Publicidade

1 Coríntios 15

45 Kwalembedwa kuti, "Munthu woyamba Adamu anakhala wamoyo," Adamu wotsiriza anakhala wopatsa moyo. 46 Zauzimu sizinabwere koyambirira, koma zachilengedwe, pambuyo pake zauzimu. 47 Munthu woyamba anali wa dziko lapansi, wochokera mʼnthaka koma munthu wachiwiri anali wochokera kumwamba. 48 Monga analili munthu wa dziko lapansi, momwemonso anthu onse amene ndi a dziko lapansi. Ndipo monga alili munthu wakumwamba, momwemonso anthu onse amene ndi akumwamba. 49 Ndipo monga momwe tinabadwa ofanana ndi munthu wa dziko lapansi uja, momwemonso tidzakhala ofanana ndi munthu wakumwamba.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-