Publicidade

1 Coríntios 13

4 Chikondi nʼcholeza mtima, chikondi nʼchokoma mtima, chilibe nsanje, sichidzikuza, sichidzitamandira. 5 Chikondi chilibe mwano, sichodzikonda, sichipsa mtima msanga, sichisunga mangawa. 6 Chikondi sichikondwera ndi zoyipa koma chimakondwera ndi choonadi. 7 Chimatchinjiriza nthawi zonse, chimakhulupirika nthawi zonse, chimakhala ndi chiyembekezo nthawi zonse, chimapirira nthawi zonse.

8 Chikondi ndi chosatha. Koma mphatso ya uneneri idzatha, pamene pali kuyankhula malilime adzatha, pamene pali chidziwitso chidzatha.

Veja também

Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-07-05_19-25-13-