Pular para o conteúdo
Publicidade

1 Coríntios 7

32 Ine ndikufuna kuti mumasuke ku nkhawa zanu. Munthu wosakwatira amangolabadira za Ambuye, mmene angakondweretsere Ambuyewo. 33 Koma wa pa banja amalabadira za dziko lapansi lino, mmene angakondweretsere mkazi wake, 34 ndipo chifukwa ichi amatanganidwa kwambiri. Mkazi wosakwatiwa kapena namwali, amalabadira za Ambuye. Cholinga chake ndi kudzipereka kwa Ambuye mʼthupi ndi mu uzimu momwe. Koma mkazi wokwatiwa amalabadira za dziko lapansi lino, mmene angakondweretsere mwamuna wake.

Veja também