Vaso
A metáfora do vaso é uma das mais belas da Bíblia. Assim como o oleiro molda o barro, Deus nos forma segundo seus propósitos, fazendo de nós vasos úteis para sua glória.
Nas mãos do oleiro
Deus é o Oleiro e nós somos o barro. Ele tem autoridade e sabedoria para nos moldar conforme sua vontade perfeita, e não devemos questionar sua obra.
Komabe, Inu Yehova ndinu Atate athu.
Ife ndife chowumba, Inu ndinu wowumba;
ife tonse ndi ntchito ya manja anu.
Yehova anawuza Yeremiya kuti, "Pita ku nyumba ya munthu wowumba mbiya, ndipo kumeneko ndikakuwuza mawu anga." Choncho ndinatsikira ku nyumba ya wowumba mbiya, ndipo ndinamuona akuwumba mbiya pa mkombero. Tsono amati ngati mbiya imene waumba ikhala yosawumbika bwino ankayiphwanya nʼkuwumbanso ina monga mmene afunira ndi dothi lake lomwe lija.
Kenaka Yehova anandiwuza kuti, "Inu Aisraeli, kodi Ine sindingathe kuchita nanu monga amachitira wowumba mbiya?" akutero Yehova. "Inu muli mʼmanja mwanga ngati mtapo mʼmanja mwa wowumba mbiya.
Koma ndiwe yani, munthu wamba, woti nʼkutsutsana ndi Mulungu? "Kodi chimene chinawumbidwa nʼkufunsa amene anachiwumba kuti, ‘Kodi unandiwumbiranji motere?’ " Kodi wowumba alibe ufulu wowumba kuchokera ku dothi lomwelo mbiya yamtengowapatali ndi ina yamtengo wotsika?
"Tsoka kwa wokangana ndi mlengi wake,
ngakhale kuti ali ngati phale chabe pakati pa mapale anzake.
Kodi dongo lingafunse munthu wowumba kuti,
‘Kodi ukuwumba chiyani?’
Kodi ntchito yako inganene kuti,
‘Ulibe luso?’
Inu mumazondotsa zinthu
ngati kuti dothi lasanduka wowumba mbiya.
Kodi chinthu chopangidwa chingawuze wochipanga kuti
"Sunandipange ndi iwe?"
Kapena mʼphika kunena kwa amene anawuwumba kuti,
"Iwe sudziwa chilichonse?"
Vasos para honra
O cristão é chamado a ser um vaso de honra, purificado e preparado para toda boa obra. Nosso valor está em quem nos formou e no que carregamos.
Mʼnyumba yayikulu simukhala ziwiya zagolide ndi zasiliva zokha, koma mumakhalanso zamtengo ndi zadothi. Zina zimakhala za ntchito yapamwamba, zina za ntchito wamba. Munthu akadziyeretsa nʼkusiya ntchito za wambazi, adzakhala chiwiya cha ntchito yapamwamba, woyeretsedwa, ndi waphindu kwa Ambuye wake, wokonzeka kugwira ntchito iliyonse yabwino.
Koma tili ndi chuma ichi mʼmbiya zadothi, kusonyeza kuti mphamvu yoposayi, imachokera kwa Mulungu osati kwa ife.
Haa! Ana a Ziyoni amtengowapatali
amene kale anali ngati golide,
tsopano ali ngati miphika ya dothi,
ntchito ya owumba mbiya!
Moldados pela graça
Mesmo quando nos sentimos frágeis e imperfeitos, o poder de Deus se aperfeiçoa em nossa fraqueza. Ele nos restaura e nos renova continuamente.
"Munandiwumba ndi kundipanga ndi manja anu.
Kodi tsopano Inu mudzatembenuka ndi kundiwononga?
Kumbukirani kuti munandipanga ndi dothi,
kodi tsopano mundibwezeranso ku fumbi?
Monga mmene chiziro chimakutira chiwiya chadothi
ndi mmene mawu oshashalika amabisira mtima woyipa.
Khetsani misozi ndi kufuwula mwamphamvu, abusa inu;
gubudukani pa fumbi, inu atsogoleri a nkhosa.
Pakuti nthawi yanu yophedwa yafika;
mudzagwa ndi kuphwanyika ngati mbiya yabwino kwambiri.