Chigololo
12 Inu mumati, "Ine ndili ndi ufulu wochita chilichonse." Komatu si zonse zimene nʼzothandiza. "Ndili ndi ufulu wochita chilichonse." Koma sindidzagonjetsedwa ndi chilichonse. 13 Inu mumati, "Chakudya, kwake nʼkulowa mʼmimba ndipo mimba ntchito yake nʼkulandira chakudyacho." Koma Mulungu adzawononga zonsezi. Thupi silochitira chigololo, koma la Ambuye, ndipo Ambuye ndiye mwini thupilo.