Publicidade

Vida

Por Bíblia Online

A vida é um dom precioso de Deus. Desde a concepção até a eternidade, as Escrituras revelam o propósito, o valor e a plenitude da vida que o Senhor nos oferece.

Deus, o autor da vida

O Senhor é quem dá a vida e a sustenta. Cada ser humano foi formado por suas mãos com propósito e intenção divina.

Tsono Yehova Mulungu anawumba munthu kuchokera ku dothi nawuziramo mpweya wamoyo mʼmphuno mwake ndipo munthuyo anakhala wamoyo.

Pakuti Inu munalenga za mʼkati mwanga;

munandiwumba pamodzi mʼmimba mwa amayi anga.

Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa;

ntchito zanu ndi zodabwitsa,

zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe.

Mapangidwe anga sanabisike pamaso panu

pamene ndimapangidwa mʼmalo achinsinsi,

pamene ndinkawumbidwa mwaluso mʼmimba ya amayi anga.

Maso anu anaona thupi langa lisanawumbidwe.

Masiku onse amene anapatsidwa kwa ine, analembedwa mʼbuku lanu

asanayambe nʼkuwerengedwa komwe.

Pakuti kwa Inu kuli kasupe wamoyo;

mʼkuwala kwanu ifenso timaona kuwala.

Ine ndidzayimbira Yehova moyo wanga wonse;

ndidzayimbira matamando Mulungu wanga nthawi yonse imene ndili ndi moyo.

A vida em Cristo

Jesus é o caminho, a verdade e a vida. Nele encontramos sentido, plenitude e a promessa de vida abundante e eterna.

Yesu anayankha kuti, "Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate popanda kudzera mwa Ine.

Mbala sibwera chabe koma kuti idzabe, kupha ndi kuwononga. Ine ndabwera kuti iwo akhale ndi moyo, ndi kukhala nawo wochuluka.

Yesu anati kwa iye, "Ine ndine kuuka ndi moyo. Wokhulupirira Ine, angakhale amwalira adzakhala ndi moyo. Aliyense amene ali ndi moyo ndi kukhulupirira Ine sadzamwalira. Kodi iwe ukukhulupirira izi?"

Kenaka Yesu ananenetsa kuti, "Ine ndine chakudya chamoyo. Iye amene abwera kwa Ine sadzamva njala, ndipo iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu.

Malemba kuti ‘Aliyense amene akhulupirira Ine, mitsinje yamadzi amoyo idzatuluka kuchokera mʼkati mwake.’ "

Ndinapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano mʼthupi lino, ndi moyo mwachikhulupiriro mwa Mwana wa Mulungu, amene anandikonda nadzipereka yekha chifukwa cha ine.

Ndinapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano mʼthupi lino, ndi moyo mwachikhulupiriro mwa Mwana wa Mulungu, amene anandikonda nadzipereka yekha chifukwa cha ine.

Vivendo com sabedoria

A Bíblia nos orienta a viver com sabedoria, aproveitando bem o tempo, guardando o coração e buscando a vontade de Deus para cada dia.

Tiphunzitseni kuwerenga masiku athu molondola,

kuti tikhale ndi mtima wanzeru.

Mwana wanga, umvere ndi kuvomereza zimene ndikunena,

ndipo zaka za moyo wako zidzakhala zochuluka.

Ndipotu mtima wako uziwuyangʼanira bwino ndithu

pakuti ndiwo magwero a moyo.

Ndipotu mtima wako uziwuyangʼanira bwino ndithu

pakuti ndiwo magwero a moyo.

Iye amene amapeza nzeru ndiye kuti amakonda moyo wake.

Wosamalitsa kukhala wanzeru, zinthu zimamuyendera bwino.

Iye amene amagwira pakamwa pake amateteza moyo wake,

koma amene amayankhula zopanda pake adzawonongeka.

Wosamalira malangizo amayenda mʼnjira ya moyo,

koma wonyoza chidzudzulo amasochera.

Kuopa Yehova ndiye kasupe wamoyo,

kumathandiza munthu kuti apewe msampha wa imfa.

Amene amatsata chilungamo ndi kukhulupirika,

amapeza moyo ndi ulemerero.

Samalani makhalidwe anu, musakhale ngati opanda nzeru koma ngati anzeru. Gwiritsani ntchito mpata uliwonse, chifukwa masiku ano ndi oyipa.

A vida no dia a dia

Cada dia é uma oportunidade de glorificar a Deus. A Escritura nos chama a viver com propósito, confiança e fé prática.

Ndidziwitseni njira zanu Inu Yehova,

phunzitseni mayendedwe anu;

Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsata

masiku onse a moyo wanga,

ndipo ndidzakhala mʼNyumba ya Yehova

kwamuyaya.

Thupi ndi mtima wanga zitha kufowoka,

koma Mulungu ndiye mphamvu ya mtima wanga

ndi cholandira changa kwamuyaya.

Yehova adzakuteteza ku zoyipa zonse;

adzasunga moyo wako.

Yehova adzayangʼanira kutuluka kwako ndi kulowa kwako;

kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Popeza Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa,

chifukwa cha dzina lanu tsogolereni ndi kundiwongolera.

Chinthu chimodzi chokha chimene ndipempha kwa Yehova,

ichi ndi chimene ndidzachifunafuna:

kuti ndikhale mʼNyumba ya Yehova

masiku onse a moyo wanga,

ndi kuyangʼana kukongola kwa Yehova,

ndi kumufunafuna Iye mʼNyumba yake.

Khala chete pamaso pa Yehova ndipo umudikire mofatsa;

usavutike pamene anthu apambana mʼnjira zawo,

pamene iwo achita zinthu zawo zoyipa.

Ine sindidzayiwala konse malangizo anu,

pakuti ndi malangizo anuwo munasunga moyo wanga.

Prioridades e eternidade

Jesus nos lembra que a vida é mais que comida e o corpo mais que roupa. O que importa é buscar o Reino de Deus e viver para a eternidade.

"Nʼchifukwa chake ndikuwuzani kuti musadere nkhawa za moyo wanu kuti mudzadya chiyani kapena mudzamwa chiyani; kapenanso za thupi lanu kuti mudzavala chiyani. Kodi moyo suposa chakudya? Kodi thupi siliposa zovala? Onani mbalame zamlengalenga sizifesa kapena kukolola kapena kusunga mʼnkhokwe komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Kodi inu simuziposa kwambiri? Kodi ndani wa inu podandaula angathe kuwonjeza ora limodzi pa moyo wake?

Kodi munthu adzapindulanji akalandira dziko lonse lapansi, koma ndi kutaya moyo wake?

Kenaka anayitana gulu la anthu pamodzi ndi ophunzira ake nati: "Ngati wina aliyense afuna kunditsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kunyamula mtanda wake ndi kunditsata. Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine ndi cha Uthenga Wabwino, adzawupulumutsa. Kodi munthu adzapindulanji akalandira dziko lonse lapansi, koma ndi kutaya moyo wake? Kapena nʼchiyani chomwe munthu angapereke chosinthana ndi moyo wake? Ngati wina achita manyazi chifukwa cha Ine ndi mawu anga mu mʼbado uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wa Atate ake pamodzi ndi angelo oyera."

Kenaka Iye anawawuza kuti, "Chenjerani! Khalani tcheru ndi makhalidwe onse adyera; moyo wa munthu sukhala chifukwa cha kuchuluka kwa zimene ali nazo."

Tsono moyo wosathawo ndi uwu: Iwo akudziweni Inu, Mulungu yekhayo woona, ndi Yesu Khristu, amene Inu mwamutuma.

Pakuti malipiro a tchimo ndi imfa, koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Musafanizidwenso ndi makhalidwe a dziko lino koma musandulike pokonzanso maganizo anu. Ndipo mudzadziwa ndi kuzindikira chifuniro chabwino cha Mulungu chomwe ndi chokondweretsa ndi changwiro.

Ife timakhala mwachikhulupiriro, osati mwa zooneka ndi maso.

Yesetsani kukhala pa mtendere ndi anthu onse ndi kukhala oyera mtima, pakuti popanda chiyero palibe ndi mmodzi yemwe adzaona Ambuye.

Yesetsani kuti mukhale moyo wofatsa. Aliyense asamale ntchito yakeyake ndi kugwira ntchito ndi manja ake. Mukatero akunja adzalemekeza makhalidwe anu a tsiku ndi tsiku, ndi kuti inuyo mukhale osadalira wina aliyense.

Chilichonse mungachite, muchite ndi mtima wanu onse, monga mmene mungagwirire ntchito ya Ambuye osati ya anthu. Inu mukudziwa kuti mudzalandira mphotho monga cholowa kuchokera kwa Ambuye. Ndi Ambuye Khristu amene mukumutumikira.

Wodala ndi munthu amene amapirira mʼmayesero, chifukwa akapambana adzalandira chipewa cha ulemerero chimene Mulungu analonjeza anthu amene amamukonda.

Ndani mwa inu amene ndi wanzeru ndi womvetsa zinthu? Mulekeni aonetse ndi makhalidwe ake abwino kuti nzeru ndiye zikutsogolera kudzichepetsa kwake ndi zochita zake

Pakuti,

"Iye amene angakonde moyo

ndi kuona masiku abwino,

aletse lilime lake kuyankhula zoyipa,

ndiponso milomo yake kunena mabodza.

Apewe zoyipa, ndipo azichita zabwino.

Afunefune mtendere ndi kuyesetsa kuwupeza.

Chamoyo chilichonse chopuma chitamande Yehova.

Tamandani Yehova.

Chinthu chilichonse chili ndi nthawi yake,

ndi nyengo yake yomwe anayika Mulungu:

Pakuti lero ndikukulamulani kuti mukonde Yehova Mulungu wanu, kuti muyende mʼnjira zake, ndi kusunga malamulo ake, malangizo ake. Mukatero mudzakhala ndi moyo ndi kuchulukana, ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mʼdziko limene mukulowa kukakhalamo.

"Lemekeza abambo ako ndi amayi ako kuti ukhale ndi moyo wautali mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.

Kuchuluka kwa masiku athu ndi 70,

kapena 80 ngati tili ndi mphamvu;

komabe zaka zonsezi ndi za mavuto ndi nkhawa,

zimatha mofulumira ndipo ife timawulukira kutali.

"Yehova ndionetseni mathero a moyo wanga

ndi chiwerengero cha masiku anga;

mundidziwitse kuti moyo wanga ndi wosakhalitsa motani.

Inu mwachititsa kuti masiku anga akhale ochepa kwambiri,

kutalika kwa zaka zanga ndi kopanda phindu pamaso panu;

moyo wa munthu aliyense ndi waufupi.

Sela

Munthu ali ngati chithunzithunzi chake pamene akuyenda uku ndi uku:

Iye amangovutika koma popanda phindu;

amadzikundikira chuma, osadziwa kuti chidzakhala chayani.

Aliyense wa inu amene amakonda moyo wake

ndi kukhumba kuti aone masiku abwino ambiri,

asunge lilime lake ku zoyipa

ndi milomo yake kuti isayankhule zonama.

Tembenuka kuchoka ku zoyipa ndipo chita zabwino;

funafuna mtendere ndi kuwulondola.

Imvi zili ngati chipewa chaufumu chaulemerero;

munthu amazipeza akakhala moyo wolungama.

Monga momwe nkhope imaonekera mʼmadzi,

chomwechonso mtima wa munthu umadziwika ndi ntchito zake.

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-22_10-02-25-