Publicidade

Vitória

Por Bíblia Online

A vitória do cristão não depende de suas próprias forças, mas do poder de Deus que opera em nós. As Escrituras declaram que somos mais que vencedores por meio daquele que nos amou.

A vitória vem de Deus

O Senhor luta por nós. Quando confiamos nele, nenhuma arma forjada contra nós prosperará e nenhum inimigo prevalecerá.

pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye amene apite nanu kukakumenyerani nkhondo ndi kugonjetsa adani anu."

Yehova anati kwa Yoswa, "Usawaope, Ine ndawapereka mʼdzanja lako. Palibe ndi mmodzi mwa amenewa amene adzalimbe."

Kavalo amamukonzera tsiku la nkhondo,

koma ndi Yehova amene amapambanitsa.

Sanalande dziko ndi lupanga lawo,

si mkono wawo umene unawabweretsera chigonjetso,

koma ndi dzanja lanu lamanja, mkono wanu ndi kuwala kwa nkhope yanu,

pakuti munawakonda.

Inu ndinu Mfumu yanga ndi Mulungu wanga

amene mumalamulira chigonjetso cha Yakobo.

Mais que vencedores

Em todas as circunstâncias, a fé nos dá a vitória. O mundo tenta nos derrubar, mas Cristo já venceu o mundo e nos faz triunfar.

chifukwa aliyense amene ndi mwana wa Mulungu amagonjetsa dziko lapansi. Chikhulupiriro chathu ndicho timagonjetsera dziko lapansi.

Ayi, mu zonsezi ife ndife oposa agonjetsi mwa Iye amene anatikonda. Pakuti ine ndatsimikiza ndi mtima wonse kuti ngakhale imfa, kapena moyo, ngakhale angelo, kapena ziwanda, ngakhale zinthu zilipo, kapena zili mʼtsogolo, kapena mphamvu zina, ngakhale kutalika, kapena kuya, kapena chilichonse mʼchilengedwe chonse, sizingathe kutisiyanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Nanga tsono tidzanena chiyani pa izi? Ngati Mulungu ali mbali yathu, adzatitsutsa ife ndani?

"Iwe imfa, kupambana kwako kuli kuti?

Iwe imfa, ululu wako uli kuti?"

Ululu wa imfa ndi tchimo, ndipo mphamvu ya tchimo ndi lamulo. Koma tiyamike Mulungu amene amatipambanitsa mwa Ambuye athu Yesu Khristu.

Força para a batalha

Deus nos reveste com sua armadura espiritual, nos fortalece e nos encoraja. Mesmo que o justo caia sete vezes, ele se levanta.

Choncho valani zida zonse za Mulungu, kuti pamene tsiku loyipa kwambiri lifika, mudzathe kuyima chilili, ndipo mutatha kuchita zonse, mudzayimabe mwamphamvu.

paja munthu wolungama akagwa kasanu nʼkawiri amadzukiriranso.

Koma woyipa adzathedwa tsoka likadzawafikira.

Chifukwa cha Mulungu wathu, ife tidzapeza chipambano,

ndipo adzapondereza pansi adani athu.

Anthu 1,000 atha kufa pambali pako,

anthu 10,000 kudzanja lako lamanja,

koma zoopsazo sizidzafika pafupi ndi iwe.

Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu.

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-22_10-02-25-