Ndalama Zothandizira Akhristu a ku Yerusalemu
1 Tsopano za zopereka zothandiza anthu a Ambuye a ku Yerusalemu. Muchite zomwe ndinawuza mipingo ya ku Galatiya kuti ichite. 2 Pa tsiku loyamba la sabata lililonse, aliyense wa inu azipatula ndalama molingana ndi zomwe wapezera. Asunge, kuti ndikabwera pasadzakhalenso msonkhamsonkha. 3 Pamenepo, ndikadzafika, ndidzawapatsa makalata a umboni anthu amene mudzawasankhe ndi kuwatuma kuti akapereka mphatso zanu ku Yerusalemu.