Publicidade

1 Coríntios 11

24 Atayamika ndi kumunyema ananena kuti, "Ili ndi thupi langa lomwe laperekedwa kwa inu; muzichita zimenezi pokumbukira Ine." 25 Chimodzimodzi, atatha kudya, anatenga chikho, nati, "Chikho ichi ndi pangano latsopano la magazi anga; imwani nthawi zonse pokumbukira Ine." 26 Pakuti nthawi zonse pamene mudya bulediyu ndikumwa chikhochi, mukulalikira imfa ya Ambuye mpaka Iye adzabweranso.

27 Chifukwa chake, aliyense amene adya buledi kapena kumwa chikho cha Ambuye mʼnjira yosayenera adzachimwira thupi ndi magazi a Ambuye. 28 Munthu adzisanthule yekha asanadye buledi kapena kumwa chikhochi.

Veja também

Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-07-05_19-25-13-