9 Yabesi anali munthu wolemekezeka kwambiri kuposa abale ake. Amayi ake anamutcha Yabesi kutanthauza kuti, "Chifukwa ndinamubala ndi ululu wambiri." 10 Yabesi analira kwa Mulungu wa Israeli kuti, "Mundidalitse ndipo mukulitse dziko langa! Dzanja lanu likhale pa ine ndipo mundisunge kuti choyipa chisandigwere ndi kundisautsa." Ndipo Mulungu anamupatsa chopempha chakecho.