Publicidade

Tristeza

Por Bíblia Online

A tristeza faz parte da experiência humana, mas a Bíblia nos assegura que Deus está perto dos que sofrem. Ele enxuga as lágrimas e transforma a dor em esperança.

Deus consola os aflitos

O Senhor está perto dos quebrantados de coração. Mesmo no vale mais escuro, sua presença é refúgio e consolo para a alma que chora.

Olungama amafuwula, ndipo Yehova amawamva;

Iye amawalanditsa ku mavuto awo onse.

Yehova ali pafupi kwa osweka mtima

ndipo amapulumutsa iwo amene asweka mu mzimu.

Yehova amatsekula maso anthu osaona,

Yehova amadzutsa onse amene awerama pansi,

Yehova amakonda anthu olungama.

Zokhumba zanga zonse zili poonekera pamaso panu Ambuye,

kusisima kwanga sikunabisike kwa Inu.

Odala ndi amene ali achisoni,

chifukwa adzatonthozedwa.

"Bwerera, kamuwuze Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga kuti, Yehova Mulungu wa Davide kholo lako akuti: Ndamva pemphero lako ndipo misozi yako ndayiona ndipo ndidzakuchiritsa. Tsiku lachitatu kuchokera lero udzapita ku Nyumba ya Yehova.

A alegria virá

A dor tem prazo de validade. A manhã de alegria sempre vem depois da noite de choro. Deus promete transformar o luto em dança.

Pakuti mkwiyo wake umakhala kwa kanthawi

koma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse;

utha kuchezera kulira usiku wonse,

koma chimwemwe chimabwera mmawa.

Ndipo ndinamva mawu ofuwula kuchokera ku Mpando Waufumu kuti, "Taonani! Malo wokhalapo Mulungu ali pakati pa anthu, ndipo Iye adzakhala ndi anthuwo. Iwo adzakhala anthu ake ndipo Mulungu mwini adzakhala nawo nakhala Mulungu wawo. Mulungu adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo. Sikudzakhalanso imfa kapena kukhuza maliro kapena kulira kapena ululu popeza zakale zapita.’ "

Iwowa sadzamvanso njala,

sadzamvanso ludzu,

dzuwa kapena kutentha kulikonse

sikudzawawotcha.

Pakuti Mwana Wankhosa amene ali pakati pa mpando waufumu

adzakhala mʼbusa wawo.

Iye adzawatsogolera ku akasupe a madzi amoyo.

Ndipo Mulungu adzawapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo.’ "

Amatiyesa achisoni, koma ndife achimwemwe nthawi zonse, aumphawi, koma olemeretsa ambiri; wopanda kanthu, koma tili ndi zonse.

Entregando a dor a Deus

Podemos lançar sobre o Senhor toda nossa ansiedade e tristeza, porque Ele cuida de nós com ternura e não nos abandona.

Tayani pa Iye nkhawa zanu zonse chifukwa ndiye amakusamalani.

Yehova mwini ndiye akukutsogolerani ndipo adzakhala nanu. Sadzakusiyani kapena kukutayani. Usachite mantha ndiponso usataye mtima."

Kondwani pamodzi ndi amene akukondwa ndipo lirani ndi amene akulira.

O choro e o arrependimento

Há tristezas que produzem arrependimento e conduzem à vida. O choro diante de Deus é acolhido e transformado em bênção.

Ngʼambani Mtima Wanu

"Ngakhale tsopano,

bwererani kwa Ine ndi mtima wanu wonse

posala zakudya ndi kukhetsa misozi," akutero Yehova.

Mpesa wauma

ndipo mtengo wamkuyu wafota;

makangadza, kanjedza ndi mitengo ya apulosi,

mitengo yonse ya mʼmunda yauma.

Ndithudi chimwemwe cha anthu

chatheratu.

Atamva zimenezi, Yobu anayimirira nangʼamba mkanjo wake, ndi kumeta tsitsi lake. Kenaka anadzigwetsa pansi napembedza Mulungu, nati,

"Ndinatuluka maliseche mʼmimba mwa amayi anga,

namonso mʼmanda ndidzalowa wamaliseche.

Yehova ndiye anapereka ndipo Yehova watenga;

litamandike dzina la Yehova."

Miyambo ya Solomoni

Miyambo ya Solomoni:

Mwana wanzeru amakondweretsa abambo ake,

koma mwana wopusa amamvetsa amayi ake chisoni.

Pakuti nzeru zochuluka zimabweretsa chisoni chochulukanso:

chidziwitso chochuluka, zowawa zochulukanso.

Choncho uchotse zokusautsa mu mtima mwako,

upewe zokupweteka mʼthupi mwako,

pakuti unyamata ndi ubwana ndi zopandapake.

Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu amene mwasindikizidwa naye chizindikiro cha tsiku la kuwomboledwa.

Seja o primeiro
Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-