Sobre ter filhos
Filhos são uma dádiva do Senhor, uma herança que Deus confia aos pais. A Bíblia celebra a maternidade e a paternidade como vocações sagradas e fontes de bênção.
Filhos: herança do Senhor
A Escritura declara que os filhos são bênção de Deus. Cada criança é um presente precioso confiado aos pais para ser cuidado com amor.
Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova,
ana ndi mphotho yochokera kwa Iye.
Ana a pa unyamata ali ngati mivi mʼmanja
mwa munthu wankhondo.
Wodala munthu
amene motengera mivi mwake mwadzaza.
Iwo sadzachititsidwa manyazi
pamene alimbana ndi adani awo pa zipata.
Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka
mʼkati mwa nyumba yako;
ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya olivi
kuzungulira tebulo lako.
Amakhazikitsa mayi wosabereka mʼnyumba yake
monga mayi wa ana wosangalala.
Tamandani Yehova.
Mulungu anawadalitsa nati kwa iwo, "Muberekane, muchulukane, mudzaze dziko lapansi ndipo muligonjetse. Mulamulire nsomba zamʼnyanja, mbalame zamlengalenga ndi cholengedwa chamoyo chilichonse chimene chimayenda mokwawa pa dziko lapansi."
Instruir nos caminhos de Deus
A Bíblia orienta os pais a instruir seus filhos nos caminhos do Senhor desde cedo, com dedicação, disciplina e exemplo.
Mwana muzimuphunzitsa njira yake,
ndipo akadzakalamba sadzachokamo.
Sungani mawu amenewa mu mtima mwanu ndi mʼmaganizo mwanu, muwamangirire pa mikono yanu ndipo muwayike pamphumi panu. Mawuwa muziphunzitsa ana anu, muzikamba za iwo pamene mukhala pansi mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mugona ndi pamene mukudzuka.
Inu abambo, musakwiyitse ana anu, kuti angataye mtima.
Umulange mwana wako ndipo adzakupatsa mtendere
ndi kusangalatsa mtima wako.
Cada vida é preciosa
Deus conhece e forma cada criança no ventre. Antes de nascer, Ele já nos separou e preparou um propósito para cada vida.
"Ndisanakuwumbe mʼmimba mwa amayi ako ndinali nditakudziwa kale,
iwe usanabadwe ndinali nditakupatula kale;
ndinakuyika kuti ukhale mneneri kwa anthu a mitundu yonse."
Pakuti Inu munalenga za mʼkati mwanga;
munandiwumba pamodzi mʼmimba mwa amayi anga.
Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa;
ntchito zanu ndi zodabwitsa,
zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe.
Mapangidwe anga sanabisike pamaso panu
pamene ndimapangidwa mʼmalo achinsinsi,
pamene ndinkawumbidwa mwaluso mʼmimba ya amayi anga.
Kuchokera mʼkamwa mwa ana ndi makanda,
Inu mwakhazikitsa mphamvu
chifukwa cha adani anu,
kukhazikitsa bata adani ndi anthu obwezera zoyipa.
Yesu anati, "Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse pakuti ufumu wakumwamba ndi wa iwo onga anawa."