27 Koma Mulungu anasankha zinthu zopusa za dziko lapansi kuti achititse manyazi anzeru. Mulungu anasankha zinthu zofowoka za dziko lapansi kuti achititse manyazi amphamvu. 28 Anasankha zinthu zapansipansi ndi zopeputsidwa za dziko la pansi lino, zinthu zimene kulibe, kuti asukulutse zimene zilipo, 29 kuti munthu asanyade pamaso pa Mulungu.
Publicidade
Publicidade