwino.
Musagonjetsedwe ndi choyipa, koma gonjetsani choyipa pochita chabwino.
Kuwunika kunawala mu mdima, koma mdimawo sunakuzindikire.
Koma tithokoze Mulungu amene amatitsogolera nthawi zonse monga ogwidwa ku nkhondo a Khristu pa chipambano chake. Tsono amatigwiritsa ntchito yofalitsa ponseponse nzeru zodziwira Khristu ngati fungo labwino.
Aliyense amene mumukhululukire, inenso ndimukhululukira. Ndipo ndikakhululukira, ngati pali kanthu koti ndikhululukire, ndiye kuti ndakhululuka chifukwa cha inu pamaso pa Khristu, kupewa kuti Satana angapezere mpata pa ife, pajatu timadziwa machenjerero ake.
Amene adzapambana, ndidzamupatsa ufulu wokhala nane pamodzi pa mpando wanga waufumu monga mmene Ine ndinapambana ndi kukhala pansi ndi Atate anga pa mpando wawo waufumu.
Amene adzapambana, ndidzamupatsa ufulu wokhala nane pamodzi pa mpando wanga waufumu monga mmene Ine ndinapambana ndi kukhala pansi ndi Atate anga pa mpando wawo waufumu.
Amene adzapambane adzavala zoyera ngati ena aja. Sindidzafafaniza dzina lake mʼbuku lamoyo, koma ndidzamuchitira umboni pamaso pa Atate anga ndi angelo ake.
Força e coragem divina
Deus é nosso escudo e fortaleza. Quando o medo tenta nos paralisar, a presença do Senhor nos fortalece e nos encoraja a prosseguir.
Yehova ndiye kuwunika kwanga ndi chipulumutso changa;
ndidzaopa yani?
Yehova ndi linga la moyo wanga;
ndidzachita mantha ndi yani?
Koma Inu Yehova, ndinu chishango chonditeteza,
Inu mwandiveka ulemerero ndipo mwanditukula.
Sindidalira uta wanga,
lupanga langa silindibweretsera chigonjetso;
koma Inu mumatigonjetsera adani athu,
mumachititsa manyazi amene amadana nafe.
Timanyadira mwa Mulungu wathu tsiku lonse,
ndipo tidzatamanda dzina lanu kwamuyaya.
Inu Yehova, tipulumutseni;
Yehova, tipambanitseni.
Wodala amene akubwera mʼdzina la Yehova.
Tikukudalitsani kuchokera ku nyumba ya Yehova.
Taonani, Yehova Mulungu wanu wakupatsani dzikoli. Pitani ndi kulitenga monga Yehova, Mulungu wa makolo anu anakuwuzirani. Musaope kapenanso kugwa mphwayi."
pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye amene apite nanu kukakumenyerani nkhondo ndi kugonjetsa adani anu."
Inu mudzamupatsa munthu
wa mtima wokhazikika
mtendere weniweni.
Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu.
Inu ana okondedwa, ndinu ochokera kwa Mulungu ndipo mwawagonjetsa aneneri onyengawa, chifukwa Iye amene ali mwa inu ndi wamkulu kuposa amene ali mʼdziko lapansi.
Inu ana okondedwa, ndinu ochokera kwa Mulungu ndipo mwawagonjetsa aneneri onyengawa, chifukwa Iye amene ali mwa inu ndi wamkulu kuposa amene ali mʼdziko lapansi.
Resistindo a tentação
A armadura de Deus nos protege contra as investidas do mal. Resistir ao diabo, vigiar e orar são essenciais para a superação espiritual.
Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye ndi mwa mphamvu zake zazikulu. Valani zida zonse za Mulungu kuti muthe kuyima ndi kukana machenjerero a Satana. Pakuti sitikulimbana ndi thupi ndi magazi, koma tikulimbana ndi maufumu, maulamuliro, mphamvu za dziko la mdima, ndi mphamvu zoyipa kwambiri zauzimu zamlengalenga. Choncho valani zida zonse za Mulungu, kuti pamene tsiku loyipa kwambiri lifika, mudzathe kuyima chilili, ndipo mutatha kuchita zonse, mudzayimabe mwamphamvu. Tsono imani mwamphamvu, mutamangira choonadi ngati lamba mʼchiwuno mwanu, mutavala chilungamo ngati chitsulo chotchinjiriza pa chifuwa. Valani Uthenga Wabwino wamtendere ku mapazi anu ngati nsapato. Kuwonjezera pa zonsezi, nyamulani chishango cha chikhulupiriro, ndipo ndi chimenechi mudzatha kuzimitsa mivi yonse yoyaka moto ya oyipayo. Valani chipewa cha chipulumutso ndi kutenga lupanga la mzimu, limene ndi Mawu a Mulungu.
Inu munaphunzitsidwa molingana ndi moyo wanu wakale, kuchotsa umunthu wakale, umene ukupitirira kuwonongeka ndi zilakolako zachinyengo; kuti mukonzedwe mwatsopano mʼmitima mwanu; ndi kuti muvale umunthu watsopano, wolengedwa kuti ufanane ndi Mulungu mu chilungamo chenicheni ndi chiyero.
Kwiyani koma musachimwe. Dzuwa lisalowe mukanali chikwiyire. Musamupatse mpata Satana.
Dziperekeni nokha kwa Mulungu. Mukaneni Mdierekezi ndipo adzakuthawani. Sendezani kufupi ndi Mulungu ndipo Iye adzasendeza kwa inu. Sambani mʼmanja mwanu, inu anthu ochimwa. Yeretsani mitima yanu, inu anthu okayikira.
Dzichepetseni pamaso pa Ambuye ndipo Iye adzakukwezani.
Wodala ndi munthu amene amapirira mʼmayesero, chifukwa akapambana adzalandira chipewa cha ulemerero chimene Mulungu analonjeza anthu amene amamukonda.
Munthu akayesedwa asanene kuti, "Mulungu akundiyesa." Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi choyipa kapena Iyeyo kuyesa munthu aliyense. Koma munthu aliyense amayesedwa akakokedwa ndi zilakolako zake zoyipa ndi kukopedwa nazo. Pamenepo, chilakolako chikakula chimabala tchimo; ndipo tchimo likakhwima limabereka imfa.
Palibe mayesero amene mwakumana nawo oposa amene anthu ena onse anakumana nawo. Mulungu ngokhulupirika; sadzalola kuti inu muyesedwe koposa muyeso umene mutha kupirira. Koma pamene mwayesedwa, Iyenso adzakupatsani njira yopambanira mayeserowo.
Menya nkhondo yabwino yachikhulupiriro. Gwiritsitsa moyo wosatha umene anakuyitanira pamene unavomereza bwino lomwe pamaso pa mboni zambiri.
Anthu amene amafuna kulemera amagwa mʼmayesero ndi mu msampha ndi mʼzilakolako zambiri zopusa ndi zoopsa zimene zimagwetsera anthu mʼchitayiko ndi mʼchiwonongeko.
Perseverança até o fim
A corrida da fé exige perseverança. Devemos lançar fora todo peso e olhar para Jesus, o autor e consumador da nossa fé.
Tsono popeza ifenso tazunguliridwa ndi gulu lalikulu la mboni, tiyeni titaye chilichonse chimene chimatitchinga, makamaka tchimo limene limatikola mosavuta, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.
Muzilingalira za Iye amene anapirira udani waukulu chotere wochokera kwa anthu ochimwa, kuti musafowoke ndi kutaya mtima.
Popeza Iye mwini anamva zowawa pamene anayesedwa, Iyeyo angathe kuthandiza amene akuyesedwanso.
Khalani odziretsa ndi atcheru. Mdani wanu mdierekezi amayendayenda monga mkango wobangula kufunafuna wina kuti amumeze. Mukaneni iye, ndipo mukhazikike mʼchikhulupiriro, chifukwa mukudziwa kuti abale anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso akumva zowawa zomwezi.
Ndipo Mulungu wachisomo chonse, amene anakuyitanani ku ulemerero wake wamuyaya mwa Khristu, mutamva zowawa pa kanthawi, adzakukonzaninso ndi kukulimbitsani pa maziko olimba.
Khalani odziretsa ndi atcheru. Mdani wanu mdierekezi amayendayenda monga mkango wobangula kufunafuna wina kuti amumeze.
Ndani amene adzatilekanitsa ife ndi chikondi cha Khristu? Kodi ndi masautso, kapena zowawa, kapena mazunzo, kapena njala, kapena umaliseche, kapena choopsa, kapena lupanga?
Ndipo ife tikudziwa kuti zinthu zonse zimathandizana kuwachitira ubwino amene amakonda Mulungu, amene anayitanidwa monga mwa cholinga chake.
Ambuye adzandilanditsa ku chilichonse chofuna kundichita choyipa ndipo adzandisamalira bwino mpaka kundilowetsa chonse mu ufumu wake wakumwamba. Kwa Iye kukhale ulemerero mpaka muyaya.
Koma Ambuye ndi wokhulupirika, ndipo adzakulimbikitsani ndi kukutetezani kwa woyipayo.
Descanso e renovação
Jesus convida os cansados e sobrecarregados a descansar nele. Sua graça é suficiente para nos renovar em meio às tribulações.
"Idzani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo.
Mtima wanu usakonde ndalama koma mukhutitsidwe ndi zimene muli nazo, chifukwa Mulungu anati,
"Sadzakusiyani,
kapena kukutayani konse."
Pakuti palibe chinthu chosatheka ndi Mulungu."
Iye anafunsa kuti, Nʼchifukwa chiyani mukugona? "Dzukani ndipo pempherani kuti inu musagwe mʼmayesero."
Atafika pamalopo, Iye anawawuza kuti, "Pempherani kuti musagwe mʼmayesero."
Ine ndakupatsani ulamuliro woponda njoka ndi zinkhanira, ndi kugonjetsa mphamvu zonse za mdani; palibe chimene chidzakupwetekani.
Khalani tcheru ndi kupemphera kuti musalowe mʼmayesero. Mzimu ukufuna, koma thupi ndi lofowoka."
Sangalala kwambiri, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni!
Fuwula, mwana wamkazi wa Yerusalemu!
Taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe,
yolungama ndi yogonjetsa adani,
yodzichepetsa ndi yokwera pa bulu,
pa mwana wamphongo wa bulu.
Iye amene amachimwa ndi wa Satana, chifukwa mdierekezi wakhala akuchimwa kuyambira pa chiyambi. Mwana wa Mulungu anaonekera kuti awononge ntchito za mdierekezi.
Inu ana okondedwa, ndikukulemberani
popeza kuti machimo anu akhululukidwa chifukwa cha dzina la Yesu.
Inu abambo, ndikukulemberani
popeza kuti munamudziwa Iye amene analipo kuyambira pachiyambi.
Inu anyamata, ndikukulemberani
popeza kuti munagonjetsa woyipayo.
Ana okondedwa, ndikukulemberani
chifukwa mumawadziwa Atate.
Abambo, ndikukulemberani
chifukwa munamudziwa Iye amene analipo kuyambira pachiyambi.
Inu anyamata, ndikukulemberani
chifukwa ndinu amphamvu.
Mawu a Mulungu amakhala mwa inu
ndipo mumamugonjetsa woyipayo.
Musamakonde dziko lapansi kapena chilichonse cha dziko lapansi. Ngati munthu wina aliyense akonda dziko lapansi, mwa iyeyo mulibe chikondi chokonda Atate.
Kodi simukudziwa kuti matupi anuwo ndi ziwalo za Khristu mwini? Kodi tsono ndingatenge ziwalo za Khristu nʼkuzisandutsa ziwalo za mkazi wadama? Zosatheka! Kodi simukudziwa kuti amene amadzipereka kwa mkazi wadama, iyeyo ndi mkaziyo amasanduka thupi limodzi? Paja kunalembedwa kuti, "Awiriwo adzakhala thupi limodzi." Koma amene amadzipereka kwa Ambuye, iyeyo ndi Ambuye amakhala mzimu umodzi.
Thawani dama. Machimo onse amene munthu amachita amakhala kunja kwa thupi lake, koma amene amachita machimo okhudza chigololo, amachimwira thupi lake lomwe. Kodi simukudziwa kuti thupi lanu ndi Nyumba ya Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene mwalandira kuchokera kwa Mulungu? Inu simuli panokha ayi. Ndinu ochita kugulidwa. Nʼchifukwa chake lemekezani Mulungu mʼthupi lanu.
Choncho ine ndikuti, mulole kuti Mzimu akutsogolereni ndipo simudzachita zofuna za thupi lanu la uchimo. Pakuti thupi lanu la uchimo limalakalaka zimene ndi zotsutsana ndi Mzimu, ndi Mzimu zimene ndi zotsutsana ndi thupi lanu la uchimo. Ziwirizi zimadana, kotero kuti simungachite zimene mukufuna.