Pular para o conteúdo
Publicidade

1 AKORINTO 12

Thupi Limodzi Ziwalo Zambiri

12 Thupi ndi limodzi, ngakhale kuti lapangidwa ndi ziwalo zambiri. Ndipo ngakhale ziwalo zake zonse ndi zambiri, zimapanga thupi limodzi. Momwemonso ndi mmene alili Khristu. 13 Pakuti tonse tinabatizidwa ndi Mzimu mmodzi mʼthupi limodzi. Myuda kapena Mgriki, kapolo kapena mfulu tonse tinapatsidwa kuti timwe Mzimu mmodzi yemweyo. 14 Tsopano thupi silinapangidwe ndi chiwalo chimodzi koma ndi ziwalo zambiri.

15 Ngati phazi litanena kuti, "Pakuti sindine dzanja, sindine chiwalo cha thupi." Chifukwa chimenechi sichingachititse phazi kuti lisakhale chiwalo cha thupi. 16 Ndipo ngati khutu litanena kuti, "Pakuti sindine diso, sindine chiwalo cha thupi." Chifukwa chimenechi sichingachititse khutu kuti lisakhale chiwalo cha thupi. 17 Kodi thupi lonse likanakhala diso, tikanamamva bwanji? Nanga thupi lonse likanakhala khutu, tikanamanunkhiza bwanji? 18 Koma zoona nʼzakuti, Mulungu anayika ziwalo mʼthupi, chilichonse monga momwe Iye anafunira. 19 Nanga zonse zikanakhala chiwalo chimodzi, ndiye thupi likanakhala lotani? 20 Mmene zililimu, pali ziwalo zambiri koma thupi ndi limodzi lokha.

21 Diso silingawuze dzanja kuti, "Iwe sindikukufuna!" Ndipo mutu sungawuze phazi kuti "Iwe sindikukufuna!" 22 Mʼmalo mwake, ziwalo zathupi zimene zimaoneka ngati zofowoka ndizo zili zofunikira kwambiri, 23 ndipo ziwalo zathupi zimene timaziyesa zopanda ulemu, ndizo timazilemekeza kwambiri. Ndipo ziwalo zosaoneka bwino ndizo zimalandira ulemu wapadera. 24 Koma ziwalo zooneka bwino, nʼkosafunika kuti tizisamalire mwapadera. Mulungu polumikiza ziwalo zathupi, anapereka ulemu wopambana kwa ziwalo zimene zimafunadi ulemuwo 25 kuti pasakhale kugawikana mʼthupi koma kuti ziwalo zonse zisamalirane. 26 Ngati chiwalo chimodzi chikumva kuwawa, ziwalo zonse zimamvanso kuwawa. Ngati chiwalo chimodzi chilandira ulemu, ziwalo zonse zimakondwera nawo.

27 Tsopano inu ndinu thupi la Khristu, ndipo aliyense wa inu ndi chiwalo cha thupilo.

Veja também